Maubwino a Mzikiti

1 Mizikiti imatengedwa kuti ndimalo okondedwa kwambiri pamaso pa Allah.

عن أبي هريرة رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال أحب البلاد إلى الله مساجدها وأبغض البلاد إلى الله أسواقها (صحيح مسلم، الرقم: 671)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (Sallallahu alaih wasallam) adati: “Malo okondedwa kwambiri ndi Allah ndi Mizikiti, ndipo malo odedwa kwambiri ndi Allah ndi misika.”

2 Munthu amene angamange musjid ndicholinga chomusangalatsa Allah, ndiye kuti Allah adzammangira nyumba yachifumu ku Jannah.

عن عبيد الله الخولاني يذكر أنه سمع عثمان بن عفان رضي الله عنه عند قول الناس فيه حين بنى مسجد الرسول صلى الله عليه وسلم إنكم قد أكثرتم وإني سمعت رسول الله صلى الله عليه وسلم يقول من بنى مسجدا لله تعالى قال بكير حسبت أنه قال يبتغي به وجه الله بنى الله له بيتا في الجنة (صحيح مسلم، الرقم: 533) وفي رواية أخرى بني له بيت أوسع منه في الجنة (مسند أحمد، الرقم: 7056)[1]

Ubaydullah Khaulaani (rahimahullah) akufotokoza kuti adamumva Uthman (radhiyallahu anhu) akunena kuti pamene anthu ankatsutsana naye pa nkhani yokulitsa mzikiti wa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) pogwiritsa ntchito mitengo ndi njerwa) “ndithudi anthu inu mwakhala mukunditsutsa kambirimbiri pa nkhani yokulitsa mzikiti, kumachita kuti ndidamumva Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) akunena kuti Munthu amene ndi cholinga chomusangalatsa Allah, Allah adzamumangira nyumba yachifumu ku Jannah.

Malingana ndi hadith ina Munthu amene angamange mzikiti ndi cholinga chofuna kumusangalatsa Allah adapatsidwa nyumba yachifumu ku Jannah yaikulu kuposa Mzikiti omwe adamangawo.


[1] قال المنذري في الترغيب (الرقم: 419): رواه أحمد بإسناد لين لهذا الحديث شاهد من حديث عبد الله بن عمرو قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من بنى لله مسجدا بنى الله له بيتا أوسع منه في الجنة رواه أحمد وفيه الحجاج بن أرطاة وهو متكلم فيه (مجمع الزوائد، الرقم: 1935)

وله شاهد آخر من حديث أبي أمامة قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من بنى لله مسجدا بنى الله له بيتا في الجنة أوسع منه رواه الطبراني في الكبير وفيه علي بن يزيد وهو ضعيف (مجمع الزوائد، الرقم: 1946)

Check Also

Masunnah Ochita Mumzikiti

1. Valani moyenera pamene mukupita kumnzikiti

Allah ta’ala akuyankhula kuti: Oh Inu ana Aadam (alyhi salaam), zikongoleseni (valani zovala zozikongoletsera) pamene mukupemphera swalah munzikiti