Aqaaid

Zikhulupiliro Zokhudza Angelo

10. Angelo amene amamufunsa munthu mafunso m’manda maina awo ndi Munkar ndi Nakiir.[1] ndipo mafunso omwe amafunsa ndi awa: a) Mbuye wako ndindani? b) Ungatiuze chani chokhuza Muhammad sallallah alaih wasallam? c) Chipembedzo chako ndi chiti?[2] 11. Mnsilamu aliyense ali ndi M’ngelo komanso shaitaan, M’ngelo amamulimbikitsa munthuyo kuchita zabwino ndipo …

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Angelo

6. Mikaa’eel (alaihis salaam) ndi amene amayang’anira zachakudya ndi nvula, angelo ena amagwira ntchito pansi pake ndipo amayang’anira mitambo nyanja mitsinje ndi mphepo, amauzidwa zoti achite ndi Allah ndipo kenaka amapeleka uthenga kwa angelo ena omwe ali pambuyo pake. 7. Israafeel (alaihis salaam) amalamuridwa ndi Allah kuti achotse mizimu ya …

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Angelo

1. Angelo ndizolengedwa zomwe zilibe tchimo komanso adalengedwa kuchokera mukuwala, angelo samaoneka ndi maso athu, ndipo sii amuna kapena akazi. iwowa samadya kumwa kapena kugona monga amachitira munthu.[1] 2. Allah adawapatsa iwowa maudindo osiyanasiyana, amakwaniritsa lamulo lirilonse limene alamuridwa ndipo samanyozera malamulo a Allah.[2] 3. Sitimadziwa chiwelengero chenicheni cha Angelo …

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Atumiki a Mulungu alaihim Salaam

6. Kuchuluka kwa aneneri onse akudziwa ndi Allah yekha, timakhulupilira mwa atumiki onse angakhale ochuluka bwanji. 7. Monga ziliri kuti ndi chizindikiro cha utumiki, Allah amamulora mtumiki kuchita zodabwitsa zomwe zimatchedwa kuti Mu’ujizaat. Komano Tikuyenera kuzindikira kuti mtumiki ndi munthuso ndipo sangapange zodabwitsa mwa iye yekha, zimangochitika kudzera muchifuniro cha …

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Atumiki a Mulungu (alaihim Salaam)

1. Allah Ta’ala adatumiza atumiki osiyanasiyana kumayiko kuti awatsogolere anthu kunjira yowongoka.[1]  2. Mtumiki ankachita kusankhidwa ndi Allah Ta’ala. Allah Ta’ala ankasankha mwa akapolo ake amene wamufuna pantchito yotamandikayi. Utumiki sungapezeke ndimunthu aliyense kudzera mu ntchito zake ndikulimbikira kwake ayi (koma umachokera kwa Allah Taala).[2]  3. Mtumiki amene adapatsidwa bukhu …

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Mtumiki Wa Allah Muhammad (Sallallah alayhi wasallam)

5. Allah Ta’ala adamudalitsa Mtumiki (sallallah alayhi wasallam) ndi zabwino zapadera zimene Atumiki ndi aneneri a Mulungu sadapatsidwe. Mtumiki (salallah alayhi wasallama) akusimba kuti:

(Ndadalitsidwa ndi zinthu zisanu ndi chimodzi (6), zimene atumiki akale sadapatsidwepo, Ndadalitsidwa popatsidwa jawaamil al kalaam (Mau amodzi koma amatanthauzo ochuluka, mwachitsanzo Quran yolemekezeka komanso mahadith olemekezeka muli matanthauzo akuluakulu kuchokera mu mau ochepa),

 

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Mtumiki Wa Allah Muhammad (Sallallah alayhi wasallam)

1. Mtumiki Muhammad (salallah alayhi wasallam) ndi Mtumiki otsirizira mwa atumiki onse a Allah. Palibenso Mtumiki wina yemwe adzatumizidwe padziko lapansi kudzaongolera anthu ku dziko lirilonse. Ngati wina wake ali ndi chikhulupiliro kuti kudzabwera mtumiki wina pambuyo pa Mtumiki Muhammad (salallah alayhi wasallam) munthu ameneyo ndi Kafiri (simsilamu) ndipo wasemphana …

Read More »

Mmene Allah Taala Amazisamalilira Zolengedwa Zake

1. Allah Taala ndi wachisoni kwambiri kwa akapolo ake. Ndipo Iye Allah amakonda kwambiri akapolo, wodekha kwa akapolo ake komanso opilira kwambiri. Iye amakhululuka machimo ndiponso amalandila kulapa kwa akapolo ake.[1] 2. Allah Taala ndi mwini chilungamo chonse. Iye sapondereza akapolo ake ngakhale mpang´ono pomwe.[2] 3. Allah Taala anamupatsa munthu …

Read More »

Zikhulupiliro zokhudza Allah – 2

6. Palibe chilichonse chofanana ndi Allah Taala mayina ake ndi mbiri zake. Iye ndiokwanilira ulemelero wake ndi mbiri zake, palibe chinachirichonse chofanana ndi Allah Ta'ala mphamvu kapena maonekedwe. Iye Allah Ta'ala alibe maonekedwe kapena mtundu ofanana ndicholengedwa chirichonse.

Read More »