{"id":4041,"date":"2026-04-25T16:12:20","date_gmt":"2026-04-25T14:12:20","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4041"},"modified":"2026-04-25T16:13:29","modified_gmt":"2026-04-25T14:13:29","slug":"kuwonekera-kwa-nkhani-zikuluzikulu-mahdi-asanafike-zizindikiro-za-qiyaamah","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4041","title":{"rendered":"Kuwonekera kwa Nkhani Zikuluzikulu Mahdi Asanafike &#8211; Zizindikiro za Qiyaamah"},"content":{"rendered":"<p>Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) asanaonekere padziko lapansi, anthu ambiri padziko lonse lapansi adzakhala Akhristu. (Muslim #2898) M&#8217;madera ambiri padziko lapansi, Ummah wa Chisilamu udzakhala ukuvutika ndipo udzazunzidwa ndi kuvutitsidwa ndi makafiri. Nkhondo zambiri zidzabuka ndipo Asilamu padziko lonse lapansi adzakhala akuyembekezera mwachidwi kubwera kwa Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) kuti awathandize.<\/p>\n<p>Panthawiyo, Sufyaani (munthu ochokera ku banja la Abu Sufyaan [radhiyallahu \u2018anhu]) adzakhala ndi mphamvu mu Syria. (Haakim #8586) Adzakhala munthu oipa ndipo adzakhala akusaka Asayyid (mbadwa za kubanja la Rasulullah [swallallahu \u2018alaihi wasallam]) ndipo adzawapha kulikonse komwe angawapeze. (Al-Fitan li-Nu\u2019aim #923)<\/p>\n<p>Adzatumiza asilikali ake ku Kufah ndi Madinah Munawwarah, ndipo adzayambitsa chisokonezo ndi kukhetsa mwazi m&#8217;mizinda imeneyi. (Ishaa\u2019ah tsamba 203) Asilamu adzakhala akufunafuna Mahdi (radhwiyallahu \u2018anhu) kuti kudzera mu utsogoleri wake ndi chitsogozo chake, athe kuthana ndi mavuto awo. (Al-Fitan li-Nu\u2019aim #868)<\/p>\n<p>Mahdi (radhwiyallahu \u2018anhu) adzakakhala ku Madinah Munawwarah, ndipo chifukwa choopa kuti anthu angamusankhe kukhala mtsogoleri, adzachoka ku Madinah Munawwarah kupita ku Makkah Mukarramah. (Mirqaat 8\/3440) Malinga ndi malipoti ena, adzathawira ku Makkah Mukarramah kulithawa gulu lankhondo la Sufyaani lomwe lidzidzapha ma Sayyid. (Al-Fitan li-Nu\u2019aim #923, 924)<\/p>\n<p>M&#8217;nkhani zina, zatchuridwa kuti Mahdi asanabwere, mtsogoleri wa Chisilamu adzamwalira ndipo padzakhala mkangano waukulu pakati pa Asilamu pankhani ya munthu amene ayenera kusankhidwa kukhala mtsogoleri otsatira.<\/p>\n<p>Mahdi akadzakhala ku Makkah Mukarramah, m&#8217;madera a Musjid-ul-Haraam pa malo a pakati pa Hajr-e-Aswad ndi Maqaam-e-Ebrahim. anthu owopa Allah Ta\u2019ala adzamuzindikira kuti ndi Mahdi, ndipo kenako adzalonjeza pamasovpake kukhulupirika. (Abu Dawood #4286)<\/p>\n<p><strong>Gulu Lankhondo Limira Pansi<\/strong><\/p>\n<p>Sufyaani akadzamva za kubuka kwa Mahdi (radhwiyallahu \u2018anhu), yemwe ndi waku banja la Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam), adzatumiza gulu lake lankhondo kuti likamuukire.<\/p>\n<p>Gululi likadzafika ku Baidaa (dera lomwe lili kunja kwa Madinah Munawwarah), lidzaima paphiri kuti lipumule. Koma akadzafika paphirili, asilikali onse adzamira pansi ndipo adzawonongedwa. Munthu m&#8217;modzi yekha ndiye adzapulumuke mgululi ndipo adzapita kwa anthu ndikuwadziwitsa zomwe zachitika.<\/p>\n<p>Bibi Hafsah (radhwiyallahu \u2018anha) akunena kuti anamva Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) akunena kuti, \u201cGulu lankhondo lidzapita ku nyumba iyi ( Ka\u2019bah Shareef) kuti akamenye nkhondo, mpaka atafika ku Baidaa komwe gawo lapakati la gulu lawo lankhondo lidzamira pansi. Gawo lakutsogolo lidzaitana gawo lakumbuyo, pambuyo pake onse adzamira pansi. Munthu m&#8217;modzi yekha ndiye adzapulumuke amene adzauze anthu za mavuto a gulu lankhondo.