Kuikonzekera Ramadhan

15. Pamene muli m’mwezi wa Ramadhan yesetsani kupanga ntchito zabwino. Hadith ina ikuti, ntchito ina iliyonse yabwino yomwe ungachite mwakufuna kwako (nafil ibaadah) m’mwezi wa Ramadhan (umalipidwa ndi Allah) ngati wachita chinthu cha faradh (chokakamizidwa kuchita) ndipo ngati wachita ntchito ya farad (yokakamizika kuchita) mumwezi wa Ramadan imaonjezeredwa malipiro ake mowirikiza makumi asanu ndi awiri (70).

عن سلمان رضي الله عنه قال خطبنا رسول الله صلى الله عليه و سلم في آخر يوم من شعبان … من تقرب فيه بخصلة من الخير كان كمن أدى فريضة فيما سواه ومن أدى فريضة فيه كان كمن أدى سبعين فريضة فيما سواه (الترغيب والترهيب، الرقم: 1483)

Sayyiduna Salman (radiyallah anhu) akunena kuti, Mtumiki (salallah alayhi wasallama) adapereka ulaliki tsiku lotsirizira lamwezi wa shaabani (Muulalikiwo adayankhula mau awa) Amene angaziyandikitse kwa Allah pochita ntchito ya Sunnah (yosakakamizidwa) adzalandila malipiro ofanana ndimalipiro amunthu amene wagwira ntchito ya faradh (yokakamizidwa) m’miyezi ina (osakhala mwezi wa Ramadan). Ndipo amene angachite ntchito ya farad (yokakamizidwa) mkati kati mwa mwezi wa Ramadhan adzadalitsidwa popatsidwa malipiro ofanana ndi munthu amene anagwira ntchitoyo m’miyezi ina kokwanira makumi asanu ndi awiri.

16. Onetsetsani kuti mukupemphera Tarawehi marakat makumi awiri (20) usiku uliwonse. Kupemphera Tarawehi ndi Sunnah yofunikira kwambiri yosayenera kuisiya. Kuyambira nthawi ya olemekezeka Umar radiyallah anhu komanso masahabah onse (Allah asangalale nawo) adagwirizanakuti Tarawehi azipemphera marakat makumi awiri (20) Yesetsani kumaliza Quran kamodzi popemphera Tarawehi.

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال : قال رسول الله صلى الله عليه وسلم : من قام رمضان إيمانا واحتسابا غفر له ما تقدم من ذنبه (سنن أبي داود، الرقم: 1373)

Olemekezeka Abu Hurayrah (radiyallah anhu) akunena kuti; Mtumiki (salallah alayhi wasallama) adati: Munthu amene angayimilire kupemphera swalah ya Tarawehi m’mwezi wa Ramadhan ali ndi Imaan (ali ndichikhulupiliro chokwanira) komanso ali ndi chiyembekezo chofuna malipiro kwa Allah, Machimo ake onse (ang´onoang´ono) adzakhululukidwa.

عن عبد الرحمن بن عوف رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم إن الله تبارك و تعالى فرض صيام رمضان عليكم و سننت لكم قيامه فمن صامه و قامه إيمانا و احتسابا خرج من ذنوبه كيوم ولدته أمه (سنن النسائي 1/308)

Sayyiduna Abdul Rahmaan bin Auf (radiyallah anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adati: Ndithudi Allah Ta´laa wakulamulirani mokakamiza kumanga Ramadhan ndipo ine ndakulamulirani (ngati Sunnah) kuima usiku kupemphera Tarawehi. Choncho amene angasale swaumu masana kenaka naimilira usiku kupemphera swalah ya Tarawehi, ali ndichikhulupiliro mu mtima mwake komanso ali ofunafuna malipiro kwa Mulungu, Munthu ameneyo adzakhululukidwa machimo ake onse nakhala opanda tchimo ngati tsiku lomwe anamubereka amayi ake.

