{"id":4049,"date":"2026-04-28T13:35:08","date_gmt":"2026-04-28T11:35:08","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4049"},"modified":"2026-05-14T13:35:06","modified_gmt":"2026-05-14T11:35:06","slug":"nkhani-yokhudza-kulowa-chisilamu-kwa-sayyiduna-wahshi-radhwiyallahu-anhu","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4049","title":{"rendered":"Nkhani Yokhudza Kulowa Chisilamu Kwa Sayyiduna Wahshi Radhwiyallahu Anhu"},"content":{"rendered":"<p>Pankhondo ya Uhud, chimodzi mwa zowawa zowawitsa zomwe zidamuchitikira Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kudali kuphedwa kwa amalume ake okondedwa Sayyiduna Hamzah (radhwiyallahu anhu) Amene adamupha Hamzah sanali wina koma Wahshi bun Harb<\/p>\n<p>Nthawi imeneyo ndikuti asadakhale nsilamu, koma Allah Talaa pambuyo pake adamdalitsa ndi Imaan ndi ulemelero okhala Sahaabi.<\/p>\n<p>Nkhani yokhudza kuvomera kwake Chisilamu ili motere:<\/p>\n<p>Pambuyo poti Allah Talaa adamudalitsa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) ndi ma Swahaabah (radhwiyallahu anhum) pogonjetsa Makka Mukarramah, Hazrat Wah\u064fshiadathawira ku Taa&#8217;if, poopa kuti Asilamu angamugwire ndikumupha ngati kubwezera imfa ya Hamzah (radhwiyallahu anhu).<\/p>\n<p>Pambuyo pake anthu aku Taa&#8217;if atafuna kulowa chisilamu, adatumiza nthumwi kwa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam).<\/p>\n<p>Nthawi imeneyo Wahshi (radhwiyallahu anhu) nayenso adatsagana ndi nthumwi imeneyi nadzafika ku Makka Mukarramah. Atadza kwa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam). Rasulullah (swallallahu alaihi\u00a0 wasallam) adamfunsa: &#8220;Kodi ndiwe Wahshi?&#8221; Hazrat Wahshi (radhwiyallahu anhu) anayankha &#8220;Inde, ndine Wahshi.&#8221;<\/p>\n<p>Kenako Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati: \u201cKodi ndiwe amene udapha Hamzah?<\/p>\n<p>Hazrat Wahshi adayankha nati, &#8220;Inde, nkhani (yokhudza ine kupha amalume anu) ili yomwemo momwe mudamvera (ndine amene ndidapha amalume anu).&#8221;<\/p>\n<p>Ngakhale Wahshi (radhwiyallahu anhu) adapha amalume ake Hazrat Hamzah (radhwiyallahu anhu) Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adali ndi nkhawabe za chipulumutso chake. Nkhawa yaikulu imeneyi idali yochokera mu chikondi chakuya chimene Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anali nacho pa Ummati wake.<\/p>\n<p>Choncho, Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) nthawi yomweyo adamuitanira Hazrat Wahshi (radhwiyallahu anhu) kuti alowe m&#8217;Chisilamu.<\/p>\n<p>Hazrat Wahshi (radhwiyallahu anhu) ankafunitsa kuti alowe Chisilamu, komabe anali ndi nkhawa zochepa mu mtima mwake zomwe zinkamulepheretsa kulowa m\u2019Chisilamu.<\/p>\n<p>Choncho adayankha: &#8220;Eh Muhammad (swallallahu alaihi wasallam) ! Ndilowe bwanji Chisilamu pomwe Qur&#8217;an Majiid ikunena kuti amene wapha munthu, kuchita shirk kapena kuchita chisembwere sadzakhululukidwa ndipo adzatumizidwa ku Jahannum? Allah akuti:<\/p>\n<p class=\"\" dir=\"RTL\" style=\"text-align: center; font-family: usmaan_taha; font-size: 16pt; line-height: 38px;\"><span id=\"25-68\" class=\"aya selected\">\u0648\u064e\u0627\u0644\u0651\u064e\u0630\u0650\u064a\u0646\u064e \u0644\u064e\u0627 \u064a\u064e\u062f\u0652\u0639\u064f\u0648\u0646\u064e \u0645\u064e\u0639\u064e \u0627\u0644\u0644\u0651\u064e\u0647\u0650 \u0625\u0650\u0644\u064e\u0670\u0647\u064b\u0627 \u0622\u062e\u064e\u0631\u064e \u0648\u064e\u0644\u064e\u0627 \u064a\u064e\u0642\u0652\u062a\u064f\u0644\u064f\u0648\u0646\u064e \u0627\u0644\u0646\u0651\u064e\u0641\u0652\u0633\u064e \u0627\u0644\u0651\u064e\u062a\u0650\u064a \u062d\u064e\u0631\u0651\u064e\u0645\u064e \u0627\u0644\u0644\u0651\u064e\u0647\u064f \u0625\u0650\u0644\u0651\u064e\u0627 \u0628\u0650\u0627\u0644\u0652\u062d\u064e\u0642\u0651\u0650 \u0648\u064e\u0644\u064e\u0627 \u064a\u064e\u0632\u0652\u0646\u064f\u0648\u0646\u064e<span class=\"sign\">\u00a0\u06da<\/span>\u00a0\u0648\u064e\u0645\u064e\u0646 \u064a\u064e\u0641\u0652\u0639\u064e\u0644\u0652 \u0630\u064e\u0670\u0644\u0650\u0643\u064e \u064a\u064e\u0644\u0652\u0642\u064e \u0623\u064e\u062b\u064e\u0627\u0645\u064b\u0627\u00a0<span class=\"ayaNumber\">\u200e\ufd3f\u0666\u0668\ufd3e\u200f<\/span><\/span>\u00a0<span id=\"25-69\" class=\"aya\">\u064a\u064f\u0636\u064e\u0627\u0639\u064e\u0641\u0652 \u0644\u064e\u0647\u064f \u0627\u0644\u0652\u0639\u064e\u0630\u064e\u0627\u0628\u064f \u064a\u064e\u0648\u0652\u0645\u064e \u0627\u0644\u0652\u0642\u0650\u064a\u064e\u0627\u0645\u064e\u0629\u0650 \u0648\u064e\u064a\u064e\u062e\u0652\u0644\u064f\u062f\u0652 \u0641\u0650\u064a\u0647\u0650 \u0645\u064f\u0647\u064e\u0627\u0646\u064b\u0627\u00a0<span class=\"ayaNumber\">\u200e\ufd3f\u0666\u0669\ufd3e<\/span><\/span><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Ndipo amene sapembedza milungu ina poiphatikiza ndi Allah, ndipo sapha munthu amene Allah waletsa kumupha, kupatula mwachilungamo, ndipo sachita zina (chigololo); ndipo amene achita izi (ngati kuchita shirk, kupha ndi zina), adzalandira chilango (mu Jahannum). Chilango (ku Jahannum) chidzawirikiza kawiri pa iye pa Tsiku la Qiyaamah ndipo adzakhalabe mmenemo monyozeka.<\/em><\/p>\n<p>Wahshi radhwiyalahu anhu kenako anati, &#8220;Kukamba za ine, ndiye ndachita machimo onse akuluakuluwa, kodi pali mwayi ulionse oti ndikhululukidwe?&#8221;<\/p>\n<p>Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adakhala chete osayankha mpaka Allah adavumbulutsa aya ya Quraan Majiid:<\/p>\n<p class=\"\" dir=\"RTL\" style=\"text-align: center; font-family: usmaan_taha; font-size: 16pt; line-height: 38px;\">\u0625\u0650\u0644\u0651\u064e\u0627 \u0645\u064e\u0646 \u062a\u064e\u0627\u0628\u064e \u0648\u064e\u0622\u0645\u064e\u0646\u064e \u0648\u064e\u0639\u064e\u0645\u0650\u0644\u064e \u0639\u064e\u0645\u064e\u0644\u064b\u0627 \u0635\u064e\u0627\u0644\u0650\u062d\u064b\u0627 \u0641\u064e\u0623\u064f\u0648\u0644\u064e\u0670\u0626\u0650\u0643\u064e \u064a\u064f\u0628\u064e\u062f\u0651\u0650\u0644\u064f \u0627\u0644\u0644\u0651\u064e\u0647\u064f \u0633\u064e\u064a\u0651\u0650\u0626\u064e\u0627\u062a\u0650\u0647\u0650\u0645\u0652 \u062d\u064e\u0633\u064e\u0646\u064e\u0627\u062a\u064d<span class=\"sign\">\u00a0\u06d7<\/span>\u00a0\u0648\u064e\u0643\u064e\u0627\u0646\u064e \u0627\u0644\u0644\u0651\u064e\u0647\u064f \u063a\u064e\u0641\u064f\u0648\u0631\u064b\u0627 \u0631\u0651\u064e\u062d\u0650\u064a\u0645\u064b\u0627\u00a0<span class=\"ayaNumber\">\u200e\ufd3f\u0667\u0660\ufd3e<\/span><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>(Amene achita machimo awa a shirk, kupha ndi zina, sadzakhululukidwa ndipo adzalangidwa ku Jahannamu) pokhapokha atalapa; ndikubweretsa Imaan, ndipo namachita ntchito zabwino, kotero iwo Mulungu adzawasinthira zoipa zawo kukhala zabwino ndithudi Allah ndi Ndi Okhululuka ndi Wachifundo.