{"id":3967,"date":"2026-01-24T12:51:43","date_gmt":"2026-01-24T10:51:43","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=3967"},"modified":"2026-01-24T22:41:01","modified_gmt":"2026-01-24T20:41:01","slug":"momwe-adabadwira-nabi-isa-alaihis-salaam","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=3967","title":{"rendered":"Momwe Adabadwira Nabi Isa (\u2018alaihis salaam)"},"content":{"rendered":"<p>Dongosolo la Allah Ta\u2018ala, kukamba momwe amalengedwera anthu, ndilakuti anthu awiri akakumana munthu amapangidwa. Chinthu choyamba ndi kudzera mwa makolo omwe mbewu ya mwamuna imabzalidwa m&#8217;mimba mwa mayi. Chinthu chachiwiri ndi mzimu omwe umalowa m&#8217;mimba mwa mwana yemwe sanabadweyo akakwanitsa miyezi inayi.<\/p>\n<p>Munthu aliyense amene anabwera padziko lapansi adatsatira njira imeneyi. Komabe, Allah Ta\u2018ala adapanga kapezekedwe ka anthu atatu kukhala kosiyana ndi ndondomekoyi ngati Nabi Aadam, Hawwaa, ndi Nabi Isa (\u2018alaihimus salaam).<\/p>\n<p>Kukamba za Nabi Aadam (\u2018alaihis salaam), Allah Ta\u2018ala adalenga thupi lake kuchokera ku dothi kenako n\u2019kumuuzira. Ichi ndi chifukwa chake iye anabadwa popanda makolo.<\/p>\n<p>Kukamba za Hawwaa (\u2018alaihas salaam), Allah Ta\u2019ala adamulenga kuchokera ku nthiti yakumanzere ya Nabi Aadam (\u2018alaihis salaam). Choncho, anabadwa kudzera mwa munthu m&#8217;modzi yekha.<\/p>\n<p>Kunena za Nabi Isa (\u2018alaihis salaam), Allah Ta\u2018ala adamulenga popangitsa mzimu kulowa m&#8217;mimba mwa amayi ake. Choncho, anabadwa kudzera mwa munthu m&#8217;modzi yekha.<\/p>\n<p>Mu Qur&#8217;aan Yolemekezeka, Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) adayerekezedwa ndi Aadam (\u2018alaihis salaam). Allah Ta\u2019ala akuti:<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Ndithudi, chitsanzo cha Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) kwa Allah chikufanana ndi cha Nabi Aadam (\u2018alaihis salaam). Allah Ta\u2018ala adamulenga (Nabi Aadam [\u2018alaihis salaam]) kuchokera ku dothi, kenako nati kwa iye (chidaumbidwa kuchokera ku dothicho), \u201cKhala!\u201d ndipo anakhala.\u201d (Surah Aal-e-Imraan v. 59)<\/em><\/p>\n<p>Mu ayah iyi, Allah Ta\u2018ala akufotokoza kuti kulengedwa kwa Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) kunali kofanana ndi kulengedwa kwa Nabi Aadam (\u2018alaihis salaam) poyang&#8217;ana kuti Nabi Aadam (\u2018alaihis salaam) sanabadwe kudzera mwa makolo, koma analengedwa ndi mzimu omwe unalowetsedwa mwa iye.<\/p>\n<p>chimodzimodzinso, Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) sanabadwe kudzera mwa bambo, koma ruuh kulowetsedwa m&#8217;mimba mwa amayi ake, zomwe zinamupangitsa kukhala munthu.<\/p>\n<p>Ndi chifukwa chake tikupeza kuti monga momwe Nabi Aadam (\u2018alaihis salaam) adalengedwera ndi Hawwaa (\u2018alaihas salaam) ndi mozizwitsa, momwemonso kulengedwa kwa Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) kunali kodabwitsa komanso kopatulika.<\/p>\n<p><strong>Zozizwitsa Za Nabi Isa (\u2018alaihis salaam)<\/strong><\/p>\n<p>Allah Ta\u2018ala adamudalitsa Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) ndi mphamvu yochita zodabwitsa zambiri. Chozizwitsa chilichonse chomwe adachita chinachitika ndi chilolezo cha Allah Ta\u2018ala, ndipo kudzera mwa Allah Ta\u2018ala adamupatsa kuthekera ndi mphamvu zotha kuchichita.<\/p>\n<p>Zina mwa zozizwitsa zomwe adachita, monga momwe zanenedwera mu Qur\u2019aan Majiid, ndichakuti adachiritsa akhate ndi omwe anabadwa akhungu. Ankaumba mbalame kuchokera ku dothi kenako nkuziuzira mpweya, ndipo Allah Ta\u2018ala ankazipatsa moyo.