Mngelo amene amaima pa manda a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndikumapeleka durood imene anthu apanga kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

عن عمار بن ياسر رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه و سلم إن الله وكل بقبري ملكا أعطاه الله أسماء الخلائق وفي رواية أسماع الخلائق فلا يصلي علي أحد إلى يوم القيامة إلا أبلغني باسمه واسم أبيه هذا فلان بن فلان قد صلى عليك (رواه البزار كما في الترغيب والترهيب، الرقم: 2574، قال الهيثمي: رواه البزار وفيه ابن الحميري واسمه عمران يأتي الكلام عليه بعده … قال البخاري: لا يتابع على حديثه وقال صاحب الميزان: لا يعرف ونعيم بن ضمضم ضعفه بعضهم، وبقية رجاله رجال الصحيح كذا في مجمع الزوائد، الرقم: 17291)

Ammaar bin Yaasir (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adati: “Allah Ta’ala adasankha Mngelo oti akhale pambali pa manda a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), Mngelo amene Allah adampatsa nzeru zodziwa maina (mu hadith ina zanenedwa kuti adapatsidwa kuthekera kokunva mawu) a zolengedwa zomwe zikutanthauza kuti palibe munthu amene angandiwelengere duruud kufikira tsiku la Qiyaamah kupatula kuti (Mngeloyu) amafikitsa duruuduyo kwa ine pamodzi ndi dzina lamunthuyo ndilabambo ake (adzanena kuti) uyu ndi uje mwana wa uje yemwe wakuwerengera duruud.’’

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akhala limodzi ndikudzipeleka pamanso pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) ndi swahabah m’modzi amene ndi otchuka kwabasi, palibe swahabah wina amene adafotokoza ma Hadith ochuluka kwambiri kuposa iyeyu, analowa chisilamu m’nchaka cha 7 A.H. ndipo kufikira pamene Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamwalira m’nchaka cha 11 A.H. adakhalabe ali ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kwa zaka zinayi zokha (4), anthu ambiri ankadabwa kuti zikutheka bwanji iyeyu kukumbukira ma Hadith ochuluka choncho kwa kanthawi kochepa.

Mwini wake akulongosora motere:

Anthu akudabwa kuti zikutheka bwanji kuti ndidalongosora ma Hadith ambiri, nkhani ndi yoti abale anga ma Muhaajir adatangwanika ndikuchita malonda ndipo ma Ansaar adatangwanika ndi ulimi pamene ine nthawi zonse ndidali ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), ndidali mgulu la anthu a Suffah. ndidalibe nazo zoti ndidzikayang’ana zakudya. Ndidali chikhalire ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), okhutitsidwa ndi chakudya chochepa chomwe ndinkapatsidwa, nthawi zina ndinkakhala ndekha ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) wina aliyense kulibe.

Tsiku lina ndidamudandaulira Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) za Kufooka kwa nzeru zanga, iye adandiuza kuti, “tambasura nsalu yako.” Mwachanguchangu ndidapanga zimenezo kenaka adandipatsa saini ndi manja ake odalitsika mu nsalu yangamo ndipo adati, “tsopano uzikutile munsalumo.” Ndidazipilingiza mnkhosi ndipo kuyambira pomwepo sindidaiwalenso zinthu zomwe sindinafune zoti ndiziiwale. (Saheeh Bukhari, # 2047)

Check Also

Kuona Malo Ako Ku Jannah

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene anganditumizire Durood ka 1000 tsiku lachisanu, sadzamwalira kufikira ataonetsedwa malo ake ku Jannah.”