Ma Ubwino A Wudhu

1. Wudhu ndi chiyeretso chamachimo ang’ono ang’ono.

عن عثمان بن عفان رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من توضأ فأحسن الوضوء خرجت خطاياه من جسده حتى تخرج من تحت أظفاره (صحيح مسلم، الرقم: ٢٤٥)

Sayyiduna Uthmaan (radhwiyallahu anhu) akuti; Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: Amene angachite-wudhu, ndipo nawuchita wudhuwo mkachitidwe kabwino kwambiri, Machimo ake (ang´onoang´ono) amafudutidwa (ndipo amatsukidwa) kuchokera mthupi mwake mpakana amagwa machimo kudzera pansi pa-zikhadabo.

2. Wudhu udzapangitsa ziwalo zochitira  wudhu kuti ziwale ndi (noor) kuwala kwapadera patsikula chiweluzo.

عن أبي هريرة رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم أتى المقبرة فقال السلام عليكم دار قوم مؤمنين وإنا إن شاء الله بكم لاحقون وددت أنا قد رأينا إخواننا قالوا أولسنا إخوانك يا رسول الله قال أنتم أصحابي وإخواننا الذين لم يأتوا بعد قالوا كيف تعرف من لم يأت بعد من أمتك يا رسول الله قال أرأيت لو أن رجلا له خيل غر محجلة بين ظهري خيل دهم بهم ألا يعرف خيله قالوا بلى يا رسول الله قال فإنهم يأتون غرا محجلين من الوضوء وأنا فرطهم على الحوض (صحيح مسلم، الرقم: ٢٤٩)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) tsiku lina adalowa pamanda ena ake ndipo adawelenga Duwa iyi:

السلام عليكم دار قوم مؤمنين وإنا إن شاء الله بكم لاحقون

Mtendere ukhale kwa inu anthu okhulupiIira amene mwagonekedwa m’manda. Ndipo ife mulungu akafuna tikumana nanu pompano.

Kenaka Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “ndikukhumba tikadakumana ndabale athu.” Masahabah (Radhwiyallahu anhum) adafunsa, kodi ifeyo sabale anu oh Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)? Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati, ndiinu ophunzila anga (i.e.ndiinu apamwamba kwambiri kuposa ummah onse, ndiinu abale anga ndiponso mwadalitsika pokhala onditsatira) abale ndi awo omwe sadabwere padziko pano.(i.e.sanabadwe adzabwera ine ndikadzamwalira) masahabah adafunsaso, oh Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), mudzawazindikira bwanji okutsatirani anu omwe adzabwere inu kulibe? Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anayankha nati” ngati munthu ali ndi akavalo (hachi) akuda oyera pachipumi ndim’miyendo ndipo asakanikirana ndakavalo ena omwe ndi akuda mopanda ntundu winanso, kodi mwini wake zingamuvute kwazindikira akavalo ake? masahabah (radhwiyallahu anhum) anayankha nati, ndithudi adzawazindikira. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anayankha nati,” adzabwera patsiku la Qiyamah zipumi ndi ziwalo zawo zina zili zowala ndi noor yapadera chifukwa cha wudhu omwe ankachita akafuna kuswali (chizindikiro chimenechi ndichomwe chidzandizindikiritse iwowo) ndipo ndidzawapatsa madzi kuti amwe patsinje wa Kauthar (akadzakumana nane patsiku lomaliza).”

3. Kukhala ndi wudhu nthawi zonse ndi chizindikiro cha Imaan (chikhulupililo choonadi).

عن ثوبان رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم استقيموا ولن تحصوا واعلموا أن خير أعمالكم الصلاة ولا يحافظ على الوضوء إلا مؤمن (سنن ابن ماجة، الرقم: ٢٧٧)[1]

Sayyiduna Thaubaan (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, yesetsani kukhala okhanzikika pachina chilichonse ngakhale mutakhala kuti simungakwaniritse chilichonse, ndipo zindikirani kuti ibadah imene ili ndi malipiro ambiri ndi swalah ndipo kusamalitsa wudhu ndichizindikiro chansilamu weniweni (i.e. kupanga wudhu moyenera ndimosamalitsa ndi kukhala ndi wudhu nthawi zonse ndi chizindikiro choti ndiiwe nsilamu weniweni).’’

