{"id":3505,"date":"2025-04-20T06:43:01","date_gmt":"2025-04-20T04:43:01","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=3505"},"modified":"2025-05-31T10:49:08","modified_gmt":"2025-05-31T08:49:08","slug":"maonekedwe-a-chithupithupi-cha-dajjaal","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=3505","title":{"rendered":"Maonekedwe a chithupithupi cha Dajjaal"},"content":{"rendered":"<p>M\u2019mahadithi olemekezeka, Olekezeka Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adatsimikizira ummah za Maonekedwe a Dajjaal a umunthu. Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) kufotokoza za Dajjaal m\u2019maonekedwe a munthu zikuonetsa kuti Dajjaal ndi munthu. Pa chifukwa chimenechi, chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah ndi chakuti Dajjaal ndi munthu, ndipo adzabwera pa dziko lapansi nthawi yoikika kuyandikira kwa Qiyaamah ngati chizindikiro chachikulu cha Qiyaamah ku ummah.<\/p>\n<p>M\u2019musimu muli maonekedwe 10 a Dajjaal omwe amatchuridwa mmahadith:<\/p>\n<p><strong>Chinthu Choyamba: Dajjaal kukhala Ndi Tsitsi Lokhala ngati lopotana<\/strong><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, &#8220;Usiku wina, ndidalota ndiri pa Ka&#8217;bah. Ndinapeza munthu wachilendo, amene anali ochititsa chidwi ndikukongora kwake, ndi khungu la mtundu osiyana. Tsitsi lake linali pakati pa mapirikaniro ake ndi mapewa ake atalipesa likutuluka madzi. Adagwira m\u2019mapewa mwa anthu awiri ndipo akuchita tawaaf pa Ka&#8217;bah. Ndinafunsa kuti, \u2018Ndi ndani uyu?\u2019 Iwo anandiuza kuti, \u2018Uyu ndi Maseeh bin Maryam (\u2018alaihis salaam).\u2019 Kenako, ndinawona munthu wina wamfupi komanso ali ndi tsitsi lopiringizana kwambiri. Diso lake lakumanja lidali ndi vuto, ngati gilepu othudzuka. Ndinafunsa kuti, \u2018Ndi ndani uyu?\u2019 Iwo anandiuza kuti, \u2018Uyu ndi Maseeh Dajjaal.\u2019&#8221; (Saheeh Muslim #169)<\/em><\/p>\n<p><strong>Maonejedwe achiwiri: Dajjaal Ali Ndi Maso Olumala<\/strong><\/p>\n<p>Maso onse a Dajjaal adzakhala ndi vuto. Koma, diso limodzi lidzakhala lotsekeka ndi khungu, pamene linalo lidzafanana ndi gilepu othudzuka (monga momwe yafotokozera Hadith).<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) anati, &#8220;Inde, ndikudziwa momwe Dajjaal aliri. Adzakhala ndi mitsinje iwiri imene idzamutsatire kulikonse. Umodzi mwa mitsinje udzakhala ndi madzi abwinobwino, pomwe wina uzidzaoneka ngati moto oyaka mwaukali. Ngati wina angadzapezeke pamenepo, adzapite ku mtsinje omwe adzauone ngati ndi moto ndikudziponya m\u2019menemo. Adzaike mutu wake pansi ndi kumwa madzi ake, popeza madzi ake ndi okoma. Ndithu, diso la Djjaal ndi lotsekeka pamwamba pake pali khungu lokhuthalapakati pa maso ake polembedwa mawu oti \u201ckaafir\u201d omwe okhulupilira wina aliyense adzakwanitsa kuwerenga amatha kuwerenga kaya samatha &#8221; (Saheeh Muslim #2934)<\/em><\/p>\n<p><strong>Maonekedwe achitatu: Dajjaal adzakhala wamfupi, Onenepa ndi wazitho kwambiri.<\/strong><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Mtumiki (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, \u201cNdithudi, Maseeh Dajjaal, ndi wamfupi, zidendeni zake ndizotalikirana ndipo mapazi ake kutsogolo ndiopotokera mkati. Tsitsi lake ndilopotana kwambiri, limodzi mwa maso ake ndilosaona ndipo linalo ndilotong\u00b4oka silotulukamo komanso silolowa mkati, ngati maonekedwe ake angadzakusokonezeni, Ndiye mudziwe kuti Mbuye wanu Allah alibe diso losawona. \u201d (Sunan Abu Dawood #4320)<\/em><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Muhadith ina, Hazrat Tameem Daari (radhwiyallahu \u2018anhu), adamufotokoza Dajjaal ponena kuti, \u201c Kenako, Mwadzidzidzi, ali momwemo (muchigwa cha Wansembe) mudali munthu wamkulu kwambiri muchinyumba ndipo munthu ameneyo sitinamuonepo kalelonse.\u201d (Saheeh Muslim #294)<\/em><\/p>\n<p><strong>Maonekedwe achinayi (4): Mapazi a Dajjaal adzakhala opotokera mkati (i.e. zidendene zake zidzakhala zotayana ndipo kutsogolo kwamapazi ake kudzakhala koyandikana)<\/strong><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Mtumiki (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, \u201cNdithudi, Maseeh Dajjaal, ndimunthu wamfupi, zindeneni zake ndi zotayana ndipo kutsogolo kwa mapazi ake ndiopotokera mkati.\u201d (Sunan Abu Dawood #4320)<\/em><\/p>\n<p><strong>Maonekedwe achisanu (5): Dajjaal adzakhala ndi tsitsi lochuluka komanso lothothana.