Kukwaniritsidwa Zofuna Za Umoyo Uno Ndi Umoyo Otsiriza

عن محمد بن يحيى بن حبان عن أبيه عن جده حبان بن منقذ أن رجلا قال: يا رسول الله أجعل ثلث صلاتي عليك قال: نعم إن شئت قال: الثلثين قال: نعم قال: فصلاتي كلها قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: إذن يكفيك الله ما أهمك من أمر دنياك وآخرتك (المعجم الكبير للطبراني، الرقم: ٣٥٧٤، وإسناده حسن كما في الترغيب والترهيب للمنذري، الرقم: ٢٥٧٨)

Olemekezeka Habbaan bin Munqiz (Rahimahullah) akusimba kuti Sahaba wina adamufunsa Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) nati “O inu Mtumiki Wa Allah Kodi ndingapereke gawo limodzi m’magawo atatu (one third) a nthawi yanga imene ndiri nayo pokuwerengerani Durood? Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adayankha nati, Inde ngati ungafune kutero, Ndiponso adafunsa nati kodi ndingaononge magawo awiri m’magawo atatu a nthawi yanga pokuwerengerani Durood? Rasulullah (sallallahu alayhi wasallam) adati inde ngati ungafune.Swahabayo adafunsanso nati kodi ndingaonongere nthawi yanga yonse pokuwerengerani durood? Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adayankha nati” Ngati ungachite zimenezi, Allah Ta’ala adzakukwaniritsira chirichonse chomwe ukuchifuna kaya za duniya (dziko lapansi) kapena zaku Aakhirat.

Mphoto Zakulemba Mau Oti (Salallah Alayhi Wasallama)

Hassan bin Muhammad (rahimahullah) akunena kuti:

Ndidamuonapo Imaam Ahmad bin Hambal (rahimahullah) ku maloto, ndipo adati kwaine “Ungathe kuchitira umboni ndi maso ako malipiro aakulu ndi madalitso ochuluka amene akuwala patsogolo pathu amene asungiridwa anthu amene amalemba Durood kwa Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) m’mabuku mwawo”. (Al-Qawlul Badee, Pg 486)

Chidziwitso: Pamene mukulemba dzina la olemekezeka Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam), Mukuyenera kulemba mokwanirira mau oti (Sallallahu alayhi wasallam) muchiyankhulo cha charabu kapena mukhonza kulemba muchiyankhulo chilichonse. Sizili zokwanilira kulemba mofupikitsa monga S.A.W kapena P.B.H.U ndikalembende kena kalikonse kofupikitsa chifukwa kutere sizikupereka ulemu ofunika kuuwonetsa kwa Mtumiki (Sallallahu alayhi wasallam).

Check Also

Kufika Kwa Durood Ya Ummah Kwa Sayyiduna Rasulullaah (Sallallahu Alaih Wasallam)

Hazrat Hassan Bin Ali (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti "Werengani durood kwa ine kwina kulikonse komwe mungakhale popeza durood yanuyo imafikitsidwa kwa ine (kudzera mwa angelo).