Hazrat Bilaal (Radhiya Allaahu ‘anhu) pa imfa yake

Pamene Hazrat Bilaal (Radhiya Allaahu ‘anhu) adatsala pang’ono kumwalira, mkazi wake adayamba kunena kuti: “Ha! Ndi zomvetsa chisoni bwanji! Mukuchoka m’dziko lino!”

Hazrat Bilaal (Radhiya Allahu anhu) anayankha kuti: “Zili zokondweretsa ndi zosangalatsa kuti mawa tikukakumana ndi abwenzi athu, tikakumana ndi Muhammad (Swalla Allaahu ‘alayhi wa sallam) ndi maswahaba ake.”

Check Also

Munthu Wabwino Kwambiri pa Ummah uwu

Hazrat Abu Dardaa radhiyallah anhu wanena kuti: “Nthaŵi ina yake, Mtumiki (Swallallaahu alaih wasallam). adandiona …