Kupeza nawo chiombolo cha Mtumiki sallallahu alaih wasallam

عن رويفع بن الثابت قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من صلى على محمد وقال: اللهم أنزله المقعد المقرب عندك يوم القيامة، وجبت له شفاعتي (المعجم الكبرى للطبراني، الرقم: 4480 ،وإسناده حسن كما في مجمع الزوائد، الرقم: 17304)

Olemekezeka Ruwaifidh  (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, munthu amene angawelenge Durood iyi chiombolo changa chidzakhala chotsimikizika pa iye.

اَللّٰهُمَّ صَلِّ عَلٰى مُحَمَّدٍ وَأَنْزِلْهُ الْمَقْعَدَ الْمُقَرَّبَ عِنْدَكَ يَوْمَ الْقِيَامَة

Oh Allah mdalitseni Mtumiki wanu Muhammad (sallallahu alaih wasallam) komanso mumpange kukhala wapafupi ndiinu

Zindikirani izi, ma Muhaditheen ena awafotokoza mawu oti chipupi kunena kuti akuimira chiombolo chomwe Allah adzampatse Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) pa tsiku lachiweruzo choti adzakapempha kwa Allah mmalo mwa zolengedwa zonse kuti Allah ayambe kuwerengetsera ntchito zathu. Ndipo ena amanena kuti ndi malo omwe ndi apamwamba jwambiri ku Jannah.

Chikondi chomwe Zaid bin Dhathinah (radhiyallahu anhu) ankamuonetsera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

Makafiri ali pafupi kuti amuphe sahabah Olemekezeka Zaid bin Dhathinah (radhiyallahu anhu) adamufunsa kuti ungasangalale kuti m’malo mwako timuphe Muhammad ndikuti iweyo tikusiye udzikasangalala ndi banja lako?

Yankho lake lodabwitsa lidali loti ndikulumbira mwa Allah sindingalore kuti ine ndikhale ndi banja langa kumasangalala ndipo Muhammad akuvutika ngakhale kutakhala kubaidwa ndi minga,

Atanva zimenezi Abu Sufyaan adayankha kuti “chikondi chimene maswahabah alinacho pa Mtumiki Muhammad (sallallahu alaih wasallam) sichingapezeke kwina kulikonse pa dziki lino lapansi.”

Check Also

Sawabu zapaderadera ukawerenga Durood ka 100

عن أبي هريرة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال من صلى …