{"id":4095,"date":"2026-06-09T11:47:56","date_gmt":"2026-06-09T09:47:56","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4095"},"modified":"2026-06-21T07:10:59","modified_gmt":"2026-06-21T05:10:59","slug":"munthu-olungama-kwambiri-fudhail-bin-iyaaz-rahimahullah","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4095","title":{"rendered":"Munthu Olungama Kwambiri &#8211; Fudhail Bin Iyaaz Rahimahullah"},"content":{"rendered":"<p>Fudhail bun Iyaaz (Rahimahullah) aDali Muhaddith olemekezeka komanso oyera mtima wa m&#8217;nthawi yake.<\/p>\n<p>Allah Talaa adamdalitsa ndi ulemelero wapamwamba kwambiri mu Hadith kotero kuti ambiri mwa ma Muhadith otsogola, monga Abdullah bin Mubaarak, Sufyaan bun Uyainah ndi Imaam Shaafi&#8217;e (Rahimahullah) adafotokoza Hadith kuchokera kwa iye.<\/p>\n<p>Zanenedwa kuti Fudhail (Rahimahullah) asanadalitsidwe ndi udindo wapamwamba mchipembedzo, ankadziwika kuti anali wachifwamba odziwika bwino wa m&#8217;misewu. Komabe Allah Talaa adamdalitsa ndi tawfiiq (kuthekera) kuti alape machimo ake ndi kukonza moyo wake.<\/p>\n<p>Nkhani yonse yokhudza kulapa Kwake<\/p>\n<p>Ntha\u0175i ina, gulu lina la kalavani linkayenda mumsewu umene Fudhail ankabera anthu. Mwa anthu omwe adali paulendowo panali Qaari yemwe ankawerenga Quraan Majiid mwanthetemya kwambiri.<\/p>\n<p>Gululi likudutsa pafupi ndi Fudhail, Qaariy ankawerenga ndime iyi ya Quraan:<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>Kodi siinafike nthawi yoti mitima ya Asilamu ikhale yamantha pokumbukira Allah&#8230;?<\/em><\/p>\n<p>Atamva aya iyi, mtima wa Fudhail udakhudzidwa kwambiri moti nthawi yomweyo adatembenukira kwa Allah Talaa kulapa ndikusiya moyo wamachimo.<\/p>\n<p>Pambuyo pake, Fudhail (Rahimahullah) adalimbikira kuchita Ibadah ndi kupeza maphunziro a dini, mpaka idafika nthawi yomwe ngakhale Haarun Rasheed (Rahimahullah) mfumu ya nthawiyo, adayamba kumamuyendera kuti apindule ndi malangizo ake.<\/p>\n<p><strong>Mfumu, Haaroon Rasheed (rahimahullah) Kupindula Ndi Malangizo a Fudhail bin Iyaaz (rahimahullah)<\/strong><\/p>\n<p>Zanenedwa kuti nthawi ina Haarun Rashiid (rahimahullah) adachita Haji, adauza Fadhl bun Rabee kuti: &#8220;Ndikumva kufooka mu mtima mwanga. Choncho nditengereni kwa bwenzi loopa Allah Talaa kuti ndikamve malangizo kwa iye ndi kupindula naye.&#8221;<\/p>\n<p>Fadhl adamulangiza kuti apite akakumane ndi Sufyaan bin Uyainah (rahimahullah) atafika kunyumba kwake pakhomo Sufyaan anamulandira ndi ulemu waukulu.<\/p>\n<p>Haaruun Rashiid anamuuza. &#8220;Cholinga cha zomwe ndabwelera ndikudzapempha upangiri kwa inu.&#8221; Sufyaan kenako anamupatsa upangiri wamba.<\/p>\n<p>Pomaliza pake, Haaruun Rashiid (rahimahullah) atafuna kuchoka, anafunsa Suyaan (rahimahullah). &#8220;Kodi muli ndi ngongole zilizonse zomwe ndingakuthandizeni kuzithetsa?&#8221; Sufyaan anayankha movomereza, ndipo Haaruun Rashiid (rahimahullah) anamulamula Fadhl kuti athetse ngongole zake.<\/p>\n<p>Atachoka Sufyan Haaruun Rashiid anatembenukira kwa Fadhl nati, &#8220;Palibe ndapindula kwa Sufyaan (rahimahullah) momwe ndimafunira.&#8221; (Mwina Haaruun Rashiid (rahimahullah) sadakhutitsidwe chifukwa ankaona kuti Sufyaan (rahimahullah) amamupatsa ulemu kwambiri ndi kumulemekeza ndipo sanamuonetse kufooka kwake kulikonse.) Choncho Fadhl adanena kuti apite kwa Imaam Abdur Razzaaq (rahimahullah).<\/p>\n<p>Imaam Abdur Razzaaq (rahimahullah) nayenso adamulandira Haarun Rashiid (rahimahullah) mwaulemu waukulu ndipo adamupatsa upangiri pa zomwe adapempha.<\/p>\n<p>Asananyamuke, Haaruun Rashiid (rahimahullah) adamufunsa: &#8220;Kodi uli ndi mangawa omwe ndingakuthandizireni?&#8221; Imaam Abdur Razzaag atayankha kuti ali ndi ngongole, Haaruun Rashiid (rahimahullah) adamuuza Fadhl kuti athetse ngongolezo.<\/p>\n<p>Apanso atachoka, Haaruun Rasheliid (rahimahullah) adati kwa Fadhl: &#8220;Sindinapindule ndi Imaam Abdur Razzaq (rahimahullah) monga momwe ndimafunira. Ndipezere munthu oyenera yemwe ndingathe kumupitira.