{"id":4020,"date":"2026-04-11T16:36:43","date_gmt":"2026-04-11T14:36:43","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4020"},"modified":"2026-04-11T16:42:45","modified_gmt":"2026-04-11T14:42:45","slug":"moyo-wa-nabi-issah-alaihis-salaam-akadzabweranso-padziko-lapansi-ndi-kuchuluka-kwa-madalitso-ndi-chitetezo-mnthawi-yake","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4020","title":{"rendered":"Moyo Wa Nabi Issah Alaihis Salaam Akadzabweranso Padziko Lapansi Ndi Kuchuluka Kwa Madalitso Ndi Chitetezo Mnthawi Yake"},"content":{"rendered":"<p>Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) akadzabwerera padziko lapansi, Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) adzakhala mtsogoleri otsogolera Asilamu. Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) adzauza Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) kuti atsogolere Asilamu, popeza iye ndi Nabi wa Allah Ta\u2018ala. (Ibnu Hibbaan #6812, Fitan li-Nu\u2019aim #1028)<\/p>\n<p>Asilikali achisilamu, motsogozedwa ndi Nabi Isa (\u2018alaihis salaam), adzamenyana ndi Dajjaal komanso asilikali ake. Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) adzamupha Dajjaal ndipo Asilamu adzapambana pankhondoyi.<\/p>\n<p>Posakhalitsa Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) adzamwalira ndipo Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) adzatsogolera kuswalira maliro ake. Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) adzapitiliza kukhala mu Ummah, kutsatira Chisilamu ndi kutsogolera anthu ku Chisilamu. Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) adzakwatira ndikukhala ndi ana.<\/p>\n<p>Pakadzapita kanthawi, Allah Ta\u2018ala adzamasula Ya\u2019jooj ndi Ma\u2019jooj padziko lapansi. Adzayambitsa chisokonezo ndi chiwonongeko padziko lonse lapansi kulikonse komwe akupita. Pambuyo pake, Allah Ta\u2018ala adzawapatsa tsoka lomwe lidzawapangitse onse kumwalira.<\/p>\n<p>Ya\u2019jooj ndi Ma\u2019jooj akadzaonongedwa ndi Allah Ta\u2018ala, Allah Ta\u2018ala adzagwetsa mvula yambiri, zomwe zidzapangitsa kuti mbewu zidzamere zambiri ndi nyama kuchulukana. Anthu padziko lapansi adzadalitsidwa ndi barakah yayikulu panthawiyo. Chifukwa cha barakah, kuchuluka kwa zipatso ndi mbewu kudzawonjezekanso. Padzakhalanso chitetezo chokwanira, mpaka kufika poti anthu sadzaopa kuvulazidwa ndi nyama zakuthengo komanso zapoizoni. Kusagwirizana ndi ndewu zidzathanso chifukwa udani ndi chidani zidzachoka m&#8217;mitima ya anthu.<\/p>\n<p>Rasulullah (Sallallahu \u2018alaihi wasallam) anati:<\/p>\n<p>Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) adzakhalabe mu ummah wanga ngati mtsogoleri olungama komanso mtsogoleri wachilungamo. Adzaswa mtanda, kupha nkhumba ndikuthetsa jizyah (msonkho omwe umaperekedwa kwa nzika zachikunja m&#8217;dziko lachisilamu siudzaperekedwanso chifukwa aliyense adzakhala kuti ndi msilamu). Zakaat sidzatengedwanso chifukwa aliyense adzakhala ndi chuma chokwanira, kotero palibe osonkhanitsa zakaat amene adzatumizidwe kukatenga mbuzi kapena ngamila. udani pakati pa wina ndi mnzake zidzathetsedwa padziko lapansi. Kuluma (ndi kuvulaza) kudzachotsedwa pa nyama iliyonse yomwe imaluma (kapena kuvulaza), mpaka mwana wamng&#8217;ono ataika dzanja lake mkamwa mwa njoka popanda kumuvulaza, ndipo mtsikana wamng&#8217;ono adzathamangitsa mkango ndipo siudzamuvulaza, ndipo mmbulu udzapezeka pamaso pa mbuzi. Dziko lapansi lidzadzazidwa ndi mtendere, monga momwe chidebe chimadzazidwira ndi madzi. Padzakhala mgwirizano wathunthu popeza Allah Ta\u2018ala yekha ndiye adzalambiridwa. Nkhondo idzatha ndipo Maquraish adzayambanso utsogoleri. Dziko lapansi lidzakhala ngati mbale yasiliva, yobereka mbewu monga momwe zidalili mu nthawi ya Nabi Aadam (\u2018alaihis salaam), mpaka gulu lonse la anthu lidzadya kuchokera ku mtolo umodzi wa mphesa ndikukhuta, ndipo gulu lonse la anthu lidzadya kuchokera ku makangaza amodzi ndikukhuta. (Sunan Ibnu Maajah #4077)<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) akadzabwerera padziko lapansi, Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) adzakhala mtsogoleri otsogolera Asilamu. Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) adzauza Nabi Isa (\u2018alaihis salaam) kuti atsogolere Asilamu, popeza iye ndi Nabi wa Allah Ta\u2018ala. (Ibnu Hibbaan #6812, Fitan li-Nu\u2019aim #1028) Asilikali achisilamu, motsogozedwa ndi Nabi Isa (\u2018alaihis salaam), adzamenyana ndi Dajjaal komanso asilikali ake. Nabi Isa (\u2018alaihis &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":3276,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[28],"tags":[],"class_list":["post-4020","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-zizikiro-za-qiyaamah"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4020","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=4020"}],"version-history":[{"count":1,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4020\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":4021,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4020\/revisions\/4021"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/3276"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=4020"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=4020"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=4020"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}