Kuona Malo Ako Ku Jannah

عن أنس بن مالك قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من صلى علي في يوم الجمعة ألف مرة لم يمت حتى يرى مقعده من الجنة
(أخرجه ابن شاهني بسند ضعيف كذا في القول البديع صـ ٣٩٧)

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene anganditumizire Durood ka 1000 tsiku lachisanu, sadzamwalira kufikira ataonetsedwa malo ake ku Jannah.”

Kuwerenga Durood Kokwana Ka 1000

Shaikh Abul Hasan Baghdaadi Ad-Dariimi (rahimahullah) akulongosora, ndidakhala ndikumuona Abu Abdillah Haaamid (rahimahullah) kutulo atamwalira, ndidamufunsa kuti adakumana ndizotani ndipo (poyankha) adati, “Allah Tabaaraka wata’ala wandikhululukira komanso wandichitira chifundo. ”kenaka ndidamufunsa, “ungandiuzeko kuti ndi ntchito yanji imene imene ingakandilowetse ku Jannah. ”adandiyankha nati, udzipemphera marakah 1000 a sunnah ndipo mu rakah iliyonse udziwerenga surah Ikhlaas ka 1000, ndidamuyankha nati, “ee koma izi ndizovutilapo kuti munthu ukwanitse “ iye adati, ngati ndichoncho udziwerenga Durood ka 1000 usiku ulionse. ”Abul Hasan akupitiliza kulongosora kuti,”umu ndimmene ndinkachitira kufikira pomwe ndidamwalilira.” (Al-Qawlul Badee, Pg,259)

Check Also

Kufika Kwa Durood Ya Ummah Kwa Sayyiduna Rasulullaah (Sallallahu Alaih Wasallam)

Hazrat Hassan Bin Ali (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti "Werengani durood kwa ine kwina kulikonse komwe mungakhale popeza durood yanuyo imafikitsidwa kwa ine (kudzera mwa angelo).