{"id":4083,"date":"2026-05-20T07:00:47","date_gmt":"2026-05-20T05:00:47","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4083"},"modified":"2026-05-20T07:01:22","modified_gmt":"2026-05-20T05:01:22","slug":"sunnati-ndi-adaab","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4083","title":{"rendered":"Sunnati Ndi Adaab 1"},"content":{"rendered":"<p>1. Mukamaliza Swala ya Esha, musakhale kumacheza nkhani zopanda pake mmalo mwake yesetsani kugona mwachangu kuti mudzukire Tahajjud komanso Swala ya Fajr mnthawi yake. Komabe, ngati pali chifukwa chomveka, monga kukambirana ndikuchita za Dini mutha, kukambirana za malamulo a Dini mashwarah ofunikira, ndi zina zotero. ndiye kuti mudzaloredwa kuchita nawo zokambiranazi pambuyo pa Esha.<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Olemekezeka Abu Barzah (radiyahullah anhu) akusimba kuti Mtumiki (swahallhu alayhi wasallam) sankakonda kuti munthu agone Esha isanapempheredwe, ndi kumakambirana pambuyo pa Esha (popanda kufunikira).<\/em><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Sayyiduna Umar (radiyahullah anhu) adati: \u201cMtumiki (swahallhu alayhi wasallam) ankakambirana pambuyo pa Esha ndi Abu Bakr. nayenso ali pomwepo.<\/em><\/p>\n<p><em>Bibi Aaishah (radiyahullah anha) akunena kuti sanamuonepo Rasulullah (swahallhu alayhi wasallam) akugona Esha asanapemphere, komanso sanamuone akukambirana zopanda pake pambuyo pa Esha. Ankachita ma zikr a Allah Talaa atatha kuswali Esha kudzera mukuchulukitsa kupeza mphotho za Tsiku Lomaliza ndikukhala opambana, apo ayi ankagona, kotero amadzipulumutsa (ku zinthu zopanda phindu).<\/em><\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Bibi \u200eAaishah (radiyahullah anha) akunenanso kuti &#8220;Kukambirana pambuyo pa Esha ndikoloredwa kwa magulu atatu a anthu; kwa omwe ali pa banja, omwe ali pa ulendo kuti zimuthandizire kukhala m&#8217;maso ndikumalizitsa ulendo wake) ndi amene akufuna kuswali mkatikati mwa usiku.<\/em><\/p>\n<p>2. Ndi sunnah kugona uli ndi wudhu.<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Sayyiduna Mu\u2019aaz bun Jabal (radiyahullah anhu) wafotokoza kuti Mtumiki (swahallhu alayhi wasallam) adati: \u201cAmene wagona uli ndi wudhu, kenako n\u2019kudzukira usiku (Kapena kutembenukira mbali kuchoka komwe anali) ndi kutembenukira kwa Allah kupempha Chilichonse chomwe kaya ndi chapadziko lapansi kapena Tsiku Lomaliza, ndithudi, Allah Talaa adzachipereka kwa iye.\u201d<\/em><\/p>\n<p>3. Musanagone, muyenera kukuntha pogona panu, chifukwa pakhoza kukhala zilombo zoopsya.<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Abu Hurairah (radiyahullah anhu) wafotokoza kuti Mtumiki (swahallhu alayhi wasallam) adati: \u201cAliyense mwa inu akamakagona, ayenera kukuntha zogonera ndi nsalu yake chifukwa siungadziwe zomwe zikanatha kubwera pogona pakopo pamene iwe kunalibepo.<\/em><\/p>\n<p>4. Tsukani mkamwa mwanu pogwiritsa ntchito miswaak musanagone.<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Abu Hurairah (radiyahullah anhu) akunena kuti nthawi iliyonse Rasulullah (swahallhu alayhi wasallam) akamakagona usiku kapena akadzukira usiku, ankagwiritsa ntchito miswaak.<\/em><\/p>\n<p>5. Ndi mustahab kuthira surmah m&#8217;maso musanagone.<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Abdullah bin Abbaas (radiyahullah anhuma) adanena kuti Mtumiki (swahallhu alayhi wasallam) adati: &#8220;Thirani surmah m&#8217;maso pogwiritsa ntchito ithmid (mtundu wa surmah), ndipo imatsuka m&#8217;maso)&#8221; Olemekezeka Abdullah bin Abbaas (radiyahullah anhuma) akupitiriza kunena kuti Mtumiki (swahallhu alayhi wasallam) ankasunga kabotolo ka surmah komwe ankagwiritsa ntchito pothira m&#8217;maso usiku ulionse. Ankathira surmah katatu m&#8217;diso lamanja ndi katatu m&#8217;diso lamanzere.<\/em><\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>1. Mukamaliza Swala ya Esha, musakhale kumacheza nkhani zopanda pake mmalo mwake yesetsani kugona mwachangu kuti mudzukire Tahajjud komanso Swala ya Fajr mnthawi yake. Komabe, ngati pali chifukwa chomveka, monga kukambirana ndikuchita za Dini mutha, kukambirana za malamulo a Dini mashwarah ofunikira, ndi zina zotero. ndiye kuti mudzaloredwa kuchita nawo zokambiranazi pambuyo pa Esha. Olemekezeka &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":4062,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[39,12],"tags":[],"class_list":["post-4083","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-kugona","category-masunna-ndi-aadaab-miyambo"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4083","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=4083"}],"version-history":[{"count":3,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4083\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":4086,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4083\/revisions\/4086"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/4062"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=4083"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=4083"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=4083"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}