Kuthandizidwa pa Mlatho wa Siraat

عن عبد الرحمن بن سمرة قال: خرج رسول الله صلى الله عليه وسلم فقال: إني رأيت البارحة عجبا … ورأيت رجلا من أمتي يزحف على الصراط مرة ويجثو مرة ويتعلق مرة فجاءته صلاته علي فأخذت بيده فأقامته على الصراط حتى جاوز ورأيت رجلا من أمتي انتهى إلى أبواب الجنة فغلقت الأبواب دونه فجاءته شهادة أن لا إله إلا الله فأخذته بيده فأدخلته الجنة (الأحاديث الطوال للطبراني صـ 273، وإسناده ضعيف كما في مجمع الزوائد، الرقم: 11764)

Sayyiduna Abu Rahmaan bin Samurah radhiyallahu anhu akufotokoza kuti tsiku linalake Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adatiuza kuti usiku ndinalota maloto odabwitsa, ndinamuona munthu ochokera mu Ummah wanga akuoloka Mlatho wa Siraat, pena amaoneka akukwawa ndipo pena amaoneka akudzikhukhudza chammbuyo Ndipo pena amatsakamira pa Mlatho kufuna kugwera mmdzenje la Jahannam ndipo mwadzidzidzi kudabwera duruud imene ankakonda kuwerenga padziko lapansi pano ndipo inamugwira dzanja ndikumuolotsa.

Mwala umene udapeleka salaam kwa Mtumiki sallallahu alaih wasallam

Sayyiduna Jaabir bin Samurah radhiyallahu anhu akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati ndikuuzindikira mwala umene unkandipatsa salaam ndisadalandire utumiki, ndithudi ndikumaukumbukira ngakhale panopa. (Saheeh Muslim, #2277)

Check Also

Mngelo Amene Amayima pa Manda Odalitsika a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti Apereke Durood ya Ummah kwa Rasulullah Ummah

Sayyiduna Ammaar (radhiyallahu anhu) kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Allah adasankha mngelo amene amakhala pafupi ndi manda anga kuti adzindifikitsira Durood ya Ummah wanga ndipo adawazindikiritsa maina (ma hadith ena amanena kuti adapatsidwa mphamvu yozindikira mawu a anthu osiyanasiyana) zomwe zikutanthauza kuti palibe munthu amene angandiwelengere Durood tsiku lina lirilonse mpaka pa Qiyaamah pokhapokha mngeloyu amafikitsa kwa ine dzina la munthuyo komanso la bambo ake. (Amanena kuti) uyu ndi uje mwana uje amene wakuwerengerani Durood.