Kugwirana Chanza Ndi Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam) Pa Tsiku Lomaliza

قال النبي صلى الله عليه وسلم من صلى علي في يوم خمسين مرة صافحته يوم القيامة (القربة لابن بشكوال، الرقم: ٨٧، وقد سكت عنه السخاوي في القول البديع صـ ٢٨٩، ويفهم من سكوته أن الحديث معمول به عنده، ولذلك ذكره في كتابه)

Zafotokozedwa kunena kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene angandiwelengere ine Durood ka 50 tsiku lirilonse, ndidzagwirana naye chanza pa tsiku la Qiyamah.”

Sayyiduna Abubakr (radhiyallahu anhu) akonzeka kuzimana china chirichonse pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam).

Nkhondo ya Badr idakali mkati, mwana wa Sayyiduna Abu bakr (radhiyallahu anhu) amene ndi Abdu-Rahman (radhiyallahu anhu) adali mbali ya adani popeza adali asadalowe chisilamu.

Patadutsa nthawi, atalowano chisilamu, ali chikhalire ndi bambo ake omwe ndi Sayyiduna Abu-Bakr Siddeeq (radhiyallahu anhu) adati, oh bambo anga okondedwa, pa nkhondo ya Badr mudayandikana ndiine nditanyamura lupanga langa kangapo konse, komano chifukwa choganizira kuti ndiinu bambo anga, sindikhale ndi maganizo oti ndikupheni.

Sayyiduna Abu-Bakr (radhiyallahu anhu) (adamuuza mwana wake kuti, ukadati ubwere pafupi ndiine tsiku limenero, sindikadakusiyasiya chifukwa unkalimbana ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). (Tareek ul Khulafa 23/1)

Check Also

Kuwerenga Durood Usiku Ndi Usana Wa Tsiku La Jumuah (Lachisanu)

Sayyiduna Aws bin Aws (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “tsiku lopambana kwambiri ndi tsiku la Jumuah/lachisanu, kotero, Chulukitsani kundiwerengera durood tsiku limeneli popeza durood yanu imabweretsedwa kwa ine, masahabah adafunsa kuti, “durood yathu idzakufikani bwanji mukadzamwalira poti mafupa anu adzakhala ataola?” Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati, “ndithudi Allah adailetsa nthaka kudya matupi a aneneri.”