Tafseer Ya Surah ‘Aadiyaat

بِسْمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحْمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

وَٱلْعٰدِيٰتِ ضَبْحًا ‎﴿١﴾‏ فالْمُوْرِيٰتِ قَدْحًا ‎﴿٢﴾‏ فالْمُغِيرٰتِ صُبْحًا ‎﴿٣﴾‏ فَأَثَرْنَ بِهِ نَقْعًا ‎﴿٤﴾‏ فَوَسَطْنَ بِهِ جَمْعًا ‎﴿٥﴾‏ إِنَّ ٱلْإِنسانَ لِرَبِّهِ لَكَنُودٌ ‎﴿٦﴾‏ وَإِنَّهُۥ عَلٰى ذٰلِكَ لَشَهِيدٌ ‎﴿٧﴾‏ وَإِنَّهُۥ لِحُبِّ ٱلْخَيْرِ لَشَدِيدٌ ‎﴿٨﴾‏ أَفَلَا يَعْلَمُ إِذَا بُعْثِرَ مَا فِى ٱلْقُبُورِ ‎﴿٩﴾‏ وَحُصِّلَ مَا فِى ٱلصُّدُورِ ‎﴿١٠﴾‏ إِنَّ رَبَّهُم بِهِمْ يَوْمَئِذٍ لَّخَبِيرُ ‎﴿١١﴾

Ndikulumbilira akavalo othamanga ali ndi phuma, Ndi otulutsa moto ku zikhotwa (pomenyetsa miyendo m’miyala), Ndi othira nkhondo adani m’mawa (dzuwa lisadatuluke), Ndi kuulutsa fumbi lambiri (kwa adani) nthawi imeneyo, Ndikulowelera mkatikati mwa adani. Ndithu munthu ali okanira mbuye wake (sathokoza Allah pa zimene amdalitsa nazo). Ndithudi iye pa zimenezi ndi mboni (yodzichitira yekha kupyolera mzochitachita zake). Ndipo ndithu iye ndi okonda chuma kwambiri (ndiponso ngwansulizo). Kodi sakudziwa zikadzatulutsidwa za mmanda, Ndikudzasonkhanitsidwa ndikuonekera poyera zomwe zidali m’mitima? Ndithu tsiku limenelo Mbuye wawo adzawadziwa kwambiri (ndikuwalongosolera zonse zochita zawo).

Mu surah imeneyi munthu waitanidwa kuti aganize mwakuya m’mene kavalo(hashi) imachitira ndikudzipereka kwake pa lamulo la Mbuye wake, hashi ndi chinyama chomwe chimabvomera lamulo la munthu ndikutsatira mwa mtima onse, ndiyokonzeka kudzipereka pa lumulo lirilonse lomwe mbuye wake ngakhale italamuridwa kuti iyike moyo wake pansi mchigulugulu cha nkhondo, nthawi ina iliyonse ya masana kapena usiku, ngati munthu angachiitane chinyama chidzabvomereza nthawi yomwe mosachedwetsa, pamene akuchikwera ndikumapita ku nkhondo chidzalowa mkatikati mwa adani kuika moyo wake pa chiopsyezo ndicholinga chofuna kutsata lamulo la mbiye wake, chida cha adani sichidzasintha maganizo ake otsatira lamulo la Mbuye wake.

Iyi ndiye levulo ya kukhulupilika ndikuthokoza komwe hashi imaonetsa kwa bwana wake, ngakhale kuti ubwino omwe bwana amachichitira chinyama ndi ochepa kwambiri tikati tiyerekezere ndi momwe ikudziperekera, bwana wake amangofunika ayipatse chakudya, komanso kachisamaliro kochepa chabe, koma hashi imayamika kwambiri kufikira kuti imakhala yokonzeka kupeleka moyo wake.

Kotero uthenga umene Allah akutipatsa mu ndime zimenezi ndi onena kuti, Oh iwe munthu, tadziyang’ana wekha ndiye uwone kuti umamuyamika bwanji mbuye wake, kodi umonetsa kuthokoza kwa mbuye wako monga m’mene chinyamachi chimaonetsera kwa mbuye wake? Ngati chinyama ngati ichi chomwe chili be nzeru zomwe munthu alinazo chikukhala ndi mtima othokoza choterendikukhulupilika, ndi kuyamika kwanji komwe kukuyembekezereka kuchokera mwa iwe komuonetsera Allah Tabaaraka wata’ala, kuzindikira kunena kuti Allah adakudalitsa pokupatsa nzeru komanso ntundu ulionse wa chabwino?

إِنَّ ٱلْإِنسانَ لِرَبِّهِۦ لَكَنُودٌ

Ndithu munthu ali okanira kwa mbuye wake (sathokoza Allah pa zimene amdalitsa nazo).

