{"id":3462,"date":"2025-01-18T17:40:41","date_gmt":"2025-01-18T15:40:41","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=3462"},"modified":"2025-01-18T17:40:41","modified_gmt":"2025-01-18T15:40:41","slug":"zizindkiro-za-qiyaamah-5","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=3462","title":{"rendered":"Zizindkiro za Qiyaamah 5"},"content":{"rendered":"<p><strong>Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah pa nkhani ya Dajjaal<\/strong><\/p>\n<p>Kutulukira komanso kubwera kwa ma fitnah a Dajjaal zimayendera limodzi m\u2019zitaab za Aqaa\u2019id (Zikhulupiriro za Chisilamu). Ma Ulama a Aqaa\u2019id amavomereza kuti kukhulupirira kutulukira kwa Dajjaal ndi gawo la Aqaa\u2019id ya Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah.<\/p>\n<p>Mahadith omwe mkati mwake Mtumiki (Swalla Allaahu \u2018alayhi wasallam) adauchenjezeratu Ummah za ma fitnah a Dajjaal ndi ochuluka, kotero kuti zitaab za a Aqaa\u2019id zonse aphatikiza kukhulupirira pa kubwera kwa Dajjaal kuti zikhale m\u2019gulu la zikhulupiriro za Ahlus Sunnah wal Jamaa&#8217;ah. Choncho, ma Muhadditheen akuluakulu adawaona kuti munthu amene angatsutse za kubwera kwa Dajjaal adzakhala m\u2019gulu la opatuka monga Khawaarij, Mu\u2019tazilah ndi ena otero.<\/p>\n<p>Malinga ndi Allaamah Suyooti (Rahimahullah), ngati munthu angaitsutse hadith yomwe ikutsimikizira kupezeka kwa Dajjaal, adzakhala kafiri. Izi zatsimikizika mu Hadith ya Rasulullah (Swalla Allaahu \u2018alayhi wasallam):<\/p>\n<p class=\"\" dir=\"RTL\" style=\"text-align: center; font-family: 'Traditional Arabic'; font-size: 16pt;\">\u0645\u0646 \u0643\u0630\u0628 \u0628\u0627\u0644\u062f\u062c\u0627\u0644 \u0641\u0642\u062f \u0643\u0641\u0631 \u0648\u0645\u0646 \u0643\u0630\u0628 \u0628\u0627\u0644\u0645\u0647\u062f\u064a \u0641\u0642\u062f \u0643\u0641\u0631<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Amene angatsutse za Dajjaal wachita ukafiri, ndipo amene angatsutse za Mahdi (Radhwiya Allaahu \u2018anhu) wachita ukafiri. (Al-Qowl-ul-Mukhtasar tsamba 16)<\/em><\/p>\n<p>Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah ndikuti Dajjaal ndi Munthu Odziwika.<\/p>\n<p>Ma Muhaddith komanso Fuqaha otchuka, Allaamah Qaadhwi Iyaaz (Rahimahullah), wanena momveka bwino kuti chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah ndikuti Dajjaal ndi munthu wina wake. Allaamah Qaadhi Iyaaz (Rahimahullah) wanena kuti:<\/p>\n<p>Mahadith awa omwe Imaam Muslim (Rahimahullah) adafotokoza za Dajjaal ndi umboni kwa amene ali panjira ya Haq, kutsimikizira kukhalapo kwa Dajjaal ndikuti iye ndi munthu odziwika. Allah Ta\u2019ala adzamtumiza kukhala mayesero kwa akapolo a Allah Ta\u2019ala ndi kumpatsa mphamvu zochitira zinthu zina za uzimu, monga kuukitsa akufa amene adamupha, kutulutsa zinthu zokongora padziko lapansi. ndi kumeretsa nthaka youma yokhala ndi zinthu zabwino, ndi chilango, ndi mitsinje (yomwe azidzaiyendetsa), adzapangitsa chuma cha m\u2019nthaka kumutsatira kulikonse, Kulamula mitambo kuti igwetse mvula, ndi nthaka kuti imeretse mbewu. Zozizwitsa zonsezi zidzaonekera kudzera mu mphamvu ya Allah Ta\u2019ala ndi chilorezo Chake. Pambuyo pake, Allah Ta\u2019ala adzathetsa mphamvu zake zonse, ndipo sadzatha kupha munthu (yemwe adamupha ndi kumuukitsa (monga momwe tafotokozera mu Hadith), kapena munthu wina aliyense. Nabiy Isa (\u2018alaihis salaam) adzamupha ndipo Allah Ta\u2019ala adzadalitsa okhulupirira ndi kupirira pa Dini. Ichi ndi chikhulupiliro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah komanso ma Muhaddithiin onse, ma Fuqahaa ndi ma Ulama a Aqaa\u2019id, mosiyana ndi amene akukanira za Dajjaal monga magulu osokera a Khawaarij, Jahmiyyah ndi ena mwa Mu\u2019tazilah .<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah pa nkhani ya Dajjaal Kutulukira komanso kubwera kwa ma fitnah a Dajjaal zimayendera limodzi m\u2019zitaab za Aqaa\u2019id (Zikhulupiriro za Chisilamu). Ma Ulama a Aqaa\u2019id amavomereza kuti kukhulupirira kutulukira kwa Dajjaal ndi gawo la Aqaa\u2019id ya Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah. Mahadith omwe mkati mwake Mtumiki (Swalla Allaahu \u2018alayhi wasallam) adauchenjezeratu &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":3463,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[28],"tags":[],"class_list":["post-3462","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-zizikiro-za-qiyaamah"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3462","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=3462"}],"version-history":[{"count":1,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3462\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":3464,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3462\/revisions\/3464"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/3463"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=3462"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=3462"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=3462"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}