Masunnah Ochita Mumzikiti

6. Werengani maduwa pamene mukupita kumzikiti. Ena mwa maduwawo ndi awa:

Dua yoyamba

Amene angawerenge duwa iyi pamene akunyamuka ulendo wakumzikiti amakhala ndichifundo cha Allah chapadera ndiponso angelo okwanira 70,000 amamuchitiranso maduwa.

اَللّٰهُمَّ إِنِّيْ أَسْأَلُكَ بِحَقِّ السَّائِلِيْنَ عَلَيْكَ وَأَسْأَلُكَ بِحَقِّ مَمْشَايَ هٰذَا فَإِنِّيْ لَمْ أَخْرُجْ أَشَرًا وَلَا بَطَرًا وَلَا رِيَاءً وَلَا سُمْعَةً وَخَرَجْتُ اِتِّقَاءَ سَخَطِكَ وَابْتِغَاءَ مَرْضَاتِكَ فَأَسْأَلُكَ أَنْ تُعِيْذَنِيْ مِنَ النَّارِ وَأَنْ تَغْفِرَ لِيْ ذُنُوْبِيْ إِنَّهُ لَا يَغْفِرُ الذُّنُوْبَ إِلَّا أَنْتَ

O Allah, Ndikukupemphani kudzera mwa amene amadalira mwainu popanga duwa. Ndiponso ndikupempha kwa inu kupyolera mapazi anga, ndithudi sindidatuluke (kupita kumzikiti) kamba kozikweza kapena kunyada kapena kuzionetsera kapenanso kupondereza ena. Ndatuluka chifukwa choopa mkwiyo wanu komanso pofunafuna chisangalaro chanu. Choncho ndikukupemphani kuti munditeteze kumoto wagehena ndiponso mundikhululukire machimo anga ndithu inu nokha ndi amene muli okhululuka machimo.

Dziwani kuti muhadith ina yomwe ikupezeka mubukhu lotchedwa Musnad Ahmad mudanenedwa kuti: Angelo 70,000 amakupangira duwa kuti Allah akukhululukire ndikuti ulandire chifundo cha Allah chapadera mpakana pamene watsirizira swalah.’


 

Check Also

Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama(qurbaani)

1. Qurbaani ndi sunna yomwe ili yaikulu kwambiri komanso ubembedzi wapamwamba kwambiri mu Deen. Mu …