عن أبى الحسناء أن علي بن أبي طالب أمر رجلا أن يصلي بالناس خمس ترويحات عشرين ركعة – باب ما روي في عدد ركعات القيام في شهر رمضان (السنن الكبرى للبيهقي، الرقم: 4805)

Abul Hasnaa (rahimahullah) adati; Olemekezeka Ali (radhwiyallahu anhu) anamusankha munthu wina kuti azipempheretsa anthu Tarawehi m’mwezi wa Ramadhan.

عن الأعمش عن زيد بن وهب قال كان عبد الله بن مسعود يصلي لنا في شهر رمضان فينصرف عليه ليل قال الأعمش كان يصلي عشرين ركعة و يوتر بثلاث (عمدة القاري 11/127)

A’amash (rahimahullah) akuti: Ukafika mwezi olemekezeka wa Ramadhan Abdullah bin Mas’ud (radhwiyallahu anhu) amawapempheretsa anthu swalah ya Tarawehi. Iye amawapempheretsa anthu Tarawehi marakat makumi awiri (20) ndi maraka atatu (3) a witri.

روى البيهقي بإسناد صحيح انهم كانوا يقيمون على عهد عمر بعشرين ركعة وعلي عهد عثمان وعلي (وهكذا هو في عمدة القاري) (فتح الملهم 2/320)

Allaama Ayni rahmahullah, “Olemekezeka Masahabah a Mtumiki (salallah alayhi wasallama) adali kupemphera Tarawehi marakat makumi awiri (20) Kuyambira mu ulamuliro wa Umar (radhwiyallahu anhu) komanso mu nthawi ya Ulamuliro wa Uthman ndi Ali (Radiyallah anhuma)

17. Chulukitsani kuchita ntchito zinayi m’mwezi wa Ramadhan.
• Kuwerenga kalimah (mawu awa) Laa ilaaha illallahu.
• istighfaar (kupempha chikhululuko kwa Allah).
• Kupempha kuti Ukalowe ku Jannah.
• Kupempha chitetezo kuti ukapulumutsidwe kumoto (Jahannam)

عن سلمان رضي الله عنه قال خطبنا رسول الله صلى الله عليه و سلم في آخر يوم من شعبان… واستكثروا فيه من أربع خصال خصلتين ترضون بهما ربكم خصلتين لا غناء بكم عنهما فأما الخصلتان اللتان ترضون بهما ربكم فشهادة أن لا إله إلا الله وتستغفرونه وأما الخصلتان اللتان لا غناء بكم عنهما فتسألون الله الجنة وتعوذون به من النار (الترغيب والترهيب، الرقم: 1483)

Sayyiduna Salman (radhwiyallahu anhu) akunena kuti, Mtumiki (Sallallahu alayhi wasallam) adapereka ulaliki tsiku losilizira lamwezi wa Shaabani (muulalikimo adayankhula mau awa:) Chulukitsani kuchita ntchito zinayi, Ntchito ziwiri ndizosangalatsa Mbuye wanu Allah ndipo ntchito ziwiri … Ntchito ziwiri zomwe zingamusangalatse Mbuye wanu Allah ndi kuchulukisa kunena mau oti Laa ilaaha illallahu komanso kupempha chikhululuko kwa Allah. Ndipo ntchito ziwiri

18. Chulukitsani kupanga maduwa m’mwezi wa Ramadhan. Duwa ya munthu omanga Ramadhan imayankhidwa (nthawi zonse) makamaka duwa imene mungapange nthawi yofutulu.

