Tafseer Ya Surah Alaq

اقْرَأْ بِاسْمِ رَبِّكَ الَّذِي خَلَقَ ﴿١﴾ خَلَقَ الْإِنسَانَ مِنْ عَلَقٍ ﴿٢﴾ اقْرَأْ وَرَبُّكَ الْأَكْرَمُ ﴿٣﴾ الَّذِي عَلَّمَ بِالْقَلَمِ ﴿٤﴾ عَلَّمَ الْإِنسَانَ مَا لَمْ يَعْلَمْ ﴿٥﴾ كَلّا إِنَّ الإِنسانَ لَيَطغىٰ ﴿٦﴾ أَن رَاهُ استَغنىٰ ﴿٧﴾ إِنَّ إِلىٰ رَبِّكَ الرُّجعىٰ ﴿٨﴾ أَرَءَيتَ الَّذى يَنهىٰ ﴿٩﴾ عَبدًا إِذا صَلّىٰ ﴿١٠﴾ أَرَءَيتَ إِن كانَ عَلَى الهُدىٰ ﴿١١﴾ أَو أَمَرَ بِالتَّقوىٰ ﴿١٢﴾ أَرَءَيتَ إِن كَذَّبَ وَتَوَلّىٰ ﴿١٣﴾ أَلَم يَعلَم بِأَنَّ اللَّـهَ يَرىٰ ﴿١٤﴾ كَلّا لَئِن لَم يَنتَهِ لَنَسفَعًا بِالنّاصِيَةِ ﴿١٥﴾ ناصِيَةٍ كـٰذِبَةٍ خاطِئَةٍ ﴿١٦﴾ فَليَدعُ نادِيَهُ ﴿١٧﴾ سَنَدعُ الزَّبانِيَةَ ﴿١٨﴾ كَلّا لا تُطِعهُ وَاسجُد وَاقتَرِب ﴿١٩﴾

Werenga mdzina la mbuye wako yemwe adalenga (chinachirichonse), adamulenga munthu kuchokera ku dontho la magazi, ndipo mbuye wako ndi olemekezeka, amene adamuphunzitsa munthu kulemba (pogwiritsa ntchito) cholembera, adamuphunzitsa munthu zinthu zomwe zankazidziwa, kotero munthu wapsyola malire chifukwa akudzitenga kuti iye atha kudziimira payekha, ndithudi, kwa mbuye wanu ndiye kobwelera, kodi wamuona uyo (Abu Jahal) amene akuletsa kapolo (Muhammad sallallahu alaih wasallam) akaima kuti apemphere, tandiuza kodi ngati iyeyo (kapolo wanga – Muhammad (sallallah alaih wasallam) ali pa chiongoko kapena akuwalamulira anthu kuchita ntchito zabwino nankha Abu Jahal ali ndi mphamvu zanji kuti amuletse)? Tandiuza ngati iyeyo (Abu Jahal) angakane ndikubwelera m’mbuyo, kodi sakuzindikira kuti Allah Ta’ala akuona zomwe oye akuchhitazo? Sichoncho, ngati sasiya zomwe akuchitazo timukoka tsitsi la paliombo (tiligwira mwamphanvu liombi lake ndikukamponya kumoto. Basi, ayitane gulu lakero ifenso tiitana asilikali athu a kumoto, sichoncho, usamunvere ameneyo oh Muhammad (sallallahu alaih wasallam) (pazimene akukuletsazo, ndipo gwetsa nkhope yako pansi ndipo udziyandikitse kwa mbuye wako.

اقْرَأْ بِاسْمِ رَبِّكَ الَّذِي خَلَقَ ﴿١﴾ خَلَقَ الْإِنسَانَ مِنْ عَلَقٍ ﴿٢﴾ اقْرَأْ وَرَبُّكَ الْأَكْرَمُ ﴿٣﴾ الَّذِي عَلَّمَ بِالْقَلَمِ ﴿٤﴾ عَلَّمَ الْإِنسَانَ مَا لَمْ يَعْلَمْ ﴿٥﴾ كَلّا إِنَّ الإِنسانَ لَيَطغىٰ

Werengani mdzina la mbuye wako yemwe adalenga (chinachirichonse), adamulenga munthu kuchokera ku dontho la magazi, ndipo mbuye wako ndi olemekezeka, amene adamuphunzitsa munthu kulemba (pogwiritsa ntchito) cholembera, adamuphunzitsa munthu zinthu zomwe zankazidziwa,

Mu Qur’an yonse yolemekezeka, MA Ayah asanu amenewa ndiye oyambilira kubvumbulutsidwa, chibvumbulutso chonse chidayamba ndikuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) amalota kutulo, China chilichonse chomwe angachione kutulo chimatsimikizika kummawa kwake kukacha.

