{"id":4161,"date":"2026-07-22T10:18:42","date_gmt":"2026-07-22T08:18:42","guid":{"rendered":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4161"},"modified":"2026-08-04T13:30:09","modified_gmt":"2026-08-04T11:30:09","slug":"tsiku-la-chiweruzo-tsiku-lodzakhudwa-kwa-anthu-ambiri","status":"publish","type":"post","link":"https:\/\/ny.alislaam.com\/?p=4161","title":{"rendered":"Tsiku La Chiweruzo &#8211; Tsiku Lodzakhudwa Kwa Anthu Ambiri"},"content":{"rendered":"<p>Mu Quraan Majid, Tsiku la Qiyaamah latchulidwa ndi mayina osiyanasiyana. Mayina ena mwa awa ndi &#8220;Tsiku la Mphotho ndi Kubwezera&#8221;, &#8220;Tsiku losonkhana&#8221;, &#8220;Tsiku la Kutayika ndi Kupindula&#8221; (lodzataika kwa osakhulupirira ndi la phindu kwa okhulupirira), ndi &#8220;Tsiku la Kukumana&#8221; (kutanthauza kukumana ndi Allah Talaa.<\/p>\n<p>Tikayang&#8217;ana mayina awa, timapeza kuti dzina lililonse likumaonetsa momwe zinthu zidzakhalire pa Tsiku la Qiyaamah.<\/p>\n<p>Mkakati mwa maina a Tsiku la Qiyaamah palinso &#8220;Tsiku la Chisoni&#8221;. Tsikuli lidzakhala tsiku lachisoni chachikulu kwa osakhulupirira, monga momwe Allah Talaa akufotokozera mu Quraan Majid:<\/p>\n<p class=\"\" dir=\"RTL\" style=\"text-align: center; font-family: 'Traditional Arabic'; font-size: 16pt;\">\u0648\u064e\u0627\u0646\u0652\u0630\u0650\u0631\u0652\u0647\u064f\u0645\u0652 \u064a\u064e\u0648\u0652\u0645\u064e \u0627\u0644\u0652\u062d\u064e\u0633\u0652\u0631\u064e\u0629\u0650 \u0625\u0650\u0630\u0652 \u0642\u064f\u0636\u0650\u064a\u064e \u0627\u0644\u0652\u0623\u064e\u0645\u0652\u0631\u064f<\/p>\n<p style=\"text-align: center;\"><em>(0h Muhammad\u00a0 (swallahu alyhi wasallam) ! Achenjeze (osakhulupirira) za Tsiku la Madandaulo, pamene chigamulo chidzaperekedwe (kuti akalowe ku moto wa Jahannum ndikukhalamo kwamuyaya).<\/em><\/p>\n<p>Kuchokera pa izi, tikuzindikira kuti Tsiku la Qiyaamah lidzakhala tsiku lodandaula mosaganizirika kwa osakhulupirira. Komabe, monga momwe lidzakhalire tsiku lachisoni kwa osakhulupirira, lidzakhalanso, pamlingo wina, tsiku la chisoni ndi lodandauritsa kwa okhulupirira ena.<\/p>\n<p><strong>Dandaulo Lokhalo La Anthu a ku Jannah<\/strong><\/p>\n<p>Pofotokoza za dandaulo la anthu okhulupirira Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati, &#8220;(Asanalowe ku Jannah,) dandaulo lokhalo lomwe anthu a ku Jannah adzakhale nalo lidzakhala nthawi ndi mphindi zomwe zidadutsa (padziko lapansi) popanda iwo kukumbukira Allah<\/p>\n<p>Allah akamadzapereka mphoto zazikulu komanso zapwamwamba kwa akapolo Ake apadera chifukwa cha nthawi yomwe adagwiritsa ntchito pomukumbukira, apkapolo ake ena adzakhudzika ndi chisoni chifukwa cha nthawi yamtengo wapatali ndi mwayi omwe adaononga padziko lapansi popanda kukumbukira Allah.<\/p>\n<p><strong>Nkhani Ya Maysarah bin Masrooq Abasi Rahimahullah<\/strong><\/p>\n<p>M\u2019munsimu muli nkhani yopangitsa kuganiza mozama yomwe ikusonyeza ubwino waukulu wa Imaan ndi moyo, ndi kufunikira kosazengereza kuchita zabwino.<\/p>\n<p>Abdullah bin Waabisah Abasi akufotokoza nkhani yotsatirayi kuchokera kwa agogo ake. Nkhaniyi idachitika agogo ake asanabwelere ku chisilamu. Iye akunena kuti:<\/p>\n<p>Nthawi ina, m&#8217;masiku oyambilira a Chisilamu, Rasulullah adabwera kwa ife pamene tili mumsasa wathu ku Mina. Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) pobwera kwa ife, anali atakwera chokwera chake pomwe Zaid bin Haarithah radhwiyallahu anhu anali atakhala kumbuyo kwake. Kenako Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adatilankhula natiitanira ku Chisilamu.