Zofunika za Dunya ndi Aakhirah Zikwaniritsidwa chifukwa chowerenga Durood tsiku la Jumuah

عن أنس بن مالك خادم النبي صلى الله عليه وسلم قال: قال النبي صلى الله عليه وسلم: إن أقربكم مني يوم القيامة في كل موطن أكثركم علي صلاة في الدنيا من صلى علي في يوم الجمعة وليلة الجمعة قضى الله له مائة حاجة سبعين من حوائج الآخرة وثلاثين من حوائج الدنيا ثم يوكل الله بذلك ملكا يدخله في قبره كما يدخل عليكم الهدايا يخبرني من صلى علي باسمه ونسبه إلى عشيرته فأثبته عندي في صحيفة بيضاء (شعب الإيمان، الرقم: ٢٧٧٣، وسنده ضعيف كما في القول البديع صـ ٣٢٩)

Hazrat Anas bun Maalik (radhiyallahu ‘anhu) akusimba kuti Hazrat Mtumiki (sallallahu ‘alaihi wasallam) adati: “Iwo mwa inu amene amawerengera duruud kwambiri  mu dunya adzakhala oyandikira kwa ine pa tsiku la Qiyaamah nthawi iliyonse. Munthu amene? Munthu amene angandiwelengere Durood Usiku ndi usana wa lachisanuJumuah, Mulungu adzamkwaniritsilira zosoweka zake kwa zana limodzi, zofunika makumi asanu ndi awiri za Aakhirah ndi zofunika makumi atatu za dunya. Duruud ikatha kuwerengedwa Allah amaipeleka kwa mngelo yemwe adzaibweretse mmanda ndikadzamwalira ngati mmene mphatso imaperekedwera kwa inu, mngelo amandidziwitsa za muntbu amene wapanga duruud dzina lake komanso la bambo ake ndipo kenako ndimaisamala.

Dziwani: Imaam Bayhaqi (rahimahullah) wafotokoza Hadith iyi pansi pa nkhani yokhudza Ambiyaa kuti mmanda ali moyo.

Hazrat Abu Bakr (radhwuyallahu) apereka mkaka kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

Hazrat Abu Bakr Siddeeq (radhiyallahu anhu) akusimba za ulendo wa  hijrah ndi Hazrat Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) motere.

Tinayenda mofulumira usana ndi usiku wonse mpaka dzuwa lidaklipa kwambiri ndikutentha. Kenako ndinapeza mseu wopanda munthu ndipo palibe amene ankayendamo, ndinayang’ana kutsogolo kuti ndione ngati ndingapeze mthunzi uliwonse kuti tibisalemo. Kenako ndinaona phanga limene tidathawirako n’kubisalako chifukwa cha kutentha. Kenako ndinati: “E  Mtumiki wa Allah (sallallahu ‘alaihi wasallam)! Khalani kaye kunja kwa phanga kuno, ndipo ndiloreni ndilowe m’phangamo ndikalongosoremo bwino mwina ndikupezeka nyama  zoopsa ndiye bola chindipweteke ine osati inu.

Nditalowa m’phangamo ndidayamba kukonzamo ndikuyala nsalu yomwe Rasulullah atagonepo. Kenako ndinamupempha kuti alowe ndikupumula ndipo anavomera pempho langa.

Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) anagona kuti apume, ndidapita kuti ndikafufuze ngati ndingapeze aliyense amene akudyetsa ziweto. Kenako ndidamuina m’busa (odyetsa nkhosa)  chapafupi ndipo ndidamufunsa kuti mwini waziwetozo  ndindani. Adatchula dzina la munthu wa ku Makka yemwe ndidamudziwa. (Monga chidali chizolowezi chofalikira pa nthawiyo kuti anthu amalora kuti apaulendo atha kukamako mkaka wankhosa zawo, Hazrat Abu Bakr Siddeeq adapempha mkaka ndipo adakambirana motere:

Hazrat Abu Bakr Siddeeq: “Kodi pali chiweto chomwe chikutulutsa  mkaka?”

M’busa: “eya.”

Hazrat Abu Bakr Siddeeq: “Kodi mungandikamireko?”

Iye adavomera ndipo anandikamira imodzi mwa mbuzizo n’kuthira m’katsuko kanga. Ndidaonjezerako madzi ku mkakawo kuti uzizizilira. Kenako ndidatenga mkakawo kuti ndikaupereke kwa Rasulullah(sallallahu alaih wasallam) . Nditayandikira kwa Rasulullah, ndinamupeza ali mmaso. Ndidati: “imwiniko E, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)”. Kumwa kwa  mkakaku komwe  Mtumiki (sallallahu ‘alaihi wasallam) ankamwa kudabweretsa chisangalalo chachikulu kumtima mwanga.”

Check Also

Sawabu zapaderadera ukawerenga Durood ka 100

عن أبي هريرة رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال من صلى …