Ndipo kenaka kudankomera kubindikira ndikumakhala malo a yekha kuphanga lotchedwa Hirah ku Jabal-Nuur. Ankatengeratu chakudya ndikumabindikira kuphangako kupanga Ibaadah yosiyanasiyana kunkumbukira Allah kwa nthawi yaitali. Nthawi zina ankabindikira kwa masiku khumi, nthawi zina makumi awiri ndipo nthawi zina ankabindikira kwa mwezi onse.

Tsiku lina ali chikhalire kuphangako mwadzidzidzi kudabwera m’ngero yemwe akutchedwa kuti Jibril alaih salaam ndikumuuza kuti anene kuti “iqra” werenga. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha kuti ما أنا بقارئ (sindingathe kuwerenga) kenaka Jibril (alaih salaam) adamukumbatira ndikumufinya koti mpakana adayamba kunva kuwawa. Kenaka adamusiya ndamuuzanso kuti awerenge. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankhamso kuti sangathe kuwerenga ndipo adamukumbatira mwamphanvu ndikumufinya pa chidali ndipo kenaka adamusiya ndikumuuza kuti “iqra”.

Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha kachitatu kuti sangathe kuwerenga. Jibril (alaih salaam) adamukumbatura kachitatu ndipo adamusiyanso, pamenepo adawerenga ma Aya asanu amenewa. Nthawi imeneyi ndi yomwe Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adalandilira utumiki.

Pambuyo pa nkumano oyambawu okumana ndi Jibril (alaih salaam), Mtumiki Muhammad (sallallahu alaih wasallam) adabwelera kunyumba ali okhumudwa ndi odandaula kuganizira kuti akwaniritsa bwanji udindo umenewu wa utumiki adalongosora nkhani yonse yokumana ndi Jibril (alaih salaam) kwa Sayyidatu Khadija (radhiyallahu anha) adamukhazikitsa mtima pansi ndikumutsimikizira kuti ndithu Allah sangamuyalutse.

Bibi Khadija (radhiyallahu anha) adamuuza Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti “ilandire nkhani yabwino yochoka kwa Allah, ndikulumbilira mwa Allah, Allah sangakuyalutse ndithudi, iwe ndi munthu amene umalimbikitsa zomanga ubale, nthawi zonse umayankhula zoona zokha zokha, umasenza ntolo wa anthu omwe ali mmavuto, umamusakira chakudya munthu yemwe ndi osauka, umamusamalira mlendo akabwera pakhomo komanso umawathandiza anthu omwe akumana ndi mavuto monga chilala ndizina.

Kudzera mukukhadzikitsidwa mtima pansi komwe Bibi Khadija adamnchitira, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) mtima wake udakhanzikika pansi, Bibi Khadija (radhiyallahu anha) adali mzimayi oyambilira kulowa chisilamu pamaso pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam).

اقْرَأْ بِاسْمِ رَبِّكَ الَّذِي خَلَقَ ﴿١﴾ خَلَقَ الْإِنسَانَ مِنْ عَلَقٍ ﴿٢﴾

Werenga Mdzina la Mbuye Wako amene adalenga chinachirichonse. adamulenga munthu kuchokera kudontho la magazi owundana.

Kumayambiliro kwa surah imeneyi, Allah akumulamulira Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) kuyamba kuwerenga potchula dzina la Allah. Kotero, tikamayamba kuwerenga Quraan Majeed tikuyenera kuyamba ndi mawu oti “Bismillahir Rahmaanir Rahiim”.

Mndime zimenezi Allah akumudziwitsa munthu kuti kodi Allah pa yekha ndindani komanso akumudziwitsa kuti iye ndi amene adalenga chinachirichonse. Allah akumukumbutsanso munthu za komwe adachokera komanso chiyambi chake. Chiyambi cha munthu ndi magazi omwe ndi onyansa mmaonekedwe. Koma Allah wamulemekeza pompatsa thupi komanso maonekedwe okongora. Ndiponso wampatsa munthuyo nzeru zopitira patsogolo mmampunziro komanso Taqwa ndizina kufikira mpaka akuwaposa angero.

اقْرَأْ وَرَبُّكَ الْأَكْرَمُ ﴿٣﴾

Werenga ndipo mbuye wako ndi mfulu (olemekezeka)

Mndime imeneyi Allah akulamulanso zowerenga potchulanso kuti iye ndiye mwini madalitso, Allah akulozera kuti kudzera muchifundo chake chokha munthu akhonza kukwanitsa kuwerenga Quraan komanso kukumbukira Allah.