<\/p>\n<p>Komabe, ndikulumbira mwa Allah sitinavomereze kuyitanira kwake, ndipo zabwino zinali zisanatilembere panthawiyo. Tidamva za iye kale ndipo tidamvanso akuitanira anthu ku Chisilamu m&#8217;masiku a Hajj. Pano pamene adayima pamaso pathu ndikutiitanira ku Chisilamu, sitidayankhe ndikulandira uthenga wake.<\/p>\n<p>Pakati pa gulu lathu panali munthu wina dzina lake Maysarah bin Masroog Abasi. Atamva uthenga ndi kuitana kwa Rasulullah (swallallahualaihi wasallam), anawafotokozera anthu ake kuti, &#8220;Ndikulumbira mwa Allah! Ngati tivomereza uthenga wa munthu uyu ndi kumutenga, mpaka titamukhazikitsa pakati pathu ndikukhala pakati pathu, ndiye kuti tidzachita zomwe zili zanzeru komanso zothandiza kwa ife! Ndikulumbira mwa Allah ndipo ndiri ndi chikhulupiliro kuti uthenga wake udzapambana ndi kupita kutali!&#8221;<\/p>\n<p>Komabe, akubanja kwake anati, &#8220;Tisiye m&#8217;nkhaniyi ndipo usatiwelengere mu chinthu chomwe sitingathe kuchichita.&#8221; Komabe, poona kuti waonetsa mtima ovomereza, Rasulullah swallallahu alaihi wasallam anakhala ndi chiyembekezo chakuti Maysarah adzabwelera ku Chisilamu ndipo kotero anapitilira kuyalankhula naye.<\/p>\n<p>Atamva mawu odala ndi uthenga wa Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) Maysarah anayankha kuti, &#8220;Mawu anu ndi abwino kwambiri komanso ndi owala! Ndikanakonda nditakutsatirani ndikukuthandizani, koma abale anga anditsutsa, ndipo munthu nthawi zonse amafunikira abale ake. Ngati abale a munthu sali okonzeka kumuthandiza, ndiye kuti n&#8217;zokaikitsa kuti angapeze thandizo kuchokera kwa ena.&#8221;<\/p>\n<p>Atalandira yankho limeneli, Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) anatembenuka ndi kupita, ndipo abale ake omwe ndi Banu Abas naonso anachoka kubwerera ku mabanja awo.<\/p>\n<p>Paulendo obwerera, Maysarah anauza abale ake a m&#8217;banja lake kuti, &#8220;Tiyeni tidutse ku Fadak, popeza Ayuda amakhala kumeneko ndipo tidzatha kuwafunsa ngati ali ndi amene wanenapo za uneneri umenewu.&#8221;<\/p>\n<p>Iwo anavomera kutero, kotero anafika ku Fadak.<\/p>\n<p>Atafika ku Fadak ndikufunsa mafunso awo kwa Ayuda, Ayuda anatenga gawo la malemba awo opatulika, Tauraah, kenako anayamba kuwerenga kufotokozera kwa Nabi omaliza zomwe kunalembedwa m&#8217;malemba awo. Mafotokozedwe omwe adawerenga anali awa:<\/p>\n<p>Nabi omaliza adzakhala osaphunzira ndipo adzachokera kudziko la Arabiya. Adzakwera ngamira ngati chokwera chake ndipo mkate ochepa udzamukwanira. Tsitsi lake silidzakhala lopota kapena lowongoka. Sadzakhala wamtali kwambiri kapena oyera kwambiri. Maso ake adzakhala ndi mtundu ofiira.<\/p>\n<p>Kenako Ayuda anati, &#8220;Ngati munthu amene anakuitanani ku dini yake akugwirizana ndi izi, landirani uthenga wake ndikukumbatira dini yake.<\/p>\n<p>&#8220;Kunena za ife, sitidzamutsata chifukwa mitima yathu yadzaza ndi nsanje pa iye. Tikudziwa kuti tidzamenyana naye nkhondo m&#8217;malo osiyanasiyana. Kuchokera pankhondo yolimbana naye, Aarabu, munthu aliyense adzamutsata kapena onetsetsani kuti muli m&#8217;gulu la omwe akumutsata.&#8221;<\/p>\n<p>Maysarah atamva izi, adalankhula ndi abale ake nati, &#8221; Anthu inu! Nkhani iyi yoti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) ndi Mneneri weniweni wa Allah tsopano yamveka bwino!\u201d Koma iwo adazengereza nati: \u201cTikabwerera ku Haji chaka chamawa tidzakumana naye ndi kulowa chisilamu.