Tembelero la Jibril (alaihis salaam) komanso Mtumiki Muhammad (sallallah alaih wasallam)

عن كعب بن عجرة قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: احضروا المنبر فحضرنا فلما ارتقى درجة قال: آمين فلما ارتقى الدرجة الثانية قال: آمين فلما ارتقى الدرجة الثالثة قال: آمين فلما نزل قلنا: يا رسول الله لقد سمعنا منك اليوم شيئا ما كنا نسمعه قال: إن جبريل عليه الصلاة والسلام عرض لي فقال: بعدا لمن أدرك رمضان فلم يغفر له قلت: آمين فلما رقيت الثانية قال: بعدا لمن ذكرت عنده فلم يصل عليك قلت: آمين فلما رقيت الثالثة قال: بعدا لمن أدرك أبواه الكبر عنده أو أحدهما فلم يدخلاه الجنة قلت: آمين (المستدرك على الصحيحين للحاكم، الرقم: 7256، وقال: هذا حديث صحيح الإسناد ولم يخرجاه وأقره الذهبي)

Hazrat Ka’b bin Ujra (radhiyallahu anhu) akulongosora nkhani iyi: tsiku lina lake Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adaitana maswahabah onse (radhiyallahu anhum) “tabwerani ku mimbar” titakhala moyandikira mimbari, Mtumiki sallallahu alaih wasallam adakwera thanthi (sitepe) yoyamba ndipo anatulutsa mawu onena kuti “Aameen” kenako adakweranso thanthi yachiwiri ndi kuyankhulanso kuti “Aameen” adakweranso yachitatu ndikunena mawu omwe aja onena kuti “Aameen”, atamaliza kupereka Khutbah ndikutsika pa Mimbari paja tidamufunsa kuti, Oh Mthenga wa Allah, takumvani mukuyankhula mawu omwe sitinakumvenipo ndikale lonse mukuyankhula, (komwe ndikuyankhula mawu oti Aameen mpaka katatu pokwera mimbari) “Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, (pomwe ndimakwera thanthi yoyamba ija, Jibril (alaihis salaam) anabwera ndikupanga duwa yoti, tsoka lipite kwa munthu amene mwezi wa Ramadhaan wampeza koma mpaka watha osakhululukidwa machimo ake (sanakwaniritse zochitika za mmwezi umenewu) ndinanena Aameen pa Dua imeneyi, m’mene ndimakwera thanthi yachiwiri ananena kuti tsoka lipite kwa uyo amene walimva dzina lako likutchuridwa koma osakuwerengera duruud, ndinati Aameen kuvomereza duwa imeneyi, ndipo pamene ndimakwera sitepe yachitatu iye anati, tsoka lipite kwa uyo amene makolo ake akalamba iye ali moyo koma (chifukwa chosawatumikira) makolo akewo osakhala njira yokalowera iyeyu ku Jannah, ndinanena kuti Aameen kuvomerezanso duwa imeneyi.

Bilaal (Radhiyallahu anhu) atatsala pang’ono kumwalira

Sayyiduna Bilaal (radhiyallahu anhu) atatsala pang’ono kumwalira mkazi wake adamuuza kuti, “Ah zodandaulitsa kuti ukuchoka pa dziko lapansi.” Sayyiduna Bilaal (radhiyallahu anhu) adayankha nati, kaje kusangalatsa ndikukonderetsa kuti mawa ndikukakumana ndi an zanga, ndikukakumana ndi Muhammad (sallallahu alaih wasallam) komanso omutsatira ake.

Check Also

Kuwerenga Durood ka 100 pa Fajr ndi Maghrib

Olemekezeka Jaabir (radhiyallah anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati "munthu amene angandiwerenge durood ka 100 kungotha kuswali swalah a ya Fajr asadayankhule, Allah adzamukwaniritsira zosowa zake zokwana 100, Allah adzafulumizitsa kukwaniritsa zosowa zake zokwana 30 (padziko pomwe pano) ndiponso Allah adzamusungire kukwaniritsa kwa zosowa zina zokwana 70 ku nkhokwe zake kuti adzampatse pa tsiku lachiweruzo, chimodzi modzinso kwa yemwe angawerenge durood ka 100 kutha kwa swalah ya Maghrib (kutanthauza kuti adzalipidwanso mofanana) "maswahaba (radhiyallahu anhum) adafunsa," tidzikuwerengerani bwanji Durood oh Mthenga wa Allah" Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adawauza maswahabah kuti adziwerenga Durood iyi: