Monthly Archives: July 2022

Kuwerenga Durood polowa munzikiti

Olemekezeka Abu Humaid kapena Abu Usaid (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, "pamene munthu a kulowa munzikiti adziwerenga Durood kumfunira zabwino Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo kenako adziwerenga duwa iyi:

Read More »

Masunnah Ochita Mumzikiti

6. Werengani maduwa pamene mukupita kumzikiti. Ena mwa maduwawo ndi awa: Dua yoyamba Amene angawerenge duwa iyi pamene akunyamuka ulendo wakumzikiti amakhala ndichifundo cha Allah chapadera ndiponso angelo okwanira 70,000 amamuchitiranso maduwa.[1] اَللّٰهُمَّ إِنِّيْ أَسْأَلُكَ بِحَقِّ السَّائِلِيْنَ عَلَيْكَ وَأَسْأَلُكَ بِحَقِّ مَمْشَايَ هٰذَا فَإِنِّيْ لَمْ أَخْرُجْ أَشَرًا وَلَا بَطَرًا وَلَا رِيَاءً …

Read More »

Tafseer Ya Surah Qaari’ah

Kugunda kwaphokoso (la qiyaamah). Kodi kugunda kwaphokoso ndichiyani?. Ndichiyani chingakudziwise zakugunda kwaphokoso?. (Kugunda kwaphokoso kudzachitika)Tsiku limene anthu adzakhala ngati agulugufe obalalika. Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya omwazidwa. Tsono munthu amene muyeso wazinthu zabwino udzalemere(ndikupepuka zoipa). Ndiye kuti adzakhala osangalala pa tsiku lachiwerudzo. Ndipo amene muyeso wake wazabwino udzapepuke(ndikulemera zoipa). Ndiye kuti kumalo ake ofikila kudzakhala ku Hawiya(dzenje lamoto wa jahannama). Chingakudziwitse mchiyani zamoto wa Hawiya. Umenewo ndimoto oyaka mwaukali.

Read More »

Kuwerenga Durood polowa munzikiti

Olemekezeka mama Aishah (radhiyallahu anha) akuforokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) akamalowa munzikiti choyambilira ankawerenga Durood ndipo kenako amawerenga dua yotsatirayi:

Rabbigh firlii dhunuubii waftahlii Abuwaaba rahmatika.

Oh Allah, ndikhululukireni machimo anga ndiponso munditsegulire makomo a chifundo chanu.

Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) akamatuluka munzikiti ankawerenga Durood ndipo kenako ankawerenga duwa yotsattirayi:

Read More »

Kuwerenga Durood ka 100 pa Fajr ndi Maghrib

Olemekezeka Jaabir (radhiyallah anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati "munthu amene angandiwerenge durood ka 100 kungotha kuswali swalah a ya Fajr asadayankhule, Allah adzamukwaniritsira zosowa zake zokwana 100, Allah adzafulumizitsa kukwaniritsa zosowa zake zokwana 30 (padziko pomwe pano) ndiponso Allah adzamusungire kukwaniritsa kwa zosowa zina zokwana 70 ku nkhokwe zake kuti adzampatse pa tsiku lachiweruzo, chimodzi modzinso kwa yemwe angawerenge durood ka 100 kutha kwa swalah ya Maghrib (kutanthauza kuti adzalipidwanso mofanana) "maswahaba (radhiyallahu anhum) adafunsa," tidzikuwerengerani bwanji Durood oh Mthenga wa Allah" Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adawauza maswahabah kuti adziwerenga Durood iyi:

Read More »

Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama (qurbaani)

17. Mukuyenera kuigoneka nyama yanu chakumanzere kwanu itayang'ana ku Qiblah.

Olemekezeka Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adazinga ndi manja akenkhosa ziwiri yakuda ndiyoyera komanso zokhala ndi minyanga uku akuwerenga Tasmiyah ndi Takbeer ndipo adaika mwendo wake m'mbali mwake (chinyamacho chidagonekedwa chakumanzere ndicholinga choti chiyang'ane ku Qiblah).

Read More »

Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama (qurbaani)

Olemekezeka Aliyy (radhiyallahu anhu) akusimba kuti tsiku la Idi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamuuza bibi Faatimah (radhiyallahu anha) uchitire umboni pamene chinyama chako chikuzingidwa (uwonelere). Pamene dontho la magazi oyamba likugwa pansi machimo akonso amakhululukidwa, nyama ndi magazi ake zidzaikidwa pasikelo ya ntchito zako zabwino ndikuchulukitsidwa ka 70, Abu Sa'eed khudri (radhiyallahu anhu) adamufunsa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti, Oh Mthenga wa Allah kodi malipilo amenewa adzapelekedwa kwa akubanja lanu lokha chifukwa banja lanu limatchuka ndikukhala ndi madalitso kapena sawabu zimenezi ndi za asilamu onse? Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati zavumbulutsidwa kwa akubanja langa komano sawabu zake ndi za nsilamu wina aliyense.

Read More »