Kupeza Mwayi Okhala Pafupi Ndi Nabi (Salallah Alayhi Wasallam) Patsiku Lachiweruzo

عن عبد الله بن مسعود أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال: أولى الناس بي يوم القيامة أكثرهم علي صلاة (سنن الترمذي، الرقم: ٤٨٤، وحسنه الإمام الترمذي رحمه الله)

Sayyiduna Abdullah bin Mas´ud (radiyallah anhuma) akusimba kuti: Nabi (sallallahu alaih wasallama) adati: ´Munthu amene adzakhale moyandikana kwambiri ndi ine (komanso oyenera kulandila chiombolo changa) patsiku lachiweruzo adzakhala amene amachulukitsa kunditumizira Durood padziko pano”

Sayyiduna Abdullah Bin Amr (radhwiyallah Anhuma) Awotcha Chovala Chake

Sayyiduna Abdullah bin Amr bin Aasi (radhwiyallahu anhuma) akunena kuti:

`Tsiku lina, Tidali limodzi ndi Nabi (salallah alaih wasallama) paulendo. Ndinapita kukamuona Iye nditavala chovala cha mtundu wachikasu/Oranje. (Ndi haraam kwa mwamuna kuvala chovala chamtundu wa yelo komanso oranje). Nabi (sallallahu alaih wasallam) adandifunsa,´Ichi nchiyani wavalachi? ´Ndipo ndidazindikira kuti sadasangalatsidwe nako kuvala kwanga zovala zamtundu umenewo. Choncho, pamene ndidafika kunyumba ndidapeza moto ukuyaka ndipo ndinaponya chovala changacho pamoto.

Tsiku lotsatila, pameme ndidapita kwa Rasulullah (sallallahu alaih wasallama) adandifunsa ´chili kuti chovala chija? ´pamene ndinamuuza zimene ndinachita nacho chovalacho, adati ´´Udayenera kumupatsa m’modzi mwa amayi akunyumba kwako, chifukwa azimayi amaloredwa kuvala zovala zamtundu umene uja´´.

Sayyiduna Abdullah bin Amr bin Aasi (radhwiyallahu anhuma) adavutika m’maganizo kwambiri poona kuti Sayyiduna Rasulullah (salallah alaih wasallama) adali okhumudwa, Choncho iye sadachedwe kupeza njira yothanirana ndi chovala chimene chidapangitsa kuti Nabi (salallah alaih wasallama) akhumudwe.Komanso sadaganizire kupeza njira ina yogwiritsira ntchito chovalacho. Tikadakhala ngati ifeyo m’malo mwa iyeyo bwenzi titakhala ndimaganizo owilingula kapena tikadangochisunga chovalacho kapena apo tikadapeza njira ina yogwiritsira ntchito. (Sunan Abi Dawood #4066)

Check Also

Kupeza Mwayi Okhala Pafupi Ndi Nabi (Salallah Alayhi Wasallam) Patsiku Lachiweruzo

Sayyiduna Abu umaamah (radhwiyallahu anhu) akusimbanso kuti: Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati: “Chulukitsani kunditumizira Durood ine lachisanu lililonse, Ndithudi Durood imene ummah wanga umachita imabweretsedwa kwa ine lachisanu lililonse. (Choncho) amene amachulukitsa kunditumizira Durood ineyo ndi amene adzakhale kufupi kwambiri ndi ine (patsiku lachiweruzo).