Kupeza duwa ya Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) chifukwa chowerenga Durood pa tsiku la Jumuah

عن عمر بن الخطاب رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال: أكثروا الصلاة علي في الليلة الزهراء واليوم الأغر فإن صلاتكم تعرض علي فأدعو لكم وأستغفر (القربة لابن بشكوال، الرقم: ١٠٧، وسنده ضعيف كما في القول البديع صـ ٣٣٥)

Sayyiduna Umar bin Khattwaab (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: Chulukitsani kundiwerengera Durood pa tsiku la Jumuah popeza Durood yanu imafikitsidwa kwa ine ndipo kenako ndimakupangirani duwa kupempha Allah kuti akukhululukireni machimo anu.

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akhala limodzi ndikudzipeleka pamanso pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) ndi swahabah m’modzi amene ndi otchuka kwabasi, palibe swahabah wina amene adafotokoza ma Hadeeth ochuluka kwambiri kuposa iyeyu, analowa chisilamu m’nchaka cha 7 A.H. ndipo kufikira pamene Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamwalira m’nchaka cha 11 A.H. adakhalabe ali ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kwa zaka zinayi zokha (4), anthu ambiri ankadabwa kuti zikutheka bwanji iyeyu kukumbukira ma Hadeeth ochuluka choncho kwa kanthawi kochepa.

Mwini wake akulongosora motere:

Anthu akudabwa kuti zikutheka bwanji kuti ndidalongosora ma Hadeeth ambiri, nkhani ndi yoti abale anga ma Muhaajir adatangwanika ndikuchita malonda ndipo ma Ansaar adatangwanika ndi ulimi pamene ine nthawi zonse ndidali ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), ndidali m’gulu la anthu a Suffah. ndidalibe nazo zoti ndidzikayang’ana zakudya. Ndidali chikhalire ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), okhutitsidwa ndi chakudya chochepa chomwe ndinkapatsidwa, nthawi zina ndinkatsala ndekha ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) wina aliyense kulibe.

Tsiku lina ndidamudandaulira Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) za Kufooka kwa nzeru zanga, iye adandiuza kuti, “tambasura nsalu yako.” Mwachanguchangu ndidapanga zimenezo kenaka adandipatsa saini ndi manja ake odalitsika mu nsalu yangamo ndipo adati, “tsopano uzikutile munsalumo.” Ndidazipilingiza m’nkhosi ndipo kuyambira pomwepo sindidaiwalenso zinthu zomwe sindinafune zoti ndiziiwale. (Saheeh Bukhari, #2047)

Check Also

Munthu Waumbombo

Sayyiduna Husain (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, munthu waumbombo kwambiri ndi amene amati akanva dzina langa samandifunira zabwino.