الَّذِي عَلَّمَ بِالْقَلَمِ ﴿٤﴾ عَلَّمَ الْإِنسَانَ مَا لَمْ يَعْلَمْ ﴿٥﴾

Amene adaphunzitsa ndicholembera, adamuphunzitsa munthu zinthu zomwe sankazidziwa.

Allah adamuphunzitsa munthu kagwiritsidwe ntchito kacholembera pogwiritsa ntchito nzeru zosiyanasiyana zomwe zingamuthandize kupita chitsogolo mu Dini ndikubwera Chifupi ndi Allah. Monga Allah adamuphunzitsa munthu kulemba ndi cholembera, Allah alinazonso mphamvu zomuphunzitsira munthu popanda kugwiritsa ntchito cholembera. Kotero Allah wamudalitsa munthu pompatsa zinthu zingapo monga kuona, kumva, kumvetsa komwe kumamuthandiza munthu kuti aphunzire ndikupeza zotsatira zabwino.

كَلّا إِنَّ الإِنسانَ لَيَطغىٰ ﴿٦﴾ أَن رَاهُ استَغنىٰ ﴿٧﴾ إِنَّ إِلىٰ رَبِّكَ الرُّجعىٰ

Sichoncho, ndithu munthu wadutsa malire, akudzitenga kuti iye ndi odzidalira.

Ngakhale Allah adamudalitsa munthu ndi zinthu zimene zimamuthandizira kuti achinvetse chinachake, amaiwala kuti kuti Allah ndi amene alindi udindo omudalitsa ndikumpatsa madalitso onse komanso mtendere umene iye akusangalala nawowo, amayamba kudzikunikira zonse zimene iye alinazo ndikumanena kuti adazipezera yekha, ndipo amamuyiwaliratu Allah mwini kupeleka, kotero amakhala umoyo otsatira zilakolako zake  komanso olumpha malire.

Pa chifukwa chimenechi Allah akutiuza chiyambi cha zonsezi kuti sichina koma kudzitenga kuti iye ndi odzidalira, amaganiza kuti ngati alindi chuma kapena udindo atsatira bwanji zokamba za wina wake, ngati munthu angakumbukire za Kufooka kwake nadzichepetsa ndikusakhala ndi mtima osayang’ana zabwino.

Munthu amene Allah akunena mu Ayah imeneyi, ndi munthu amene amazitama mwa iye yekha kuti ndi woziyimira pa yekha ndipo wafanana zochitika zake ndi Abu Jahal. Ngakhale zili choncho Allah Ta’ala adamudalitsa ndi chuma, mphamvu, ulemelero ndi kulandira ulemu, koma chonsecho adasankha kukanira Allah Ta’ala, kutengera pa zonse zomwe amapindula pa khama lake. Ngakhale iye anali wa kubanja la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) iye adamkana Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) utumiki wake ndipo adagwira ntchito yolimbana ndi chisilamu.

إِنَّ إِلىٰ رَبِّكَ الرُّجعىٰ ﴿٨﴾

Ndithudi kwa mbuye wako ndiye kobwelera

Mu ndime imeneyi Allah a kumukumbutsa munthu kuti pakhalekhale tsiku lina adzamwalira ndikubwelera kwa Allah. Zingavute bwanji adzayenera akuyenera kudzasamuka umoyo wa padziko lapansi ndikupita ku umoyo umene ulinkudza omwe ndi wamuyaya Kumene atadzaunikidwe ntchito zake. Ngati munthu angakhale ndi maganizo a umoyo umene ulinkudza ndikumuopa kaundula wa tsiku limeneli adzakhala mu njira yoongoka.

أَرَءَيتَ الَّذى يَنهىٰ ﴿٩﴾ عَبدًا إِذا صَلّىٰ ﴿١٠﴾ أَرَءَيتَ إِن كانَ عَلَى الهُدىٰ ﴿١١﴾ أَو أَمَرَ بِالتَّقوىٰ ﴿١٢﴾ أَرَءَيتَ إِن كَذَّبَ وَتَوَلّىٰ ﴿١٣﴾ أَلَم يَعلَم بِأَنَّ اللَّـهَ يَرىٰ ﴿١٤﴾

Kodi wamuona (Abu Jahal) yemwe akuletsa kapolo (yemwe ndi) Muhammad (sallallah alaih wasallam) kuswali pamene akuima kuti apemphere, tandiuza ngati kapoloyo (Muhammad) sallallahu alaih wasallam ali pa chiongoko komanso kulamulira kuchita ntchito zabwino, kodi Abu Jahal alindi mphamvu zomuletsa kutero, tandiuza kodi ngati iye (Abu Jahal) angakane ndikutembenukira kumbuyo kodi sakudziwa kuti Allah akuona.

