Madalitso okamuzonda/kumuyendera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

عن ابن عمر عن النبي صلى الله عليه وسلم قال من زار قبري بعد موتي كان كمن زارني في حياتي (المعجم الأوسط، الرقم: ٢٨٧) رواه الطبراني والدارقطني والبيهقي وضعفه كذا في الإتحاف وفي المشكوة برواية البيهقي في الشعب بلفظ : من حج فزار قبري بعد موتي كان كمن زارني في حياتي واستدل به الموفق في المغني على استحباب الزيارة (فضائلِ حج صـ ١٨٤)

Sayyiduna Ibnu Umar (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “munthu amene angandiyendere Ine ndikadzamwalira ziri ngati wandiyendera Ndidakali ndi moyo.”

Kuwala kwa Durood pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

Sayyiduna Abul Qaasim Marwazi (rahimahullah) akufotokoza:

Ine pamodzi ndi bambo anga tinkawerenga mahadeeth, usiku tidalota maloto ndipo kumalotoko tidaona kuti malo amene tidakhalawo padadzabwera kuwala komwe kudakafika mpakana kumitambo. Wina adafunsa kuti ndichani chabweretsa kuwala kotere. Zinanenedwa kuti kuwalaku kudabwera kamba ka kuwerengedwa kwa Durood kumuwerengera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kumene awiriwa amapanga akamawerenga hadith. (Al Qawlul Badee, Pg,491)

Check Also

Kuwerenga Durood M’mawa Ndi Madzulo

Sayyiduna Abu Dardaa (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “munthu amene angandifunire zabwino pondiwerengera Durood kokwana ka khumi m’mawa ulionse komanso kumadzulo kulikonse adzapeza nawo pempho langa la Shafaa patsiku lachiweruzo.”