<\/p>\n<p>Kotero anabwerera kwawo, ndipo anthu ena a m\u2019banja lake sanavomereze zimene ananena ndipo sanafune kuchita zimene anawauza. Momwemo, zaka zidadutsa mpaka Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adapanga hijrah ku Madina Munawwarah. Pomaliza, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) atabwerera ku Makka Mukarramah Atachita Haji yotsanzika, Maisarah adakumana naye ndipo adamuzindikira.<\/p>\n<p>Maysarah adabwera kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) nati: \u201cE, Mtumiki wa Allah!, kuyambira nthawi imene munaimika ngamira yanu pa ife ndikutiyankhula ndinkalakalaka kubwera kwa inu kuti ndidzalowe chisilamu ndikukutsatirani, komano china chake chimandilepheretsa nthawi ndikumapita, ndimmene mukuonera, kulowa kwanga kwa Chisilamu kwachedwedwa mpaka pano.<\/p>\n<p>\u201cNdithu abale anga ena omwe mudawayankhula ku Mina, onse adamwalira. Oh Mtumiki wa Allah! Ndiuzeni ali kuti ku Jannah kapena ku Jahannum?\u201d<\/p>\n<p>Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adayankha: &#8220;Aliyense amene amamwalira pa deen ina osati Chisilamu adzajakhala ku Jahannum.&#8221; Atamva izi Maysarah adati: &#8220;Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah amene wandipulumutsa ku Jahannum!&#8221;<\/p>\n<p>Pambuyo pake adalowa Chisilamu ndipo adakhala Msilamu owopa Allah, owona mtima, mpaka kulemekezedwa kwambiri ndi Abu Bakr radhwiyallahu anhu mu nthawi ya Khilaafah yake.<\/p>\n","protected":false},"excerpt":{"rendered":"<p>Mu Quraan Majid, Tsiku la Qiyaamah latchulidwa ndi mayina osiyanasiyana. Mayina ena mwa awa ndi &#8220;Tsiku la Mphotho ndi Kubwezera&#8221;, &#8220;Tsiku losonkhana&#8221;, &#8220;Tsiku la Kutayika ndi Kupindula&#8221; (lodzataika kwa osakhulupirira ndi la phindu kwa okhulupirira), ndi &#8220;Tsiku la Kukumana&#8221; (kutanthauza kukumana ndi Allah Talaa. Tikayang&#8217;ana mayina awa, timapeza kuti dzina lililonse likumaonetsa momwe zinthu zidzakhalire &hellip;<\/p>\n","protected":false},"author":3,"featured_media":2655,"comment_status":"closed","ping_status":"open","sticky":false,"template":"","format":"standard","meta":{"footnotes":""},"categories":[24],"tags":[],"class_list":["post-4161","post","type-post","status-publish","format-standard","has-post-thumbnail","","category-minda-ya-chikondi"],"_links":{"self":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4161","targetHints":{"allow":["GET"]}}],"collection":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts"}],"about":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/types\/post"}],"author":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/users\/3"}],"replies":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcomments&post=4161"}],"version-history":[{"count":4,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4161\/revisions"}],"predecessor-version":[{"id":4187,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/posts\/4161\/revisions\/4187"}],"wp:featuredmedia":[{"embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=\/wp\/v2\/media\/2655"}],"wp:attachment":[{"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fmedia&parent=4161"}],"wp:term":[{"taxonomy":"category","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Fcategories&post=4161"},{"taxonomy":"post_tag","embeddable":true,"href":"https:\/\/ny.alislaam.com\/index.php?rest_route=%2Fwp%2Fv2%2Ftags&post=4161"}],"curies":[{"name":"wp","href":"https:\/\/api.w.org\/{rel}","templated":true}]}}