Kukhululukidwa Machimo

عن أبي بردة بن نيار رضي الله عنه قال قال رسول الله صلي الله عليه وسلم من صلى علي من أمتي صلاة مخلصا من قلبه صلى الله عليه بها عشر صلوات ورفعه بها عشر درجات وكتب له بها عشر حسنات ومحا عنه عشر سيئات (السنن الكبرى للنسائى، الرقم: 9809، ورواته ثقات كما في فتح الباري 11/167)

Sayyiduna Abu Burdah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati,” amene anganditumizire Durood mwa ummah wanga kuchokera pansi pa mtima, Allah adzamdalitsa munthu ameneyo pompatsa zifundo zokwana khumi, adzamukwezera ulemelero wake ndi masiteji okwana khumi ku Jannah, adzamulipira sawabu zokwana khumi ndikumukhululukira machimo okwana khumi.”

Chikondi Cha Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) Kumukonda Nabi (sallallahu alaih wasallam)

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adawuyamba nsamuko pamodzi ndi Abu Bakr (radhwiyallahu) anhu chakumadzulo, nkatikati mwa ulendowu, nthawi zina Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) ankayenda kutsogolo kwa Nabi (sallallahu alaih wasallam), ndipo nthawi zina ankayenda kumbuyo kwake, nthawi zina kumanja kwake ndipo nthawi zina kumanzere kwake.

Nabi (sallallahu alaih wasallam) atazindikira machitidwe achilendowa anamfusa iye kuti, oh Abu bakr! Ndikumakuona ukuyenda pena kutsogolo kwanga ndipo pena kumbuyo kwanga, nthawi zina kumanja kwanga pena kumanzere kwanga, ndichani chikukupangitsa iwe kuchita zimenezi? Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) adayankha nati: nthawi zonse maganizo akandifika oti adani atha kukubwererani kumbuyo kwanu, ndikumathamangira kumbuyo kwanu, ndipo mantha akandifika kuti nkutheka adani akubisalirani kutsogolo kwanu ndikumathamangira kutsogolo kwanu, chimodzimodzinso maganizo akandifika oti adani atha kubwera kudzera kumanja kwanu kapena kumanzere, ndikumapita mbali imeneyo.”

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati, oh Abu bakr! Ukulolera kuika moyo wako pachiswe chifukwa chaine? ndipo Abu Bakr adayankha nati,inde, kwabasi oh Nabi (sallallahu alaih wasallam), ndikulumbilira iye amene adakutumizani kukhala Nabi ndi chipembedzo chenicheni cha Chisilamu!” (Mustadrak Lil Haakim #4268)

Check Also

Kulandira Zifundo Zokwana Khumi (10)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Nabi (sallallahu alaihi wasallam) adati, amene anganditumizire Durood kamodzi, Allah Ta’ala adzamulipira munthu ameneyo ndikumpatsa zifundo zokwana khumi.