Katchuridwe Koyenera Ka Mawu a Adhaan

Popanga Adhaan opangayo akuyenera kuwatchura mawu onse moyenera pachifukwa chimenechi pali mfundo zimene zikuyenera kutsatiridwa.

1. pamene mukuwerenga mawu oti راَللهُ أَكْبَرَ اللهُ أَكْبَرْ (raa) amene akupezeka pa أَكْبَرْ oyambilira mudzamuwerenga ndi fat-hah (ــَـ) mukamamulumikiza ndi liwu loti اَللهُ (Allahu).

2. mukamadzanena mawu oti أَشْهَدُ أَلَّا إِلٰهَ إِلَّا اللهْ liwu loti أَلَّا mudzaliwerenga popanda kulidzadzitsa mkamwa. Ndipo tashdeed (ــّـ) yemwe ali pa ل (laam) asalimbitsidwe kodutsa muyeso ndicholinga chofuna kukoka manvekedwe a ل (laam). chimodzimodzinso tashdeed (ــّـ) pa م (meem) ndi ر (raa) asachitidwe modutsa muyezo.

Sukuun (ــْـ) yemwe akupezeka pa ش (sheen) anveke bwinobwino mondondozana ndi ه (haa). osachotsa sukoon ndi هـ (haa) polumikiza هـ (haa) ndi ش (sheen) ponena kuti “ashadu” popanda kumutchura هـ (haa) olo mpang’ono. Ndipo katchuridwe koyenera ndi “ash-ha-du”.

3. Pamene mukuwerenga mawu oti أَشْهَدُ أَنَّ مُحَمَّدًا رَّسُوْلُ اللهْ liwu loti أَنَّ (anna) lisatsindikizidwe kwambiri ndi cholinga choti mukoke manvekedwe a ن (noon) kwambiri kuposa mlingo opangira ghunnah.

4. Mukamanena mawu oti حَيَّ عَلٰى الصَّلَاةْ tashdeed (ــّـ) yemwe ali pa ي (yaa) m’mawu oti حَيَّ (hayya) akufunika kuwerengedwa bwinobwino. ي (yaa) asawerengedwe popanda tashdeed ponena kuti “haya”m’malo monena kuti “hayya”. chimodzimodzinso chilembo cha ع (ain) m’mawu oti على (ala) akuyenera kutchuridwa bwinobwino.

Pamene mukuima pa mawu oti الصَّلَاةْ (salaah), ة (taa) adzawerengedwa ndi sukoon (ــْـ) zomwe zikusonyeza kuti adzakhala هـ (haa), osamutchura ة (taa) ponena kuti hayya alas salaat. Chimodzimodzinso mudzaonetsetsa kuti sakusintha kunveka kuti ح (haa).

5. Potchura mawu oti حَيَّ عَلٰى الْفَلَاحْ poima pa mawu oti الْفَلَاحْ (falaah), onetsetsani kuti mukumutchura m’mene aliri kuti ndi ح (haa) osati ngati هـ.

Check Also

Mawu A Iqaamah Komanso Njira Ya Sunnat Yopangira Iqaamah

1. Mawu a Iqaamah ndichimodzimodzi ndi azaana. Koma popanga iqaamah mukuyenera kunena kamodzikamodzi kupatula mawu …