\u201d (Muslim #2883)<\/p>\n<p>M&#8217;nkhani zina, zanenedwa kuti anthu awiri adzapulumuka mu gululi. Mmodzi adzabwerera kwa Sufyaani ndikumuuza zomwe zachitika, ndipo winayo adzabwera kwa Mahdi ndikumuuza zomwe zachitika. (Ishaa\u2019ah pg. 206, Al-Fitan li-Nu\u2019aim #947)<\/p>\n<p>Nkhani yoti asilikali a Sufyaani adzamira m\u2019nthaka ikadzafalikira pakati pa anthu, Abdaal aku Shaam ndi anthu olungama ku Iraq adzabwera kwa Mahdi (radhwiyallahu \u2018anhu) ndi kumulonjeza chikole pamaso pake.<\/p>\n<p>Kenako Mahdi (Radhwiyallahu \u2018anhu) adzati: \u201cYakwana nthawi yoti ndituluke ku Makka Mukarramah.\u201d\u00a0 (Ishaa\u2019ah tsamba 206)<\/p>\n<p>Mtumiki (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wa sallam) adafotokoza za kuonekera kwa mahdi (Radhiya Allaahu \u2018anhu) mu Hadith yolemekezwka. Rasulullah (swallallahu \u2018alaihi wasallam) anati:<\/p>\n<p>\u201cPadzakhala kusiyana maganizo (pakati pa Asilamu omwe ali ndi udindo osankha mtsogoleri) mtsogoleri wawo akadzamwalira. (Panthawiyo,) munthu wina ochokera ku Madinah Munawwarah adzatulukira, kuthawira ku Makkah Mukarramah. Ena mwa anthu a ku Makkah Mukarramah adzabwera kwa iye ndikumutulutsa (mnyumba mwake) mosasamala kanthu za zomwe akufuna, pambuyo pake adzalonjeza kukhulupirika pamaso pake pakati pa Hajr-e-Aswad ndi Maqaam-e-Ebrahim. Pambuyo pake, gulu lankhondo lidzatumizidwa motsutsana naye kuchokera kwa anthu a ku Shaam. Gulu limeneli lidzamira pansi likadzafika pamalo ouma pakati pa Makkah Mukarramah ndi Madinah Munawwarah. Anthu akadzaona izi, Abdaals a ku Shaam ndi anthu opembedza a ku Iraq adzabwera kwa iye ndikulonjeza kukhulupirika pamaso pake pakati pa Hajr-e-Aswad ndi Maqaam-e-Ebrahim. (Abu Dawood) #4286)<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) asanaonekere padziko lapansi, anthu ambiri padziko lonse lapansi adzakhala Akhristu. (Muslim #2898) M&#8217;madera ambiri padziko lapansi, Ummah wa Chisilamu udzakhala ukuvutika ndipo udzazunzidwa ndi kuvutitsidwa ndi makafiri. Nkhondo zambiri zidzabuka ndipo Asilamu padziko lonse lapansi adzakhala akuyembekezera mwachidwi kubwera kwa Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) kuti awathandize. Panthawiyo, Sufyaani (munthu ochokera ku banja la &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":3880,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[28],"tags":[],"class_list":["post-4041","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-zizikiro-za-qiyaamah"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4041","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=4041"}],"version-history":[{"count":1,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4041\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":4042,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4041\/revisions\/4042"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/3880"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=4041"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=4041"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=4041"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}