Daily Archives: June 2, 2022

Mngelo Amene Amayima pa Manda Odalitsika a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti Apereke Durood ya Ummah kwa Rasulullah Ummah

Sayyiduna Ammaar (radhiyallahu anhu) kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, Allah adasankha mngelo amene amakhala pafupi ndi manda anga kuti adzindifikitsira Durood ya Ummah wanga ndipo adawazindikiritsa maina (ma hadith ena amanena kuti adapatsidwa mphamvu yozindikira mawu a anthu osiyanasiyana) zomwe zikutanthauza kuti palibe munthu amene angandiwelengere Durood tsiku lina lirilonse mpaka pa Qiyaamah pokhapokha mngeloyu amafikitsa kwa ine dzina la munthuyo komanso la bambo ake. (Amanena kuti) uyu ndi uje mwana uje amene wakuwerengerani Durood. 

Read More »