Kuonjezereka kwa ma riziqi

عن سهل بن سعد رضي الله عنه قال: جاء رجل إلى النبي صلى الله عليه وسلم فشكا إليه الفقر وضيق العيش أو المعاش فقال له رسول الله صلى الله عليه وسلم: إذا دخلت منزلك فسلم إن كان فيه أحد أو لم يكن فيه أحد ثم سلم علي واقرأ قل هو الله أحد مرة واحدة ففعل الرجل فأدَرَّ الله عليه الرزق حتى أفاض على جيرانه وقراباته (أبو موسى المديني وسنده ضعيف كما في القول البديع صـ 279)

Olemekezeka Sa’d (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti tsiku linalake sahabah wina adabwera kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndikudandaula za umphawi komanso kuvutikira kwambiri mmapezedwe amariziqi, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati kwa sahabayu kuti” ukamalowa m’nyumba mwako udzipereka salaam posatengera kuti muli anthu kapena ayi kenako undipemphere madalitso kwa Allah komanso uwerenge aulhuwallahu kamodzi” sahabayu adachita monga adalamulidwira ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo Allah adamdalitsa kwambiri mmapezedwe kufikira kuti adayamba kumawapatsako anthu oyandikana nawo nyumba.

Mahri (Chiongo) A Nabi Aadam (alaihis salaam)

Shaikh Abdul Haqq Dehlawi (rahimahullah) adalemba m’bukhu lake lotchedwa” Madaarijun Nubuwwah” kuti, Hawwa (radhwiyallahu anha) atalengedwa, Aadam (alaihis salaam) adanyamula dzanja lake kuti amugwire. Angelo adati kwa iye, upeze ntima ndikudikira kuti nikah (ndowa) ichitike ndikumpatsa mahri.”

Aadam alaihis salaam adafunsa nati, ndipeleke chani ngati mahri? Angelo adayankha nati, kuwerenga Durood kumuwerengera Nabi (sallallahu alaihi wasallam),” mu hadith ina zimanenedwa kuti, mahri anali kuwerengedwa kwa Durood ka 20 (makumi awiri kumuwerengera Nabi (sallallahu alaih wasallam)). (Fazaail-e-Durood  pg.155)

Check Also

Sawabu zapaderadera ukawerenga Durood ka 100

عن أبي هريرة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال من صلى …