Kuikonzekera Ramadhan

1. Ikonzekereni bwino Ramadhan isanayambe, anthu m’mbuyomo ankaukonzekera mwezi umenewu patatsala miyezi isanu ndi umodzi.

2. Mwezi wa Rajab ukayamba mudzwelenga duwa iyi:

اَللّٰهُمَّ بَارِكْ لَنَا فِيْ رَجَبٍ وَّشَعْبَان وَبَلِّغْنَا رَمَضَان

Oh Allah tidalitseni m’mwezi umenewu wa Rajab ndi Sha’baan, ndipo tiloreni kuti tifike mwezi wa Ramadhan.

عن أنسٍ رضي الله عنه قال كَانَ النَّبِيُّ صَلَّى اللهُ عَلَيهِ وَسَلَّمَ إذَا دَخَلَ رَجَبٌ قَالَ: اَللّهُمَّ بَارِكْ لَنَا فِيْ رَجَبٍ وَّشَعْبَانَ وَبَلِّغْنَا رَمَضَان (شعب الايمان، الرقم: ٣٨١٥)

Sayyiduna Anas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, mwezi wa Ramadhan ukayamba, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankapanga duwa iyi, “Oh Allah, tidalitseni m’mwezi umenewu wa Rajab komanso wa Sha’baan, tiloreni kuti tiufike mwezi wa Ramadhan.”

3. Konzani m’ndandanda wa nthawi ndikukhanzikitsa nthawi imene mudzipanga ibadah (mapemphero) monga kuwerenga Qur’aan ndizina zotero. Kudzera mukukhanzikitsa nthawizi, zidzakuthandizani kuti mugwiritse ntchito bwino nthawi yanu m’mwezi umenewu wa Ramadhan.

عن أبي سعيد الخدري رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه و سلم قال من صام رمضان وعرف حدوده وتحفظ مما ينبغي له أن يتحفظ كفر ما قبله (صحيح ابن حبان، الرقم: 3433)

Sayyiduna Abu Saeedil khudriyy (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anati “amene angasale kudya mmwezi wa Ramadhan, navomeleza ndikulemekeza malire ake ndikukwaniritsa malamulo onse a kusala kudya monga m’mene akuyenelekera kuchitira, machimo onse omwe adachimwa adzakhululukidwa.”

4. Ngati wina ali ndi ngongole kwa Allah (monga; swalah zofunikira kubweza, namazani kapena Zakati) kapena anapondereza wina wake, adakhumudwitsa munthu wina wake kapena ali ndi ngongole ndi munthu wina wake yoti abweze, akufunika kudzikonza pobwezeretsa nchimake ndikubweza ngongole zonse, akapanga zimenezi ndiye kuti adzapeza madalitso ochuluka a m’mwezi umenewu wa Ramadhan.

5. Yesetsani kuchulukitsa ibadah pang’ono pang’ono mwezi wa Ramadhan usadafike, ndikukhala ndi chizolowezi chokwaniritsa ibadah yanu m’nthawi imene mudaikonza ndicholinga choti kupanga ibadah m’mwezi wa Ramadhan zidzakhale zopepuka.

6.Chulukitsani kupanga istighfaar (kupempha chikhululuko) komanso kupanga ma dua Ramadan isadafike.

7.Yesetsani kumalizitsa ntchito zofunikira zonse kupanga mwezi wa Ramadhan usadafike ndi cholinga chokuti ukafika mweziwu nthawi yanu yonse idzakhala yopanga ma ibadah.

عن عبادة بن الصامت رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه و سلم قال يوما وحضر رمضان أتاكم رمضان شهر بركة يغشاكم الله فيه فينزل الرحمة ويحط الخطايا ويستجيب فيه الدعاء ينظر الله تعالى إلى تنافسكم فيه ويباهي بكم ملائكته فأروا الله من أنفسكم خيرا فإن الشقي من حرم فيه رحمة الله عز وجل (مسند الشاميين، الرقم: 2238)

Sayyiduna Ubaadah bin Saamit (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti nthawi ina yake Ramadhan itatsala pang’ono Rasulullah (sallallahu alaihi wa sallam) adapereka ulaliki kwa ma swahaaba polankhula kuti “Ramadhan yatsala pang’ono kuti ikufikeni. Ramadhan ndi mwezi wa madalitso. Mu mwezi umenewu Allaah ta’ aala amabweretsa chifundo chapaderadera kwa inu, amakhululuka nsambi zanu komanso amayankha zopempha zanu zonse. Amayang’ana kupikisana kwanu mu zintchito zabwino mu mwezi wa Ramadhan ndipo amakutchulani mokunyadilani pamaso pa angelo ake. Choncho m Onetsani kwa Allaah zabwino zanu, izi zili choncho chifukwa munthu watsoka ndi uja amene wamanidwa chifundo cha Allaah mu mwezi olemekezeka umenewu.

Check Also

Kapangidwe Ka Istinja (Kutawasa) Ka Sunnah ~ Gawo La chisanu Nchiwiri

21. Mukamaliza kudzithandizako, dikirani madontho otsalira kunkodzo wanu kuti amalizike musanapange wuzu.