<\/strong><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Mtumiki (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, \u201cDiso lakumanzere la Dajjaal ndilosaona ndipo tsitsi lake ndi lochuluka komanso lothothana. Ndipo azidzayenda ndi Jannah komanso Gehena. Gehena yake choonadi chake idzakhala Jannah ndipo Jannah yake choonadi chake idzakhala Gehena.\u201d (Saheeh Muslim #2934)<\/em><\/p>\n<p><strong>Maonekedwe achisanu ndi chimodzimodzi (6): Dajjaal adzakhala ndi chipumi chotambasuka.<\/strong><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Mtumiki (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, \u201cChoncho Maseeh Osocheretsayo, Ndi munthu amene chipumi chake ndi chotambasuka, Diso lake lakumanzere mlosaona ndipo gawo lapansi pakhosi pake ndi lalikulu. Ndipo. Ndipo ndichimodzimodzi ndi Abdul Uzza bin Qatan.\u201d (Majma\u2019uz Zawaa\u2019id #12539)<\/em><\/p>\n<p><strong>Maonekedwe achisanu ndichiwiri: Dajjaal sadzakhala ndi ana.<\/strong><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Hadith yomwe ikupezeka mu swahihi Muslim ikulongosora kuti, \u201cKodi Rasulu- Allah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) sananene kuti Dajjaal adzakhala osabereka komanso sadzakahala ndi ana?\u201d (Saheeh Muslim #2927)<\/em><\/p>\n<p><strong>Maonekedwe achisanu ndi chitatu (8): Dajjaal ndi oyera khungu<\/strong><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Mtumiki (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adafunsidwa zokhuza Dajjaal ndipo anayankha nati, \u201cNdikuona kuti iye adzakhala okandapala ndiwazitho komanso oyera khungu. Diso lake limodzi ndi lotulukamo ngati nyenyezi yowala. Tsitsi lake ngati nthambi zamtengo.\u201d (Musnad-e-Ahmed #3546)<\/em><\/p>\n<p><strong>Maonekedwe achisanu ndi chinayi (9): Mau oti \u201cKaafir\u201d adzalembedwa pakati pamaso a Dajjaal<\/strong><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Mtumiki (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati mau oti , \u201c kaafir adzalembedwa pakati pamaso ake awiri, Munthu okhulupilila wina aliyense adzakwanitsa kuwerenga mawuwo kaya ndiodziwa kuwerenga ngakhale osadziwa kuwerenga\u201d (Saheeh Muslim #2934)<\/em><\/p>\n<p><strong>Maonekedwe a khumi: Kufanana ndi kaafir, Abdul Uzza bin Qatan<\/strong><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Rasulullah (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wasallam) adati: \u201cIne ndikumufanizira (Dajjaal) ndi Abdul Uzza bin Qatan.\u201d (Saheeh Muslim #2937)<\/em><\/p>\n<p>Kuchokera m&#8217;mahadith omwe tatchulayi omwe ali afotokoza maonekedwe khumi a Dajjaal, tikumvetsa kuti Dajjaal ndi munthu. Akadakhala kuti Dajjaal ndi ziwanda, kapena osakanikirana pakati pa munthu ndi ziwanda, kapena dongosolo lapadziko lapansi, Mtumiki (Swalla Allaahu \u2018alayhi wasallam) sakadamufotokoza mwa maonekedwe a umunthu wake.<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>M\u2019mahadithi olemekezeka, Olekezeka Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adatsimikizira ummah za Maonekedwe a Dajjaal a umunthu. Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) kufotokoza za Dajjaal m\u2019maonekedwe a munthu zikuonetsa kuti Dajjaal ndi munthu. Pa chifukwa chimenechi, chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah ndi chakuti Dajjaal ndi munthu, ndipo adzabwera pa dziko lapansi nthawi yoikika kuyandikira kwa Qiyaamah ngati &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":3404,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[28],"tags":[],"class_list":["post-3505","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-zizikiro-za-qiyaamah"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3505","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=3505"}],"version-history":[{"count":5,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3505\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":3575,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3505\/revisions\/3575"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/3404"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=3505"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=3505"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=3505"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}