Daily Archives: May 24, 2021

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La chisanu Nchinayi

25. Ngati mbali iliyonse yachiwalo chomwe ndi fardh kusambitsa pamene mukupanga wudhu yasiidwa osasambitsa, wudhu udzakhala opelewera.

Sayyiduna Umar (radhwiyallahu anhu) akunena kuti munthu anapanga wudhu nasiya malo amodzi osasambitsa kuphanzi kwake mlingo wachikhadabu poyang’anitsitsa malo amenewo Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) anamuuza iye kuti “pita ukamalizitse kupanga wudhu wako.”

 

Read More »