Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo La Chisanu Nchiwiri

18. Mukamaliza wudhu, welengeni shahaadah ngati muli malo otakasuka, popanga shahaadah[1] yang’anani kumwamba, momwemonso werengani duwa iliyonse yomwe imabwera m’mahadith. Ena mwamaduwa a sunnah amene anenedwa m’mahadith oyenera kuwerengedwa pamapeto popanga wudhu ndi awa m’musimu: Duwa yoyamba: Amene angawerenge duwa imeneyi makomo asanu ndi atatu a ku Jannah amatseguka kuti …

Read More »

Kuikonzekera Ramadhan

27. Pangani itikafu (M´bindikiro) masiku khumi otsirizira a mwezi wa Ramadan ngati mungakwanitse kutero.

Olemekezeka Ibn Abbas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adanena zokhudza kukhala mu itikafu kuti: ‘’Munthu amene akupanga itikafu (akubindikira munzikiti) amakhala kutali ndi machimo ndiponso nthawi yomweyo amalandila mphotho za ntchito zomwe akadatha kuzigwira pamene iye asali mu itikaafu.

 

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo Lachisanu Nchimodzi

15. Pangani masah m’makutu mwanu katatu pogwiritsa ntchito madzi atsopano, mukamapanga masah, gwiritsani ntchito chala chankomba phala mukamapaka mkati mwakhutu ndipo chala chachikulu kunja kwake (kuseli kwakhutu). kenako, tengani madzi ena ndikunyowetsa chala chaching’ono kapena chankomba phala ndikupanga m’mabowo a mkhutu ndipo pamapeto pake yendetsani manja anu m’makutu onse.[1] عن …

Read More »

Kukwaniritsidwa Zofuna Za Umoyo Uno Ndi Umoyo Otsiriza

Olemekezeka Habbaan bin Munqiz (Rahimahullah) akusimba kuti Sahaba wina adamufunsa Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) nati "O inu Mtumiki Wa Allah Kodi ndingapereke gawo limodzi m’magawo atatu (one third) a nthawi yanga imene ndiri nayo pokuwerengerani Durood? Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adayankha nati, Inde ngati ungafune kutero, Ndiponso adafunsa nati kodi ndingaononge magawo awiri m’magawo atatu a nthawi yanga pokuwerengerani Durood? Rasulullah (sallallahu alayhi wasallam) adati inde ngati ungafune.Swahabayo adafunsanso nati kodi ndingaonongere nthawi yanga yonse pokuwerengerani durood? Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adayankha nati" Ngati ungachite zimenezi, Allah Ta’ala adzakukwaniritsira chirichonse chomwe ukuchifuna kaya za duniya (dziko lapansi) kapena zaku Aakhirat.

Read More »

Njira Ya Sunnah Yopangira Wudhu Gawo lachisanu

12. Tengani madzi m’manja mwanu ndikutsuka dzanja lanu lamanja mpaka mwakasukusuku katatu. Kenako, tengani madzi m’manja mwanu ndikutsuka dzanja lanu lamanzere mpakana mwakasukusuku katatu. Ndi sunnah pamene mukuyamba kutsuka dzanja lanu kuyambira ku zala kumakwezeka mpaka mwakasukusuku, ngati wina wayambira akasukusuku kumatsika m’musi mpaka ku zala kutsuka kudzalandiridwa, komano zikusemphana ndi njira yasunnah yotsukira dzanja.

Read More »

Kuikonzekera Ramadhan

15. Pamene muli m’mwezi wa Ramadhan yesetsani kupanga ntchito zabwino. Hadith ina ikuti, ntchito ina iliyonse yabwino yomwe ungachite mwakufuna kwako (nafil ibaadah) m’mwezi wa Ramadhan (umalipidwa ndi Allah) ngati wachita chinthu cha faradh (chokakamizidwa kuchita) ndipo ngati wachita ntchito ya farad (yokakamizika kuchita) mumwezi wa Ramadan imaonjezeredwa malipiro ake …

Read More »