<\/p>\n<p><strong>Allah Ta\u2018ala Amunyamura Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) Kupita Kumwamba<\/strong><\/p>\n<p>Kukamba za Nabi Isa (\u2018alaihis salaam), Akristu amakhulupirira kuti adapachikidwa pamtanda ndipo adaphedwa ndi Ayuda. Komabe, chikhulupiriro ichi ndi chabodza ndipo chatsutsidwa momveka bwino mu Qur\u2019aan Majiid.<\/p>\n<p>Chiphunzitso cha Chisilamu ndichakuti Ayuda sanamuphe, koma Allah Ta\u2018ala anamupulumutsa ku mavuto awo ndipo anamunyamura kupita kumwamba mozizwitsa. Allah Ta\u2018ala akufotokoza momveka bwino izi mu Qur\u2019aan Majiid. Allah Ta\u2018ala akuti,<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>\u201cNdipo iwo (Ayuda) sanamuphe, kapena kumupachika; koma adapombonezedwa ndi munthu wina. iwo amene akutsutsana za izi ndithudi ali mu chikaiko pa zimenezi, alibe uzindikiri ulionse otsimikizika ndipo amangotsatira maganizo awo, ndithudi zoona zake ndi zakuti iwo sadamuphe, koma kuti Allah adamunyamura kupita kwa iye, Allah ndiye mwini ulemelero mwini kuzindikira mwakuya.<\/em><br \/>\n(Surah Nisaa v. 157-158)<\/p>\n<p>Kuchokera pamwambapa, taona kuti moyo wa Nabi Isa (\u2018alaihis salaam\u2019) ndi chizindikiro chachikulu choonekera bwino cha Qudrat (mphamvu) ya Allah Ta\u2019ala. Kuyambira momwe anabadwira ndi zozizwitsa zomwe adachita mpaka pomwe Allah Ta\u2018ala adamunyamulira kupita kumwamba &#8211; zonse zikuonetsa mphamvu ya Allah Ta\u2018ala.<\/p>\n<p>Dajjaal akadzabwera padziko lapansi, adzakhala akupanga ma fitnah akuluakulu komanso zoipa zambiri padziko lapansi. Fitnah yake, monga momwe yatchulidwira mu Hadith, idzakhala fitnah yaikulu kwambiri yomwe dziko lapansi lidzakumane nayo kuyambira pamene dzikoli lidalengedwa. Panthawi yofunikira kwambiri ngati imeneyo, adzakhala Nabi ameneyu wa Allah Ta\u2018ala olemekezeka\u00a0 &#8211; Nabi Isa (\u2018alaihis salaam), yemwe ndi chizindikiro cha Qudrat ya Allah Ta\u2018ala, yemwe adzatumizidwe ndi Allah kudziko lapansi kuti adzapulumutse Ummah wa Rasulullah (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wa sallam) pomupha Dajjaal, amenewo adzakhala mathero a zoipa zake zonse.<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Dongosolo la Allah Ta\u2018ala, kukamba momwe amalengedwera anthu, ndilakuti anthu awiri akakumana munthu amapangidwa. Chinthu choyamba ndi kudzera mwa makolo omwe mbewu ya mwamuna imabzalidwa m&#8217;mimba mwa mayi. Chinthu chachiwiri ndi mzimu omwe umalowa m&#8217;mimba mwa mwana yemwe sanabadweyo akakwanitsa miyezi inayi. Munthu aliyense amene anabwera padziko lapansi adatsatira njira imeneyi. Komabe, Allah Ta\u2018ala adapanga &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":3463,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[28],"tags":[],"class_list":["post-3967","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-zizikiro-za-qiyaamah"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3967","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=3967"}],"version-history":[{"count":4,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3967\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":3970,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/3967\/revisions\/3970"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/3463"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=3967"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=3967"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=3967"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}