4. Munthu amene angamwalire alindi wudhu amadalitsika ndi imfa ya shahidi (yemwe wafera kunkhondo ya Allah).

عن أنس بن مالك رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم يا بني إن استطعت أن لا تزال على وضوء فإنه من يأتيه الموت وهو على وضوء يعطى الشهادة (مجمع الزوائد، الرقم: ١٤٧٠)[2]

Sayyiduna Anas bin Malik (radhwiyallahu anhu) akunena kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, oh mwana wanga okondedwa, ngati ungakwanitse kukhala ndi wudhu nthawi zonse (tatero) chifukwa choti munthu yemwe angamwalire ali ndi wudhu amaikidwa m’gulu la shahidi (ofera kunkhondo).”

5. Munthu amene amapanga wudhu onse amadziteteza kwa shaitani mongai m’mene asilikali achisilamu omwe akulondera malire adziko lachisilamu pofuna kuteteza asilamu kwadani achisilamu.

عن أبي هريرة رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال ألا أدلكم على ما يمحو الله به الخطايا ويرفع به الدرجات قالوا بلى يا رسول الله قال إسباغ الوضوء على المكاره وكثرة الخطا إلى المساجد وانتظار الصلاة بعد الصلاة فذلكم الرباط (صحيح مسلم، الرقم: ٢٥١)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) tsiku linalake adawafunsa ophunzira ake (radhwiyallahu anhum) kuti ‘’kodi ndisakuuzeni za ntchito (yabwino) imene mukaichita Allah ta’ala adzafufuta machimo anu ndikukupatsani ulemelero wa pamwamba?’’ masahabah (radhwiyallahu anhum) anayankha kuti,’’ chonde tiuzeni oh Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), Mtumiki (sallallahu alaih I wasallam) adati, kupanga wudhu onse mokwanira bwino munthawi zopweteka, kuyenda popita kunzikiti kukapemphera ndikudikira swalah yotsatira pamene mwamaliza kuswali ntchito zimafanana ndi awo amene akulondera malire achisilamu kwa adani (kudzera mukuchita zimenezi munthuyo amakhala akudziteteza kuzoipa zachilakolako chamtima wake komanso shaitani, ngati m’mene anthu olondera malire achisilamu amakhala kuti akuteteza asilamu ku adani achisilamu).”


[1] قال البوصيري في الزوائد (1/102): رجال إسناده ثقات أثبات إلا أن فيه انقطاعا بين سالم وثوبان ولكن أخرجه الدارمي وابن حبان في صحيحه من طريق ثوبان متصلا

[2] قال الهيثمي: رواه أبو يعلى والطبراني في الصغير وزاد يا بني إذا خرجت من بيتك فلا يقعن بصرك على أحد من أهل القبلة إلا ظننت أنه له الفضل عليك يا بني إن ذلك من سنتي ومن أحيا سنتي فقد أحبني ومن أحبني كان معي في الجنة وفيه محمد بن الحسن بن أبي يزيد وهو ضعيف

قال البوصيري في الإتحاف (الرقم: 540): علي بن زيد بن جدعان ضعيف لكن لم ينفرد به علي بن زيد فقد رواه أحمد بن منيع ثنا يؤيد أبنا العلاء أبو محمد الثقفي سمعت أنس بن مالك … فذكره وسيأتي لفظه في آخر كتاب المواعظ إن شاء الله روى الترمذي قطعة منه في الصلاة وأخرى في العلم من طريق علي بن زيد