Kulandila Satifiketi Yomasuridwa Ku Unaafiq Komanso Ku Moto Wa Jahannam

عن أنس بن مالك قال: قال رسول الله صلى الله عليه وآله وسلم: من صلى علي صلاة واحدة صلى الله عليه عشرا ومن صلى علي عشرا صلى الله عليه مائة ومن صلى علي مائة كتب الله له بين عينيه براءة من النفاق وبراءة من النار وأسكنه الله يوم القيامة مع الشهداء (المعجم الصغير للطبراني، الرقم: ٨٩٩، وقال الهيثمي في مجمع الزوائد (الرقم: ١٨٢٩٨): رواه الطبراني في الصغير والأوسط وفيه إبراهيم بن سالم بن شبل الهجيمي ولم أعرفه وبقية رجاله ثقات، وقال المنذري في الترغيب والترهيب (الرقم: ٢٥٦٠): وفي إسناده إبراهيم بن سالم بن شبل الهجعي لا أعرفه بجرح ولا عدالة)

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene anganditumizire Durood kamodzi ngati malipiro ya Durood Allah adzamulipira munthu ameneyo sawabu ndikumuchitira chifundo ka 10, ndipo amene anganditumizire Durood kokwana ka 10 Allah adzamulipira munthu ameneyo sawabu zokwana 100, ndipo munthu amene anganditumizire Durood kokwana ka 100 Allah adzamulembera chiphaso pakati pa maso ake yommasura ku ukamberembere komanso ku chilango cha Jahannam, Ndiponso Allah adzamulemekeza munthu ameneyo pa tsiku la Qiyaamah pomudzutsa ndi gulu la anthu omwe adafera ku nkhondo”.

Kutetezeka Ku Chilango Chifukwa Chowerenga Durood

Munthu adalota, kumalotoko adamuona munthu wina akuoneka mochititsa mantha ndimoopsya, atamufunsa kuti iye ndindani, adayankha kuti “ndiine ntchito zako zoipa” kenaka munthu uja adafunsa kuti “nankha ndingatetezeke bwanji kwa iweyo?” iye adayankha kuti: ungadziteteze pochulukitsa kuwerenga Durood Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) nthawi ndi nthawi”. (Al-Qawlul Badee, Pg,260)

Check Also

Kuona Malo Ako Ku Jannah

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene anganditumizire Durood ka 1000 tsiku lachisanu, sadzamwalira kufikira ataonetsedwa malo ake ku Jannah.”