Kupeza Chifundo Chochuluka Cha Allah Ta’ala

عن ابن عمر وأبي هريرة رضي الله عنهما قالا قال رسول الله صلى الله عليه وسلم صلوا علي صلى الله عليكم (الكامل لابن عدي، الرقم: ١١٠٨٦، وإسناده ضعيف كما في التيسير للمناوي ٢/٩٣)

Sayyiduna Abdullah bin Umar komanso Abu Hurairah (radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati, ndifunireni zabwino (pondiwerengera Durood) Allah Ta’ala adzakuchitirani chifundo.

Sayyiduna Abu Bakr (Radhwiyallahu Anhu) Kuphanga Lotchedwa Thaur

Adakali muphanga muja paulendo wa Hijra (kupita ku Madina) zanenedwa kuti Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) nkhawa zake zonse zinali zoti pasapezeke chilichonse chotuluka mudzenje chomwe chingapeleke vuto kwa Nabi (sallallahu alaih wasallam), kotero adayamba kutseka mayenje onse omwe anali mphangamo ndi zigamba zachovala chake chakumusi, komano padatsalira mayenje awiri omwe sadatsekedwe chifukwa chosowekera zotsekera, ndipo Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) adatseka mayenjewo ndimapazi ake, kenaka Nabi (sallallahu alaih wasallam) adaika mutu wake odalitsika pantchafu za Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) mpaka anagona tulo.

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adakali ntulo chomwecho, Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) adanva kulumidwa phazi lake ndinjoka yomwe idali kudzenje kuja, posafuna kumusokoneza Nabi (sallallahu alaih wasallam) mpang’ono pomwe, Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) adapilira ku ululu omwe ankauva ndipo sadasunthe mpang’ono pomwe, komano chifukwa cha kunva kwambiri ululu ndikukanika kupilira, misozi idayamba kuyendelera pamasaya ake ndipo idagwera pankhope yodalitsika ya Nabi (sallallahu alaih wasallam).

Nabi (sallallahu alaih wasallam) mwadzidzidzi adadzuka ndikufunsa Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) kuti chachitika ndichani Sayyiduna Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu anhu) adayankha nati, “ndalumidwa ndinjoka, makolo anga apelekedwe nsembe chifukwa chainu oh Nabi (sallallahu alaih wasallam),” Nabi (sallallahu alaih wasallam) adapaka malovu ake pamalo olumidwawo ndipo nthawi yomweyo ululu udatha. (Mishkatul Masabeeh #6034)

Check Also

Kupeza Mwayi Okhala Pafupi Ndi Nabi (Salallah Alayhi Wasallam) Patsiku Lachiweruzo

Sayyiduna Abu umaamah (radhwiyallahu anhu) akusimbanso kuti: Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati: “Chulukitsani kunditumizira Durood ine lachisanu lililonse, Ndithudi Durood imene ummah wanga umachita imabweretsedwa kwa ine lachisanu lililonse. (Choncho) amene amachulukitsa kunditumizira Durood ineyo ndi amene adzakhale kufupi kwambiri ndi ine (patsiku lachiweruzo).