Kuwerenga Durood polowa munzikiti

عن أبي حميد أو أبي أسيد الأنصاري رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم إذا دخل أحدكم المسجد فليسلم على النبي صلى الله عليه وسلم ثم ليقل اللهم افتح لي أبواب رحمتك فإذا خرج فليقل اللهم إني أسألك من فضلك (سنن أبي داود، الرقم: 465، وسكت عليه هو والمنذري في مختصره، الرقم: 465)

Olemekezeka Abu Humaid kapena Abu Usaid (radhiyallahu anhuma) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “pamene munthu a kulowa munzikiti adziwerenga Durood kumfunira zabwino Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo kenako adziwerenga duwa iyi:

اَللّٰهُمَّ افْتَحْ لِيْ أَبْوَابَ رَحْمَتِك

Allahummaftahlii Abuwaaba Rahmatika

Oh Allah nditsegulireni makomo a chifundo chanu

Ndipo akamatuluka adziwerenga Durood kumfunira zabwino Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo kenako adziwerenga duwa iyi:

اَللّٰهُمَّ إِنِّيْ أَسْأَلُكَ مِنْ فَضْلِكَ

Allahumma innii As’aluka min fadhlika.

Oh Allah ndikupempha mtendere wanu.

Hazrat Hakeem bin Hizaam (radhiyallahu anhu) asiya kupempha

Olemekezeka Hakeem bin Hizaam (radhiyallahu anhu) tsiku lina anabwera kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kudzapempha chithandizo, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adampatsa. Anadzabweranso kachikena kuti adzapempheso thandizo ndipo Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adampatsanso China chake.

Atabweranso kachitatu Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adampatsa China chake ndipo adati kwa Iye, “Oh Hakeem! Ndalama ili ndi maonekedwe achinyengo, imaoneka ngati ndiyozuna koma sichoncho. Imakhala ndi madalitso ngati ungaisake ndi mtima okhutira, koma siimakhala ndi madalitso ngati yasakidwa ndi mtima osakhutira (monga kupempha).” Olemekezeka Hakeem (radhiyallahu anhu) adati, Oh Mthenga wa Allah (sallallahu alaih wasallam) sindidzapemphetsanso kwa wina aliyense kuyambira pano.” (Saheeh Bukhari, #1472)

Check Also

Kuwerenga Durood ukadzukira Tahajjud

Olemekezeka Abdullah bin Abbas (radhiyallahu anhuma) adati, Allah amasangalatsidwa ndi anthu awiri, munthu oyamba ndi amene wakumana ndi mdani yemwe ali pa Hashi yake yabwino kwambiri limodzi ndi anzake. Ndikupezeka kuti anzake onse agonja koma iye ndikupitiriza kumenya nkhondo, ngati angamwalire ndiye kuti wamwalira ali Shahid, ngati sangaphedwe ndiye kuti ali mgulu la anthu amene Allah wasangalatsidwa nawo. Munthu wina ndi amene amadzuka usiku kuswali Tahajjud mopanda wina aliyense kuzindikira kuti iyeyu wadzukira Tahajjud, amapanga wudhu wake moyenera ndipo akatero amamutamanda Allah ndikumuyeretsa, komanso amamfunira zabwino Mtumiki (swallallahu alaih wasallam). Ndipo akatero amayamba kuwerenga Quran. Uyu ndiye munthu amene Allah amasangalatsidwa naye, Allah akuyankhula zokhudza munthu amene "Tamuonani kapolo wanga amene akuswali pamene wina aliyense sakumuona kupatula ine".