Mawu a Adhaan

Mu Adhaan muli magawo amawu okwana asanu ndi awiri, mawu asanu ndi awiriwa atchulidwa mmusimu:[1]

1. Poyamba mudzanena mawu awa:

اَللهُ أَكْبَرَ اللهُ أَكْبَرْ

Allah ndi wankulu, Allah ndi wankulu

اَللهُ أَكْبَرَ اللهُ أَكْبَرْ

Allah ndi wankulu, Allah ndi wankulu

2. Pachiwiripa mudzanena mawu anayi awa koma mudzayamba ndikunena motsitsa mawu ndipo kenako mudzakweza mawu.

أَشْهَدُ أَلَّا إِلٰهَ إِلَّا اللهْ

Ndikuikira umboni kuti palibe wina opembedzedwa mwachoonadi koma Allah.

أَشْهَدُ أَلَّا إِلٰهَ إِلَّا اللهْ

Ndikuikira umboni kuti palibe wina opembedzedwa mwachoonadi koma Allah.

أَشْهَدُ أَنَّ مُحَمَّدًا رَّسُوْلُ اللهْ

Ndikuikira umboni kuti Muhammad (sallallahu alaih wasallam) ndi mthenga wa Allah.

أَشْهَدُ أَنَّ مُحَمَّدًا رَّسُوْلُ اللهْ

Ndikuikira umboni kuti Muhammad (sallallahu alaih wasallam) ndi mthenga wa Allah.

3. Kenaka mudzanena mawu awa.

حَيَّ عَلٰى الصَّلَاةْ

Bwerani mudzaswali

حَيَّ عَلٰى الصَّلَاةْ

Bwerani mudzaswali

4. Kenako nenani mawu awa:

حَيَّ عَلٰى الْفَلَاحْ

Bwerani kuchipulumutso

حَيَّ عَلٰى الْفَلَاحْ

Bwerani kuchipulumutso

5. Kenako naneni mawu awa:

اَللهُ أَكْبَرَ اللهُ أَكْبَرْ

Allah ndi wankulu, Allah ndi wankulu

6. Ndipo Pamapeto pake nenani mawu awa:

لَا إِلٰهَ إِلَّا اللهْ

Palibe Mulungu wina koma Allah.


[1] أما احكام المسألة فمذهبنا أن الأذان تسع عشرة كلمة كما ذكر بإثبات الترجيع وهو ذكر الشهادتين مرتين سرا قبل الجهر وهذا الترجيع سنة على المذهب الصحيح الذي قاله الأكثرون فلو تركه سهوا أو عمدا صح أذانه وفاته الفضيلة (المجموع شرح المهذب 3/71)

Check Also

Mawu A Iqaamah Komanso Njira Ya Sunnat Yopangira Iqaamah

1. Mawu a Iqaamah ndichimodzimodzi ndi azaana. Koma popanga iqaamah mukuyenera kunena kamodzikamodzi kupatula mawu …