Sawabu zofanana ndikupereka sadaqah ukawerenga Duruud

عن أبي سعيد الخدري رضي الله عنه عن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال أيما رجل مسلم لم تكن عنده صدقة فليقل في دعائه اللهم صل على محمد عبدك ورسولك وصل على المؤمنين والمؤمنات والمسلمين والمسلمات فإنها زكاة وقال لا يشبع مؤمن خيرا حتى يكون منتهاه الجنة (صحيح ابن حبان، الرقم: ٩٠٣ ،وإسناده حسن كما في مجمع الزوائد، الرقم: ١٧٢٣٢)

Olemekezeka Abu Sa’eed khudri (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “Msilamu amene alibe kena kalikonse kuti apereke sadaqah adziwerenga duruud iyi mkatikati mwa duwa yake popeza idzampezetsa iyeyo sawabu zoti wapeleka sadaqah ndikumuyeretsa ku machimo.

اللهم صل على محمد عبدك ورسولك وصل على المؤمنين والمؤمنات والمسلمين والمسلمات

Oh Allah pelekani madalitso anu kwa Muhammad yemwe ndi kapolo komanso Mtumiki wanu, achitireninso chifundo anthu okhulupilira achimuna ndi achikazi komanso asilamu achimuna ndi achikazi.

Kenaka pambuyo pake Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Msilamu amachita ntchito zabwino nthawi zonse ndipo sakhutitsidwa kufikira atamwalira nayo ntchito yabwino imene wakhala akuchita.

Nkhani ya Sayyid Rifaai Rahimahullah

Sayyid Rifaai (Rahimahullah) ndi munthu m’modzi amene ali odziwika bwino pa nkhani ya dini, mchaka cha 555 A.H adanyamuka ulendo opita ku Haji pamapeto pake adapita ku Madinah Munawwarah adakali chiimile pa manda a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adawerenga ndime za ndakatulo iyi.

في حالة البعد روحي كنت أرسلها       تقبل الأرض عني فهي نائبتي

وهذه نوبة الاشباح قد حضرت       فامدد يمينك كي تحظى بها شفتي

  1. Kuchokera kutali mzimu wanga ndakhala ndikuutumiza.                  Ndicholinga choti udzapereke salaam kwa inu.

Apa ndiine ndabwera ndi chithupithupi changa pamaso panu.        Dzanja lanu liyandikitseni kwa ine kuti mlomo wanga upsyopsyone.

Atawerenga ndakatuloyi adaliona dzanja la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) likutuluka pa mtumbira.

Ndipo pamaso pa anthu osachepera 90 000 wina aliyense adadzionera ndi maso ake Sayyid Rifaai akupsyopsyona dzanja la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo mmodzi wa anthu amene adalipowa padalinso Shaikh Abdul Qaadir Jeelani (rahimahullah).

Check Also

Kuwerenga Durood Pamkumano

عن أنس عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: ما من عبدين متحابين في الله …