Sawabu zapaderadera ukawerenga Durood ka 100

عن أبي هريرة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال من صلى علي عشرا صلى الله عليه مئة ومن صلى علي مئة صلى الله عليه ألفا ومن زاد صبابة وشوقا كنت له شفيعا وشهيدا يوم القيامة (أخرجه أبو موسى المديني بسند قال الشيخ مغلطاى لا بأس به، كذا في القول البديع صـ 236)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati” amene angawerenge durood ka 100 Allah adzamudalitsa ndi madalitso 100, ndipo amene angandifunire madalitso ka 100 adzamuchitira chifundo munthu ameneyo ka 1000, ndipo wina aliyense amene angachulukitse kundifunira zabwino zabwino chifukwa chondikondetsetsa kwambiri I komanso ndicholinga chofuna Kupeza sawabu ndidzamuikira kumbuyo munthu ameneyo pa tsiku lachiweruzo.

Nkhani ya munthu amene adalemba chitabu chotchedwa Dalaailul Khairaat

Zanenedwa nkhani yokamba za munthu amene adalemba chitabu chotchedwa Dalaailul Khairaat kuti tsiku lina lake adali pa ulendo. Ali mkatikati mwa ulendo wake iye adafuna madzi kuti apangire wudhu, mwamwayi adachipeza chitsime penapake, komano chifukwa chopanda chititi komanso chingwe choti atungire sadathe kukwanitsa kuti atunge madziwo, chifukwa choidandaulira swalah adali okhumudwa kwabasi ndikudandaula.

Ali chikhalire chonchi mtsikana wina yemwe adali osatha msinkhu panthawiyi adamuona munthu uja ndipo adabwera pafupi ndikumufunsa za vuto lake kuti lidali chani, munthu uja adalongosora vuto lakelo, mtsikana uja nthawi yomweyo adalavulira mchitsimemo zomwe zidachititsa kuti madzi aja achuluke ndikufika mpakana pamwamba pa chhitsimechi.

Ataona zozizwitsazi adali odabwa kwambiri ndipo adamufunsa mtsikanayo kuti mphamvu zimenezo adazitenga kuti, Mtsikana adayankha ponena kuti awa ndi madalitso obwera chifukwa chowerenga duruud yomwe ndidamupemphera malitso Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Ndipo kudzera mu zodabwitsa zimene Mtsikanayu adaonetsa zidamupangitsa Munthuyu kuti alembe chitabu chotchedwa Dalaailul Khairaat.

Allaamah Zardaq (rahimahullah) a kulongosora kuti pa infa ya munthu yemwe adalemba chitabu chotchedwa Dalaailul Khairaat Fungo lonunkhira kwambiri linkanveka kuchokera pa manda a munthu ameneyu. Awa adali madalitso odza kamba kowerenga Durood. (Fadail – Durood, Pg152)

Check Also

Kuwerenga Durood Pamkumano

عن أنس عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: ما من عبدين متحابين في الله …