Aayah imeneyi yandondozana ndi kulumbira kulumbilira zinthu zosiyanasiyana zomwe akavalo amachita akakhala pa nkhondo, phunziro lomwe likuperekedwa ndilonena kuti ngakhale kuti Allah adachigonjetsa chinyama cha mphamvu ngati chimenechi ndikukhala chogonjera munthu, mmalo moti munthu ayamike kwa Allah pa mtendere otelewu omwe ndi ochokera kwa Allah ndikukhala ogonjera malamulo ake monga kavalo amachitira, munthu akupitilirabe kusamuyamika Allah.

Kotero, Mndime imeneyi Allah a kumudandaulira munthu zakusayamike osamuthokoza mbuye wake. Liwu loti ‘kanuud’ limene Allah waligwiritsa ntchito kumulongosora munthu, likutanthauza munthu yemwe nthawi zonse amangokumbukirako zamatsoka ake ndi mavuto omwe amampeza, koma amaiwala mtendere ndi chisangalalo chomwe amakumana nacho, ichi ndiye chikharidwe cha munthu, amasangalala ndi mtendere umene Namalenga wake akumpatsa koma amamuiwala yemwe wampatsa madalitso onsewa. Amasangalala kwambiri mpakana kuiwala kuti China chirichonse chomwe alinacho chikubwera chifukwa cha chifundo cha Allah yemwe ndi wachifundo koposa, mwini kupeleka mtendere. Samaonanso ayi ndipo amaiwala kuti zonsezi adazipeza kudzera mu nzeru zake.

وَإِنَّهُۥ لِحُبِّ ٱلْخَيْرِ لَشَدِيدٌ

Ndipo ndithudi iye ndi okonda chuma kwambiri.

Mndime imeneyi Allah akukalipa kwambiri za chikharidwe chomwe munthu alinacho lokonda kwambiri chuma, kukonda chuma sikuti ndikoletsedwa ayi, koma kuchikondetsetsa chuma ndikukhala ndi mtima ofuna kukhala ndi chuma chambiri ndikumene kuli kolakwika chifukwa kumamupangitsa munthu kusalabadira za malamulo a Allah. Nthawi zina chifukwa chofuna kupeza chuma chambiri siumasiyanitsa njira za kapezedwe ka chuma kuti ndi halaal kapena haraam kapena umatha kusalingalira Kumene pochita zinthu zimene zingabweretse nkwiyo wa Allah.

Kotero tipeza kuti kholo la mavuto onse ndiko kukonda kwambiri chuma, ndi chifukwa chake Allah akunena m’mene tingathetsere mavuto amenewa  ndipo mankhwala ake ndiye kuliganizira kwambiri tsiku lachiweruzo pamene munthu adzafunsidwa ndi Allah.

أَفَلَا يَعْلَمُ إِذَا بُعْثِرَ مَا فِى ٱلْقُبُورِ ‎﴿٩﴾‏ وَحُصِّلَ مَا فِى ٱلصُّدُورِ ‎﴿١٠﴾‏ إِنَّ رَبَّهُم بِهِمْ يَوْمَئِذٍ لَّخَبِيرُ ‎﴿١١﴾

Kodi sakudziwa (zomwe zidzachitike) pamene zonse zomwe ziri pansi pa nthaka zidzatulutsidwe? Ndi zomwe ziri mzidali (m’mitima) za anthu zidzatulutsidwa? Ndithudi tsiku limenelo mbuye wawo adzawadziwa kwambiri(ndikuwalongosolera zomwe ankachita.

Mndime imeneyi Allah akutitengera ku tsiku lachiweruzo, tsiku limeneli china chilichonse chomwe chinabisika chidzabweretsedwa poyera, zomwe ziri mmanda zidzaturutsidwa komanso zomwe zili m’mitima zidzaonekera poyera. Zolinga zonse zomwe munthu anabisa m mu mtima mwake zidzatulutsidwa pa tsiku lachiweruzo. Ngati munthu adachita ntchito inayake yopezetsa sawabu koma ndi cholinga chodzionetsera kwa anthu tsiku limenelo zolinga zake zolakwikazi zidzaonekera poyera pamanso pa anthu.

Check Also

Tafseer Ya Surah Qadr

بِسمِ اللّٰـهِ الرَّحمٰنِ الرَّحيمِ اِنَّا أَنزَلنٰهُ فى لَيْلَةِ القَدْرِ ﴿١﴾ وَما أَدرىٰكَ ما لَيلَةُ القَدرِ ﴿٢﴾ لَيلَةُ القَدرِ خَيرٌ …