Nkhani Yabwino Yochoka Kwa Allah Ta’ala Kwa Awo Amene Amawerenga Durood (Amanfunira Zabwino Nabi (sallallahu alaih aasallam)) Kuchokera M’mahadith

عن عبد الرحمن بن عوف رضي الله عنه قال خرج رسول الله صلى الله عليه وسلم فاتبعته حتى دخل نخلا فسجد فأطال السجود حتى خفت أو خشيت أن يكون الله قد توفاه أو قبضه قال فجئت أنظر فرفع رأسه فقال ما لك يا عبد الرحمن قال فذكرت ذلك له فقال إن جبريل عليه السلام قال لي ألا أبشرك إن الله عز وجل يقول لك من صلى عليك صليت عليه ومن سلم عليك سلمت عليه (مسند أحمد، الرقم: ١٦٦٢، وقال البيهقي في الخلافيات ٣/١٤٣ عن طريق لهذه الرواية بنحو هذه الألفاظ :قال أبو عبد الله – رحمه الله -: هذا حديث صحيح)

Sayyiduna Abdul Rahman bin Aufi (radhwiyallahu anhu) akunena kuti, tsiku lina Nabi (sallallahu alaih alaihi wasallam) adachoka kunyumba kwake ndipo ndidamulondora, kufikira mpaka adalowa m’munda wa tende nagwetsa nkhope yake pansi. Nabi (sallallahu alaihi wasallam) adakhala pasajdah kwanthawi yaitali mpaka ndidaganiza ngati Allah wachotsa nzimu wake. Kenaka ndidapita pafupi kuti ndikaone chomwe chanchitikira Nabi (sallallahu alaihi wasallam). Kenaka Nabi (sallallahu alaihi wasallam) adanyamula mutu wake olemekezeka kuchoka pa sajdah ndikundifunsa kuti chachitika ndichani, kudzera pamenepo ndidaonetsa mantha komanso nkhawa zanga (zokhudza kumuganizira kuti wamwalira pa sajdah). Nabi (sallallahu alaihi wasallam) adayankha nati,” (chifukwa chomwe ndidapangira sajdah yaitali chotero ndichakuti) Jibril (m’ngelo) (alaihis salaam) anandibwelera ndikundifunsa kuti, kodi ndisakuuze nkhani yabwino yomwe Allah Ta’ala akunena kuti, Amene angakutumizire durood, ndimanfikitsira chifundo changa, ndipo amene amakutumizira salaam ndimampatsa ntendere ndikumudalitsa.'”

Mahri (Chiongo) A Nabi Aadam (alaihis salaam)

Shaikh Abdul Haqq Dehlawi (rahimahullah) adalemba m’bukhu lake lotchedwa” Madaarijun Nubuwwah” kuti, Hawwa (radhwiyallahu anha) atalengedwa, Aadam (alaihis salaam) adanyamula dzanja lake kuti amugwire. Angelo adati kwa iye, upeze ntima ndikudikira kuti nikah (ndowa) ichitike ndikumpatsa mahri.”

Aadam alaihis salaam adafunsa nati, ndipeleke chani ngati mahri? Angelo adayankha nati, kuwerenga Durood kumuwerengera Nabi (sallallahu alaihi wasallam),” mu hadith ina zimanenedwa kuti, mahri anali kuwerengedwa kwa Durood ka 20 (makumi awiri kumuwerengera Nabi (sallallahu alaih wasallam)). (Fazaail-e-Durood – Urdu pg.155)

Check Also

Ma Ulemelero Khumi Amakwezedwa

Sayyiduna Anas bin Maliki (radiyallah anhu) akusimba kuti, Nabi (salallah alayhi wasallam) adati; "Amene angandifunire ine zabwino kamodzi (popanga Durood), Allah Ta´ala adzamutumizira iyeyo madalitso khumi, machimo ake khumi adzakhululukidwa ndiponso levo yake ku Jannah idzakwezedwa ndi masiteji okwanira khumi".