Mndime zimenezi Allah akumutamanda Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) komanso akunena zoti iye (Muhammad sallallahu alaih wasallam ali pachiongoko kulamulira anthu kuchita ntchito zabwino. Tsopano Abu Jahal ndiye Allah akumudzudzula ndikumuchenjeza pachifukwa chokana chilungamo kuchitembenukira chisilamu komanso kumuletsa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kumpembedza Allah, ankapsya mtima komanso kuyesetsa mu njira iliyonse kumuletsa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuswali.

Tsiku lina Abu Jahal adamuina Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) akuswali munzikiti olemekezeka wa Haram, adanyansidwa kwambiri ndikumufunsa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti kodi sindinakuletse kuti uswamaswali, ndikadzakuinanso ukuswali ndidzakuponda khosi.

Allah adamulonjeza Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti iye sadzalora kuti Abu Jahal amukhudze Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndikukwaniritsa chiwembu chake, ndipo kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndi otetezedwa ndi Allah.

Allah akuyankhula kunena kuti: kodi (Abu Jahal) sakudziwa kuti Allah akumuona, Mndime imeneyi muli uthenga onena kuti Allah adzachitanaye Abu Jahal monga kukufunikira komanso adzamuononga ku moto wa Jahannam.

كَلّا لَئِن لَم يَنتَهِ لَنَسفَعًا بِالنّاصِيَةِ ﴿١٥﴾ ناصِيَةٍ كـٰذِبَةٍ خاطِئَةٍ ﴿١٦﴾ فَليَدعُ نادِيَهُ ﴿١٧﴾

Sichoncho ngati iye (Abu Jahal) asasiye zoipa zimene akuchitazo timukoka tsitsi la paliombo mwamphanvu ndikukamponya kumoto wa Jahannam, liombo labodza ndiponso lochimwa, Basi aliitane gulu lakero ifenso tiitana a Zabaania angero a kumoto, Ayi ndithu usamumvere pa zomwe akukuletsanzo koma gwetsa nkhope yako pansi ndipo udziyandikitse kwa mbuye wako.

Abu Jahal adali odzadza ndi mtima odzikweza odzimva chifukwa cha chuma komanso utsogoleri umene adalinawo, ankaziona kuti ali ndi anthu omuthandizira, ndipo nthawi ina ikiyonse ngati angawaitane ankakhala tcheru kutsati zimene iye anganene, kotero, mndime zimenezi Allah Tabaaraka wata’ala akumuchenjeza Abu Jahal zachilango choopsya chhomwe angakakumane nacho ngati angamuletse Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuswali, Allah akunena kuti: ayenera asamale chifukwa ngati sasiya zomwe akuchitazo adzamukoka ndi tsitsi lake la paliwombo chiliwombo chambodza. “Ndiyetu awaitane anthu akewo (ngati akufuna) ifenso tiitana asilikali athu akumoto omwe ndi angelo ” mukunena kwina, angelo athu adzamuononga iyeyi ndikumuthandizira Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ngati angapange chiganizo chosafuna kusiya zomuletsa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuswali ndiye kuti angelo athu adzamunyenyanyenya.

Zanenedwa kuti ulendo wina wake Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ali pa sajdah Abu Jahal adapita pomwepo ndicholinga chofuna kupanga chiwembu choti amuponde pakhosi, komano atayandikira mwadzidzidzi adagwidwa ndi mantha ndipo adabwelera, azinzake atamufunsa kuti ndi chifukwa chani wabwelera kumachita kuti analumbira kuti akaponda khosi la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)? Iye adayankha kunena kuti: nditafika pamalopo ndidaona chidzenje chamoto ndipo ndidaonamonso zinthu zina zake zikuuluka mmenemomo, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti amenewo ndi angelo ndipo akadangoyerekeza kuponda khosi langa akadamunyenyanyenya.

Check Also

Tafseer Ya Surah Qadr

بِسمِ اللّٰـهِ الرَّحمٰنِ الرَّحيمِ اِنَّا أَنزَلنٰهُ فى لَيْلَةِ القَدْرِ ﴿١﴾ وَما أَدرىٰكَ ما لَيلَةُ القَدرِ ﴿٢﴾ لَيلَةُ القَدرِ خَيرٌ …