Angelo Okwana 70 Kulemba Zabwino Kwa Masiku 1000

عن أبي هريرة رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من سره أن يكتال بالمكيال الأوفى إذا صلى علينا أهل البيت فليقل اللهم صل على محمد النبي الأمي وأزواجه أمهات المؤمنين وذريته وأهل بيته كما صليت على آل إبراهيم إنك حميد مجيد (سنن أبي داود، الرقم: ٩٨٢، وسكت عليه هو والمنذري في مختصره، الرقم: ٩٨١)

Sayyiduna Ibnu Abbas (radhiyallahu anhuma) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene angawerenge Durood iyi, adzakhala ndi mwayi oti angelo okwana 70 adzamulembera zabwino kwa masiku okwana 1000.

اللَّهُمَّ صَلِّ عَلَى مُحَمَّدٍ النَّبِىِّ الأُمِّيِّ وَأَزْوَاجِهِ أُمَّهَاتِ الْمُؤْمِنِينَ وَذُرِّيَّتِهِ وَأَهْلِ بَيْتِهِ كَمَا صَلَّيْتَ عَلَى آلِ إِبْرَاهِيمَ إِنَّكَ حَمِيدٌ مَجِيدٌ

Allah amulipire (Mtumiki sallallahu alaih wasallam) kudzera mwa ife monga m’mene zikuyenerekera (sawabu zimene zingapindulire ulemu wake).

Kudalitsika Kwa Ma Hadith a Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam)

Olemekezeka Abu Ahmad, Abdullah bin Bakr bin Muhammad (Rahimahullah) tsiku lina adafotokoza kunena kuti, “maphunziro amene ali opambana kwambiri komanso odalitsika komanso ndi othandiza kwambiri pano padziko lapansi komanso ku Aakhirah pambuyo poiphunzira Quran ndi maphunziro olemekezeka a mahadith a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), munthu adzadalitsika kudzera mukuphunzira ma Hadith a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) chifukwa chakuchuluka kowerenga Durood kumuwerengera Mtumiki (sallallah alaih wasallam) pamene akuwerenga mahadith a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)”. Ma hadith a Mtumiki (sallallah alaih wasallam) ali ngati minda kapena M’dimba momwe ungapeze ntundu ulionse wa chabwino chirichonse. (Al-Qawlul Badee, Pg, 287)

Check Also

Kuwerenga Durood Usiku Ndi Usana Wa Tsiku La Jumuah (Lachisanu)

Sayyiduna Aws bin Aws (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “tsiku lopambana kwambiri ndi tsiku la Jumuah/lachisanu, kotero, Chulukitsani kundiwerengera durood tsiku limeneli popeza durood yanu imabweretsedwa kwa ine, masahabah adafunsa kuti, “durood yathu idzakufikani bwanji mukadzamwalira poti mafupa anu adzakhala ataola?” Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati, “ndithudi Allah adailetsa nthaka kudya matupi a aneneri.”