Kufika Kwa Durood Ya Ummah Kwa Sayyiduna Rasulullaah (Sallallahu Alaih Wasallam)

عن أبي هريرة قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم لا تجعلوا بيوتكم قبورا ولا تجعلوا قبري عيدا وصلوا علي فإن صلاتكم تبلغني حيث كنتم (سنن أبي داود، الرقم: ٢٠٤٢، وإسناده جيد كما في البدر المنير ٢٩٠/٥)

Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti ” nyumba zanu musazipange kukhala ngati ndi manda (zipangeni nyumba zanu kukhala za moyo popangilamo ntchito za bwino monga ngati swalah, kuwerenga Qur’aan majeed ndi zina zambiri. Choncho mukamatero nyumba zanu sizikhala ngati ndi manda kumene sikumachitikako ma aamaal abwino.) Ndipo manda anga musawatenge ngati ndi malo opangilapo zisangalalo, komanso mudziwerenga durood kwa ine, ndithudi mwa njira ina iliyonse Durood yo imandifika (kudzera mwa angelo) kuchokera kwina kuli konse komwe muli.”

Chikondi Cha Sahabi Pa Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam)

Sahabi wina adabwera kwa Mtumiki (sallallahu alai wasallam) ndipo adafunsa, “oh Mtumiki wa Allah (sallallahu alai wasallam) Qiyamah idzabwera liti?” Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati, waikonzekera bwanji Qiyamah imeneyi? Sahabi uja adayankha nati, oh Mtumiki wa Allah, sindikutanthauza kuti ndiri ndi swalah, kusala, ndikupereka swadaqah zochuluka, komano ndimankonda Allah ndi Mtumiki wake (sallallahu alaih wasallam) kuchokera pansi pa ntima, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “ndithudi, wina aliyense adzakhala pamodzi ndamene amankonda pa tsiku la Qiyamah.”

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akufotokoza, palibe chinthu chomwe chidawasangalatsa ma swahabah kuposa mawu amenewa amene adanenedwa ndi Mtumiki (sallallah alaih wasallam).” (Sunan At Tirmizi, #2385)

Check Also

Kuwerenga Durood Usiku Ndi Usana Wa Tsiku La Jumuah (Lachisanu)

Sayyiduna Aws bin Aws (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “tsiku lopambana kwambiri ndi tsiku la Jumuah/lachisanu, kotero, Chulukitsani kundiwerengera durood tsiku limeneli popeza durood yanu imabweretsedwa kwa ine, masahabah adafunsa kuti, “durood yathu idzakufikani bwanji mukadzamwalira poti mafupa anu adzakhala ataola?” Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati, “ndithudi Allah adailetsa nthaka kudya matupi a aneneri.”