{"id":4065,"date":"2026-05-09T15:38:02","date_gmt":"2026-05-09T13:38:02","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4065"},"modified":"2026-05-09T15:42:15","modified_gmt":"2026-05-09T13:42:15","slug":"gulu-lankhondo-lokhala-ndi-mbendera-zakuda-lochokera-ku-khurasaan","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4065","title":{"rendered":"Gulu Lankhondo Lokhala ndi Mbendera Zakuda Lochokera ku Khurasaan"},"content":{"rendered":"<p>Pambuyo poti Mahdi waonekera pakati pa anthu ndipo nkhani ya kuonekera kwake yayamba kufalikira padziko lonse lapansi, gulu lankhondo lokhala ndi mbendera zakuda lidzachoka ku Khurasaan kupita ku Makkah Mukarramah ndikukhalira limodzi ndi Mahdi. Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) adalimbikitsa ummah kuti udzakhale ndi gulu lankhondo limeneli pobwera kwa Mahdi.<\/p>\n<p>Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, \u201cMukadzaona gulu lankhondo lokhala ndi mbendera zakuda likuchokera ku Khuraasaan (likupita ku Makkah Mukarramah kukagwirizana ndi Mahdi), ni ndi gulu lankhondo ili. Popeza ndithudi, mgulu lankhondo limeneli mudzakhala Khaleefah wa Allah Ta\u2018ala, Mahdi (kutanthauza kuti adzakhala mgulu lankhondo ili akadzagwirizana naye ku Makkah Mukarramah).\u201d (Musnad-e-Ahmed #22387)<\/p>\n<p>Mu nkhani ina, Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) adanena kuti munthu aliyense adzayenera kuyesetsa kuti adzakhale nawo mgulu lankhondo la Mahdi (radhwiyallahu \u2018anhu), ngakhale atadzachita kudzikhukhuluza pansi mu sinowo kuyesa kukalifikira. (Sunan Ibnu Maajah #4084 ndi Al-Fitan li-Nu\u2019aim #853 )_<\/p>\n<p>M&#8217;ma Riwaayaat ena, pali magulu ena ankhondo omwe adzanyamure mbendera zakuda. Komabe, sadzakhala gulu lankhondo la Mahdi. kotero, ndikofunikira kuti ummah usadzasokonezeke kulizindikira gulu la Mahdi. Chinthu chodziwika bwino cha gulu lankhondo la Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) ndichakuti adzakhala anthu olungama, chifukwa adzakhala akusunga Sunnah ya Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) nthawi zonse.<\/p>\n<p>Gulu lankhondo la Khurasaan likadzalowa m\u2019gulu la Mahdi (Radhwiyallahu \u2018anhu) ku Makkah Mukarramah, Mahdi (Radhwiyallahu \u2018anhu) adzachoka ku Makka Mukarramah ndi asilikali kupita ku Madina Munawwarah.<\/p>\n<p>Akadzafika ku Madinah Munawwarah, Mahdi (Radhwiyallahu \u2018anhu) adzabwera ku Rowdhah Mubaarak ndikupereka salaamu yake kwa Mtumiki (Swalla Allaahu \u2018alayhi wa aalihi wa sallam). (Qiyaamat kub Aaegi pg. 90) Adzapulumutsanso anthu a ku Madina Munawwarah ndi ma Sayyid omwe adzakhale kuti adatsekeredwa m\u2019ndende ndi kuzunzidwa ndi gulu lankhondo la Sufyaani. (Ishaa\u2019ah tsamba 206)<\/p>\n<p>Pochoka ku Madina Munawwarah, Mahdi (Radhwiyallahu \u2018anhu), pamodzi ndi gulu lankhondo la Asilamu, adzamenya nkhondo zambiri. Zina mwa nkhondo zomwe adzamenyane ndi nkhondo yolimbana ndi gulu la Sufyaani. Pankhondoyi, Allah Ta \u2018ala adzadalitsa gulu lankhondo la Mahdi ndi chigonjetso.<\/p>\n<p>Akadzapambana, Mahdi adzagawa zofunkha pakati pa gulu lake lankhondo motsatira Sunnah ya Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam), ndipo kuyambira pamenepo, Chisilamu chidzayamba kufalikira padziko lapansi.<\/p>\n<p>Pofotokoza za nkhondo ndi Sufyaani ndi chigonjetso chimene Allah Ta\u2018ala adzamupatse Mahdi (Radhwiyallahu \u2018anhu), Rasulullah (Swallallahu \u2018alayhi wasallam) adati:<\/p>\n<p>\u201cMunthu ochokera mwa Aquraish, amene banja lake la amayi ake lidzachokera ku fuko la Kalb (Yemwe ndi Sufyaani), adzatuluka ndi kutumiza gulu lankhondo motsutsana ndi Mahdi (radhwiyallahu \u2018anhu) ndi omutsatira ake. Mahdi (radhwiyallahu \u2018anhu) ndi omutsatira ake adzagonjetsa gulu limeneli. Gulu lankhondo limenelo lidzakhala lochokera ku fuko la Kalb, ndipo amene sadzakhalapo nthawi imene zofunkha zomwe zidzatengedwe kuchokera ku fuko la Kalb zidzagawidwa adzakhala otaika (amene sadzakhala nawo m\u2019gulu lankhondo la Mahdi, akumenyana ndi gulu lankhondo la Sufyaani mpaka kumapeto adzatayika). Mahdi (radhiyallahu \u2018anhu) adzagawa chuma ndipo adzathandiza anthu mogwirizana ndi sunnah ya Nabi wawo (Swallallahu alaihi wasallam). Kenako Chisilamu chidzakhala champhamvu ndi kukhazikika padziko lapansi.\u201d (Abu Dawood #4286 )<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Pambuyo poti Mahdi waonekera pakati pa anthu ndipo nkhani ya kuonekera kwake yayamba kufalikira padziko lonse lapansi, gulu lankhondo lokhala ndi mbendera zakuda lidzachoka ku Khurasaan kupita ku Makkah Mukarramah ndikukhalira limodzi ndi Mahdi. Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) adalimbikitsa ummah kuti udzakhale ndi gulu lankhondo limeneli pobwera kwa Mahdi. Rasulullah (Swallallahu \u2018alaihi wasallam) adati, \u201cMukadzaona &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":3351,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[28],"tags":[],"class_list":["post-4065","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-zizikiro-za-qiyaamah"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4065","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=4065"}],"version-history":[{"count":2,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4065\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":4068,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4065\/revisions\/4068"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/3351"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=4065"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=4065"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=4065"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}