Kuyankhidwa Kwa Ma Duwa

عن عمر بن الخطاب رضي الله عنه قال : إن الدعاء موقوف بين السماء والأرض لا يصعد منه شيء حتى تصلى على نبيك صلى الله عليه و سلم (سنن الترمذي، الرقم، ٤٨٦)

Umar (radhwiyallahu anhu) akulongosora kuti: Duwa imakhala idakali pakati pa mitambo ndi nthaka (munlengalenga). Siimapititsidwa mpakana kumwamba ngati muduwamo simunawerengedwe Durood (kutanthauza kuti sipamakhala chitsimikizo cha kuyankhidwa kwa duwayo).

Chisangalaro Cha Umar (Radhwiyallahu Anhu)

Umar (radhwiyallahu anhu) nthawi ina adamuuza Abbaas (radhwiyallahu anhu) (amalume ake a Rasulullah (sallallahu alaih wasallam)) kuti ine ndinali osangalatsidwa ndi kulowa Chisilamu kwa bambo anga, koma kulowa chisilamu kwa inu kunabweretsa chisilamu kwa Rasulullaahi. (Sharhu Maanil Aathaar, 3/321)

Check Also

Kupeza Mwayi Okhala Pafupi Ndi Nabi (Salallah Alayhi Wasallam) Patsiku Lachiweruzo

Sayyiduna Abdullah bin Mas´ud (radiyallah anhuma) akusimba kuti: Nabi (sallallahu alaih wasallama) adati: ´Munthu amene adzakhale moyandikana kwambiri ndi ine (komanso oyenera kulandila chiombolo changa) patsiku lachiweruzo adzakhala amene amachulukitsa kunditumizira Durood padziko pano”