عن أبي هريرة قال : قال رسول الله صلى الله عليه و سلم ثلاثة لا ترد دعوتهم الصائم حتى يفطر والإمام العادل ودعوة المظلوم يرفعها الله فوق الغمام ويفتح لها أبواب السماء ويقول الرب وعزتي لأنصرنك ولو بعد حين (سنن الترمذي، الرقم: 3598)

Olemekezeka Abu Hurayrah (radiyallah anhu) adanena kuti, Mtumiki (salallah alayhi wasallama) adati: Pali anthu atatu amene maduwa awo samakanidwa kwa Allah, Munthu omanga swawumu mpaka pamene akufutula, Mfumu yachilungamo ndipo ina ndi duwa ya munthu oponderezedwa, Allah amaitenga duwa ndikukafika duwayo pamwamba ku mitambo yonse ndipo imatseguliridwa zitseko zonse za kumwamba. Ndipo Allah amanena kuti “Ndikulumbilira Ulemelero wanga! ine ndikuthandiza (ndikuyankha duwa yako) ngakhale patadutsa ka nthawi.

عن عمرو بن شعيب، عن أبيه، عن جده، قال: سمعت رسول الله صلى الله عليه وسلم يقول: للصائم عند إفطاره دعوة مستجابة “. وكان عبد الله بن عمرو إذا أفطر دعا أهله وولده ودعا (شعب الايمان، الرقم: 3624)

Olemekezeka Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alayhi wasallama) adati; Pa nthawi yofutulu, Duwa ya munthu omanga imalandilidwa ndi Allah Talaa Choncho Olemekezeka Abdullah bin Amr (radhwiyallahu anhu) ankasonkhanitsa akazi ake ndi ana ake pa nthawi yofutulu ndikumapanga duwa.

19. Mwezi wa Ramadan umadziwikanso kuti ndi mwezi wa Qur’aan, Choncho wina akhoza kuwerenga Quran moiwirikiza ngati angakwanitse kutero.
Amene adaloweza Quran akuyenera kuiwerenga mowirikiza kwambiri kuposera amene sadailoweze.

20. Khalani ochulukitsa kupereka sadaqa m’mwezi waramadan. Mtumiki (salallah alayhi wasallama) ankachulukitsa kupereka sadaqah mumwezi wa Ramadan kuposera miyezi ina yonse yapachaka.

عن ابن عباس رضي الله عنهما قال كان رسول الله صلى الله عليه وسلم أجود الناس وكان أجود ما يكون في رمضان حين يلقاه جبريل وكان يلقاه في كل ليلة من رمضان فيدارسه القرآن فلرسول الله صلى الله عليه وسلم أجود بالخير من الريح المرسلة (صحيح البخاري، الرقم: 6)

Sayyiduna Ibn Abbas (radhwiyallahu anhuma) akunena kuti, Mtumiki (salallah alayhi wasallama) anali opereka sadaqah kwambiri mwa wathu. Ndipo ukafika mwezi wa Ramadan amachulukitsa kupereka kwambiri. M’ngero Jibril alayhi salaam ankabwera kudzakumana ndi Mtumiki (salallah alayhi wasallama) (kudzamubwerezera kuwerenga Quran). M’ngero Jibril (alayhi salaam) ankakumana ndi Mtumiki (salallah alayhi wasallama) mu usiku wa Ramadan uliwonse ndipo ankawerengerana Qur’aan wina ndi m’nzake. Ndipo Mtumiki (salallah alayhi wasallam) ndipo Mtumiki (salallah alayhi wasallama) adali ofulumira kwambiri kupereka sadaqah kuposera mphepo yabwino imene imaomba. (Mphepo imadziwika kuti ilibe malire ndipo imatha kufikira malo aliwonsewo, choncho kupereka sadaqah kwa Mtumiki kumaponsera mphepo kamba koonetsa chikondi ndi chifundo kuzolengedwa).

Check Also

Kapangidwe Ka Istinja (Kutawasa) Ka Sunnah ~ Gawo La chisanu Nchimodzi

19. Gwiritsani ntchito dzanja lamanzere potawasa, kutawasira dzanja lamanja ndi makuruhu (zonyasa). Chimodzimodzinso, musagwire maliseche ndidzanja lamanja.