{"id":3929,"date":"2026-01-10T18:21:14","date_gmt":"2026-01-10T16:21:14","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=3929"},"modified":"2026-01-11T06:22:40","modified_gmt":"2026-01-11T04:22:40","slug":"nabi-isah-alaihis-salaaam","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=3929","title":{"rendered":"Nabi Isah &#8216;alaihis salaaam"},"content":{"rendered":"<p>Isa (\u2018alaihis salaam) ndi Mtumiki wa Allah Ta\u2018ala ndipo ali m&#8217;gulu la Aneneri apamwamba. Allah Ta\u2018ala adamuvumbulutsira Injeel (Baibulo) ndipo adamudaritsa ndi Shari\u2019ah. Iye ndi Nabi amene anatumizidwa padziko lapansi Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) asanabwere.<\/p>\n<p>Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, \u201cAmbiyaa onse (\u2018alaihimus salaam) ali ngati ana a bambo m&#8217;modzi. Amayi awo ndi osiyana, ndipo deen yawo ndi imodzi (onse amakhulupirira tauhiid &#8211; umodzi wa Allah, ngakhale kuti Shari\u2019ah zawo ndi zosiyana). Ine ndine munthu wapafupi kwambiri ndi Nabi Isa bin Maryam (\u2018alaihis salaam) chifukwa palibe Nabi wina pakati pathu. Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) adzatsika ndithu.\u201d (Musnad Ahmed #9270)<\/p>\n<p>Allah Ta\u2018ala anamutumiza Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) kwa Bani Israa\u2019eel, koma iwo sanamukhulupirire ndipo anamukana. Anayesera kumupha, koma Allah Ta\u2018ala adamuteteza ndikumukweza kumwamba ali wamoyo. Pakadali pano, Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) ali moyo kumwamba, ndipo Qiyaamah ikamadzayandikira, Allah Ta\u2018ala adzamutsitsa kubwera padziko lapansi.<\/p>\n<p>Mu Hadith yolemekezeka, Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, \u201cNdikulumbira Mwa amene moyo wanga uli m\u2019manja mwake! Nthawi yayandikira kwambiri (Qiyaamah) pamene mwana wa Maryam (Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) adzatsika kuchokera kumwamba, ndipo adzalamulira pakati panu ngati mtsogoleri olungama. Adzaphwanya mtanda ndikupha nkhumba\u2026\u201d\u00a0(Sahiih Muslim #155)<\/p>\n<p><strong>Kutsika kwa Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) \u2013 Chizindikiro Chachikulu cha Qiyaamah<\/strong><\/p>\n<p>Kutsika kwa Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) kuchokera kumwamba kubwera padziko lapansi kumaikidwa mgulu la zizindikiro zikuluzikulu za Qiyaamah.<\/p>\n<p>Mu Qur\u2019aan Yolemekezeka, Allah Ta\u2018ala akuti, \u201cNdipo ndithudi iye (Nabi Isa [alaihis salaam]) ndi chimodzi mwa zizindikiro za Qiyaamah, choncho musakhale ndi kukaikira kulikonse pa kutha kwa dziko (kubwera kwa Qiyaamah)\u2026 (Surah Zukhruf v. 61)<\/p>\n<p>Mu Hadith ina, Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adanena kuti, \u201cZoonadi, Qiyaamah sidzachitika kufikira mutaona zizindikiro khumi zikuluzikulu zikuchitika. Utsi (mtundu wa nthunzi kapena utsi omwe udzatsike padziko lapansi kuchokera kumwamba Qiyaamah isanafike,ndi pomwe Asilamu adzagwidwe ndi chimfine ndipo ma kuffaar adzakomoka), kutuluka kwa Dajjaal, kutuluka kwa chilombo, kutuluka kwa dzuwa kuchokera kumadzulo, kutsika kwa Nabi Isa (\u2018alaihis salaam), kubwera kwa Ya\u2019juuj ndi Ma\u2019juuj, kumira kwa nthaka kokwana katatu, Kumira kum&#8217;mawa, kumira kumadzulo ndi kumira ku Arabian Peninsula. Chizindikiro chomaliza chidzakhala moto omwe udzabuke ku Yemen ndikukusira anthu onse kupita ku bwalo la mahshar (Syria).\u201d (Saheeh Muslim #2901)<\/p>\n<p>Chikhulupiriro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah ponena za Nabiy Isa (\u2018alaihis salaam) Kupha Dajjaal.<\/p>\n<p><strong>Chikhulupiliro cha Ahlus Sunnah wal Jamaa chokhudza Isa &#8216;alaihis salaam kupha Dajjaal.<\/strong><\/p>\n<p>Chimodzi mwa zifukwa zimene adzatumizidwire Isa &#8216;alaihis salaam ku dziko lapansi qiyaama isadafike ndi kudzapha Dajjaal. Isa &#8216;alaihis salaam kupha Dajjaal ndi zina mwa zikhulupiriro zikuluzikulu za Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah.<\/p>\n<p>Allaamah Qadhi Iyaadh (rahimahullah) wafotokoza kuti Nabiy Isa (\u2018alaihis salaam) kubwereranso padziko lapansi kudzapha Dajjaal ndi zina mwa zikhulupiriro zikuluzikulu za Ahlus Sunnah wal Jamaa\u2019ah. Ma Muhadditheen, Fuqahaa ndi Ulamaa a Aqaa\u2019id onse amavomereza chikhulupiriro ichi.<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Isa (\u2018alaihis salaam) ndi Mtumiki wa Allah Ta\u2018ala ndipo ali m&#8217;gulu la Aneneri apamwamba. Allah Ta\u2018ala adamuvumbulutsira Injeel (Baibulo) ndipo adamudaritsa ndi Shari\u2019ah. Iye ndi Nabi amene anatumizidwa padziko lapansi Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) asanabwere. Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, \u201cAmbiyaa onse (\u2018alaihimus salaam) ali ngati ana a bambo m&#8217;modzi. Amayi awo ndi osiyana, ndipo &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":3404,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[28],"tags":[],"class_list":["post-3929","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-zizikiro-za-qiyaamah"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3929","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=3929"}],"version-history":[{"count":1,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3929\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":3930,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3929\/revisions\/3930"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/3404"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=3929"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=3929"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=3929"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}