<\/em><\/p>\n<p>atamva vesi iyi, Hazrat Wahshire anayankha kuti, &#8220;analonjeza kukhululukira anthu amene achita izi zomwe ndachita, koma kukhululukidwa kwawo kuli ndi malire.<\/p>\n<p>&#8220;Chofunikira ndichakuti alape, abweretse Imaan ndikuchita ntchito zabwino m&#8217;miyoyo yawo.&#8221; Ndidziwa bwanji ngati ndikwanitsa kukwaniritsa izi (ndipo kuti ndipeza chikhululukiro cha Allah)&#8221;<\/p>\n<p>Ndipo Allah Talaa adavumbulutsa ndime iyi:<\/p>\n<p class=\"\" dir=\"RTL\" style=\"text-align: center; font-family: usmaan_taha; font-size: 16pt; line-height: 38px;\">\u0625\u0650\u0646\u0651\u064e \u0627\u0644\u0644\u0651\u064e\u0647\u064e \u0644\u064e\u0627 \u064a\u064e\u063a\u0652\u0641\u0650\u0631\u064f \u0623\u064e\u0646 \u064a\u064f\u0634\u0652\u0631\u064e\u0643\u064e \u0628\u0650\u0647\u0650 \u0648\u064e\u064a\u064e\u063a\u0652\u0641\u0650\u0631\u064f \u0645\u064e\u0627 \u062f\u064f\u0648\u0646\u064e \u0630\u064e\u0670\u0644\u0650\u0643\u064e \u0644\u0650\u0645\u064e\u0646 \u064a\u064e\u0634\u064e\u0627\u0621\u064f<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Ndithu Allah samakhululuka tchimo lomuphatikiza iye ndi mafano, ndipo amakhululuka machimo ena onse amene wamfuna.<\/em><\/p>\n<p>Atamva izi,Wahshi adati: Oh Muhammad, Aya iyi Allah akunena kuti adzamukhululukira ekhayo amene iye wamufuna, koma ineyo sindikudziwa kuti kodi Allah adzafuna kuti andikhululukire kapena ayi, kodi pali njira inayake yomwe ungandiuze ngati yomwe ingandipatse chiyembekezo choti ndidzakhululukidwa?<\/p>\n<p>Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adakhala chete osayankha mpaka Allah Talaa Adavumbulutsa aya iyi:<\/p>\n<p class=\"\" dir=\"RTL\" style=\"text-align: center; font-family: usmaan_taha; font-size: 16pt; line-height: 38px;\"><span class=\"juz-sign\">\u06de<\/span>\u00a0\u0642\u064f\u0644\u0652 \u064a\u064e\u0627 \u0639\u0650\u0628\u064e\u0627\u062f\u0650\u064a\u064e \u0627\u0644\u0651\u064e\u0630\u0650\u064a\u0646\u064e \u0623\u064e\u0633\u0652\u0631\u064e\u0641\u064f\u0648\u0627 \u0639\u064e\u0644\u064e\u0649\u0670 \u0623\u064e\u0646\u0641\u064f\u0633\u0650\u0647\u0650\u0645\u0652 \u0644\u064e\u0627 \u062a\u064e\u0642\u0652\u0646\u064e\u0637\u064f\u0648\u0627 \u0645\u0650\u0646 \u0631\u0651\u064e\u062d\u0652\u0645\u064e\u0629\u0650 \u0627\u0644\u0644\u0651\u064e\u0647\u0650<span class=\"sign\">\u00a0\u06da<\/span>\u00a0\u0625\u0650\u0646\u0651\u064e \u0627\u0644\u0644\u0651\u064e\u0647\u064e \u064a\u064e\u063a\u0652\u0641\u0650\u0631\u064f \u0627\u0644\u0630\u0651\u064f\u0646\u064f\u0648\u0628\u064e \u062c\u064e\u0645\u0650\u064a\u0639\u064b\u0627<span class=\"sign\">\u00a0\u06da<\/span>\u00a0\u0625\u0650\u0646\u0651\u064e\u0647\u064f \u0647\u064f\u0648\u064e \u0627\u0644\u0652\u063a\u064e\u0641\u064f\u0648\u0631\u064f \u0627\u0644\u0631\u0651\u064e\u062d\u0650\u064a\u0645\u064f\u00a0<span class=\"ayaNumber\">\u200e\ufd3f\u0665\u0663\ufd3e<\/span><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>E inu akapolo Anga amene adzilakwir okha! Musataye mtima ndi chifundo cha Allah. Allah amakhululukira machimo onse popeza Iye Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni.<\/em><\/p>\n<p>Hazrat Wahshi (radhwiyallahu anhu) atamva ndime iyi, Adati: &#8220;Inde! Ndime iyi (ndi aya yomwe yandipatsa chiyembekezo choti ndikhululukidwa)!