{"id":3399,"date":"2024-12-11T17:11:34","date_gmt":"2024-12-11T15:11:34","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=3399"},"modified":"2024-12-12T06:20:15","modified_gmt":"2024-12-12T04:20:15","slug":"ma-sunnah-komanso-miyambo-ya-dua-7","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=3399","title":{"rendered":"Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 7"},"content":{"rendered":"<p>18. Popempha mpempheni Mulungu kuti akudalitseni ndi aafiyah (ie kuti akudalitseni momasuka m\u2019magawo onse a moyo wanu).<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Abbaas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti: \u201cNthawi ina ndinamufunsa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam): \u201cE, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) wa Allah, ndiphunzitse duwa (yaphindu) imene ndiyenera kupempha kwa Allah. Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anayankha, \u201cPemphani kwa Allah kuti akudalitseni ndi Aafiyah (kumasuka kwakuthupi ndi kwauzimu).\u201d Pambuyo pa masiku angapo, ndinadzanso kwa Mtumiki (Swalla Allaahu \u2018alayhi wasallam) ndipo ndinamufunsa kuti, \u201cE, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) wa Allah ndiphunzitse dua (yaphindu) imene ndiyenera kuipempha kwa Allah. Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anayankha kuti, \u201cE, iwe Abbaas, iwe malume a Mtumiki wa Allah, pempha Allah kuti akudalitseni ndi aafiyah pa dziko lapansi ndi Aakhirah.\u201d<sup class=\"\" style=\"color: #39485f;\">[1]<\/sup><\/em><\/p>\n<p>19. Lekani kudya zinthu zaharamu kapena chakudya chokayikitsa ndikuchita machimo. Kudya haramu ndikuchita machimo kumalepheretsa ma dua kuyankhidwa.<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Olemekezeka Abu Hurairah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: \u201cE inu anthu! Allah walamula Asilamu ndi lamulo lomwe adawapatsa Ambiyaa . (Pankhani ya Ambiyaa(alaihimus salaam), Allah wati: \u201cE inu Atumiki, idyani choyera ndi chabwino, ndipo chitani zinthu zabwino. Ndithudi, ine ndikudziwa zonse zimene mukuchita.\u201d (Kwa okhulupirira) Allah wanena kuti: \u201cE inu okhulupirira, idyani zakudya zoyera ndi zabwino zomwe takupatsani. Pambuyo pake, Rasulullah (Swallallahu alaihi wasallam) adalongosola za chikhalidwe cha munthu amene akuyenda ulendo wautali otopetsa. Tsitsi lake losapesa ndipo zovala zake zakuda ndi fumbi. Amakweza manja ake kumwamba, akulira mopempha nati: \u201cE, Mbuye wanga! Komabe, chakudya chake ndi zakumwa zake ndi zaharaam, zobvala zake zachokera ku Haramu, ndipo thupi lake ladyetsedwa ndi haraam, ndiye ma dua ake angayankhidwe bwanji?\u201d (i.e. Ngakhale ali m\u2019masautso ndi maonekedwe omvetsa chisoni, ma dua ake sangayankhidwe).<sup class=\"\" style=\"color: #39485f;\">[2]<\/sup><\/em><\/p>\n<hr \/>\n<p class=\"\" dir=\"RTL\" style=\"font-family: 'Traditional Arabic'; font-size: 14pt;\">[1] \u0633\u0646\u0646 \u0627\u0644\u062a\u0631\u0645\u0630\u064a\u060c \u0627\u0644\u0631\u0642\u0645: 3514\u060c \u0648\u0642\u0627\u0644: \u0647\u0630\u0627 \u062d\u062f\u064a\u062b \u0635\u062d\u064a\u062d<\/p>\n<p class=\"\" dir=\"RTL\" style=\"font-family: 'Traditional Arabic'; font-size: 14pt;\">[2] \u0635\u062d\u064a\u062d \u0645\u0633\u0644\u0645\u060c \u0627\u0644\u0631\u0642\u0645: 1015<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>18. Popempha mpempheni Mulungu kuti akudalitseni ndi aafiyah (ie kuti akudalitseni momasuka m\u2019magawo onse a moyo wanu). Abbaas (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti: \u201cNthawi ina ndinamufunsa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam): \u201cE, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) wa Allah, ndiphunzitse duwa (yaphindu) imene ndiyenera kupempha kwa Allah. Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anayankha, \u201cPemphani kwa Allah kuti akudalitseni ndi &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":2461,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[26,12],"tags":[],"class_list":["post-3399","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-dua","category-masunna-ndi-aadaab-miyambo"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3399","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=3399"}],"version-history":[{"count":1,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3399\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":3400,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3399\/revisions\/3400"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/2461"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=3399"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=3399"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=3399"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}