&#8221; Fadhl adamuuza kuti apite akakumane ndi Fudhail bin Iyaaz (rahimahullah).<\/p>\n<p>Atakumana ndi Fudhail Haaruun Rashiid (rahimahullah) adamupempha kuti amupatse malangizo.<\/p>\n<p>Fudhail adamuuza kuti, &#8220;Umar bin Abdil Aziiz atasankhidwa kukhala Khalifah, anaitana Saalim bin Abdillah, Muhammad bin Ka&#8217;b ndi Rajaa bin Haywah nati kwa iwo. &#8216;Ndayesedwa ndi mayesero awa a ulamuliro, choncho chonde ndilangizeni.'&#8221;<\/p>\n<p>Fudhail adati, &#8220;Umar bin Abdil Aziiz anali ndi nkhawa kwambiri ndi Khilaafah kotero kuti adaitenga ngati ndi mayeso, pomwe inu mumaitenga ngati ndi mdalitso (ndipo mulibe nkhawa ngati iye).&#8221;<\/p>\n<p>Fudhail (rahimahullah) anamuchenjeza kuti ngati sadzayang&#8217;anira zinthu za Khilaafah motsatira malamulo a shari&#8217;ah, ndiye kuti adzalangidwa ndi chilango cha Jahannum. Chenjezoli linamukhudza kwambiri Haaruun Rashiid (rahimahullah) kotero kuti anayamba kulira kwambiri.<\/p>\n<p>Haaruun Rashiid akufuna zoti adzinyamuka adamufunsa Fudhail &#8220;Kodi muli ndi ngongole zilizonse zomwe mungafune kuti ndikuthandizeni kubweza? Fudhail (rahimahullah) anayankha, &#8220;Inde! Ndili ndi ngongole zomwe ndi ufulu omwe ndili nawo kwa Mbuye wanga. Ngati mukufuna kundithandiza mutha kutero.&#8221;<\/p>\n<p>Kenako Haaruun Rashiid adapereka ndalama kwa Fudhail nati, &#8220;Nazi ma dinar chikwi. Landirani kuchokera kwa ine ngati mphatso ndipo mugwiritse ntchito kwa omwe amadalira inu.&#8221;<\/p>\n<p>Fudhail (rahimahullah) anayankha &#8220;Subhaanallah! Ndakuwonetsani njira yopezera chipulumutso, ndipo umu ndi momwe mukundibwezera? Mukupereka chuma ichi kwa munthu amene alibe chosowa. Muyenera kuchipereka kwa amene akuchisowa.&#8221;<\/p>\n<p>Haarun Rashid (rahimahullah) ndi Fadhl pambuyo pake adachoka ku nyumba ya Fudhail (rahimahullah) Haarun Rashid (rahimahullah) adati kwa Fadhl: \u201cOh Fadhl! ukafuna kunditengera kwamunthu aliyense uzinditengera kwameneyu,Ndithu, Uyu ndi Mtsogoleri wa Asilamu onse!\u201d<\/p>\n<p>Haarun Rashid (rahimahullah) adachita chidwi kwambiri ndi Fudhail (rahimahullah) chifukwa cha makhalidwe abwino omwe adali nawo &#8211; kuopa kudzayankha mlandu wake pa Tsiku Lomaliza, kuopa kwake kwakukulu, kusakondweretsedwa kwake ndi zapadziko lapansi, kudzipereka kwake mu shariah ndi Sunnah ndi malangizo ake owona mtima kwa mfumu.<\/p>\n<p>za m\u2019mene ayenera kuyendetsera zinthu za Khilafah Kunena zoona, Haarun Rashid (rahimahullah) adachitira umboni kuti Fudhail (rahimahullah) anali chitsanzo cha Sunnah.<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Fudhail bun Iyaaz (Rahimahullah) aDali Muhaddith olemekezeka komanso oyera mtima wa m&#8217;nthawi yake. Allah Talaa adamdalitsa ndi ulemelero wapamwamba kwambiri mu Hadith kotero kuti ambiri mwa ma Muhadith otsogola, monga Abdullah bin Mubaarak, Sufyaan bun Uyainah ndi Imaam Shaafi&#8217;e (Rahimahullah) adafotokoza Hadith kuchokera kwa iye. Zanenedwa kuti Fudhail (Rahimahullah) asanadalitsidwe ndi udindo wapamwamba mchipembedzo, ankadziwika &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":2970,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[24],"tags":[],"class_list":["post-4095","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-minda-ya-chikondi"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4095","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=4095"}],"version-history":[{"count":3,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4095\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":4109,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4095\/revisions\/4109"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/2970"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=4095"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=4095"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=4095"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}