&#8221; Atalankhula izi nthawi yomweyo adalowa Chisilamu.<\/p>\n<p>Kenako ma Swahaabah (radhiyallahu anhumu) adafunsa Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) &#8220;E, Mtumiki wa Allah (Swallallahu alaihi wasallam)! M\u2019ndime iyi, Allah Talaa walonjeza kuti adzawakhululukira amene alapa kwa Iye. Kodi lonjezo limeneli likukhudzanso ifeyo?&#8221;<\/p>\n<p>Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adati:<\/p>\n<p>\u201cLonjezo ili likugwira ntchito kwa Asilamu onse amene amatembenukira kwa Allah ndi kulapa.&#8221; Kuchokera pa nkhaniyi, tikuona chikondi chachikulu chomwe Allah ali nacho pa akapolo ake.<\/p>\n<p>Allah amakonda kukhululukira akapolo Ake. Kaya munthu ali kutali bwanji ndi deen, komanso kuti machimo ake ndi ochuluka bwanji komanso oipa bwanji, ngati atembenukira kwa Allah Talaa ndi kulapa koona mtima ndi kupanga chitsimikizo cholimba chosintha makhalidwe ake, ndiye kuti Allah adzamukhululukiradi.<\/p>\n<p><strong>Chifundo Chachikulu ndi Chikhululuko cha Allah<\/strong><\/p>\n<p>Zanenedwa mu Hadith Qudsi kuti Allah akunena kuti: Oh mwana wa Aadam bola ngati utatembenukira kwa Ine (kulapa ndikukhala ndi chiyembekezo ndi chikhululuko Changa, ndidzakukhululukira machimo ako, ndipo sindidzasamala (palibe angandifunse).<\/p>\n<p>&#8220;Oh iwe mwana wa Aadam ! Ngakhale machimo ako atafika kumitambo ndipo kenako niutembenukira kwa Ine, kufunafuna chikhululuko Changa, Ine ndidzakukhululukira ndipo sindidzasamala.<\/p>\n<p>&#8220;Oh mwana wa Aadam ! Ngati ubwera kwa Ine ndi machimo ako ochuluka kudzadza dziko lonse lapansi ndipo ndikubwera kwa ine uli oti siunandiphatikizeko ndi milungu ina, Ine ndidzabwera kwa iwe ndi dziko lonse lapansi lodzadza ndi chikhululuko.&#8221;<br \/>\nChoncho, okhulupirira sayenera kutaya mtima ndi chiyembekezo mu chifundo cha Allah Talaa Choncho pangatalike bwanji chiyembekezo chilipo.<\/p>\n<p>Allah atidalitse tonse ndi tawfeeq yotembenukira kwa Iye nthawi zonse polapa, aameen.<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Pankhondo ya Uhud, chimodzi mwa zowawa zowawitsa zomwe zidamuchitikira Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kudali kuphedwa kwa amalume ake okondedwa Sayyiduna Hamzah (radhwiyallahu anhu) Amene adamupha Hamzah sanali wina koma Wahshi bun Harb Nthawi imeneyo ndikuti asadakhale nsilamu, koma Allah Talaa pambuyo pake adamdalitsa ndi Imaan ndi ulemelero okhala Sahaabi. Nkhani yokhudza kuvomera kwake Chisilamu ili &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":3556,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[24],"tags":[],"class_list":["post-4049","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-minda-ya-chikondi"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4049","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=4049"}],"version-history":[{"count":4,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4049\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":4075,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4049\/revisions\/4075"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/3556"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=4049"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=4049"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=4049"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}