Nkhani Yabwino Yochoka Kwa Allah Ta’ala Kwa Awo Amene Amawerenga Durood (Amanfunira Zabwino Nabi (sallallahu alaih aasallam)) Kuchokera M’mahadith

Sayyiduna Abdul Rahman bin Aufi (radhwiyallahu anhu) akunena kuti, tsiku lina Nabi (sallallahu alaih alaihi wasallam) adachoka kunyumba kwake ndipo ndidamulondora, kufikira mpaka adalowa m'munda wa tende nagwetsa nkhope yake pansi. Nabi (sallallahu alaihi wasallam) adakhala pasajdah kwanthawi yaitali mpaka ndidaganiza ngati Allah wachotsa nzimu wake. Kenaka ndidapita pafupi kuti ndikaone chomwe chanchitikira Nabi (sallallahu alaih wasallam). 

Read More »

Kapangidwe Ka Istinja (Kutawasa) Ka Sunnah ~ Gawo Lachinayi

11. Musayankhule pamene mukudzithandiza, pokhapokha patafunikira kuti mulankhule.

Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati, anthu awiri asakadzithandizire malo amodzi komwe akakhale ndikumayankhulana maliseche awo ali pantetete (osavala) ndithudi Allah Ta'ala amadana ndi nchitidwe otelewu.’’

Read More »

Chenjezo Kwa Osasamala Za Ukhondo Akamapanga Istinja (Kutawasa)

Hadith yoyamba

Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati:"Chilango chachikulu (chomwe anthu ambiri amakumana nacho) m'manda ndi chifukwa cha nkodzo (kusasamala nkodzo omwe umadonthekera pathupi komanso unve wina. kotero, wudhu wawo, swalah ndi ibadah ina siidzalandiridwa chifukwa chosowekera ukhondo)"

Read More »